Chimene Achichepere Afunikira Lerolino
Mtsikana wazaka 14 wa ku New Jersey, U.S.A., ananena kuti kuchiyambi kwa chaka chino anafunikira kulemba lipoti lamutu wakuti “Chimene Ophunzira Amachitira Monyenga pa Mayeso.” Anapita kusukulu ndi buku lake lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza kuti akafufuze. Mmodzi wa anzake a kusukulu analitenga nayamba kuŵerenga mitu ya zigawo pa zamkatimu, yonga “Kugonana ndi Makhalidwe” ndi “Kupalana Chibwenzi, Chikondi, ndi a Ziŵalo Zosiyana.”
“Kodi ndingatenge bukuli?” mnzakeyo anafunsa motero.
“Ndinamuuza kuti bukulo linali langa,” wophunzirayo anatero, “koma kuti ndidzambweretsera lina. Nditatero, mnzanga wina anaona bukulo nandipempha kumbweretseranso lake. Posapita nthaŵi, ndinabweretsa mabuku khumi a Achichepere Akufunsa kwa ophunzira omwe anali kuwafuna.”
Wophunzira wazaka 14 ameneyo akuganiza kuti bukulo nlabwino kukhala nalo. Anati: “Tifunikiradi chofalitsa chimenechi chifukwa unyamata masiku ano ngwovuta kwambiri.”
Ngati mukufuna kukhala ndi kope la buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza kapena kuti wina adzafike kwanu kudzakambitsirana nanu za phindu la maphunziro a Baibulo, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku keyala yapafupi ndi kwanu pa ndandanda ya patsamba 5.