Kodi Mudziŵa?
(Mayankho a mafunsoŵa mungawapeze m’malemba a m’Baibulo osonyezedwawo, ndipo mpambo wa mayankho ake onse uli patsamba 24. Kuti mudziŵe zowonjezereka, fufuzani buku la “Insight on the Scriptures,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.)
1. Kodi nchiyani chinaletsa Yesu kuchita zamphamvu pakati pa anthu a m’gawo lakwawo? (Marko 6:5, 6)
2. Kodi ndi mbewu ziŵiri ziti zimene Yesu anatchula ponena za lamulo la Afarisi la kupereka chakhumi kopanda chifundo? (Luka 11:42)
3. Kodi ndi nyama yotani imene inatchulidwa mwaulosi kusonyeza mmene Yesu adzakhalira “du” pozunzidwa? (Yesaya 53:7)
4. Kodi ndi mkulu wa ansembe uti amene analandira chilango choopsa chifukwa cholemekeza ana ake kuposa Yehova? (1 Samueli 2:27-29)
5. Kodi Yesu ‘anadzudzula’ chiyani chimene chinamleka mpongozi wa Simoni kotero kuti anachira? (Luka 4:38, 39)
6. Kodi kusakhalitsa kwa moyo wa munthu kwayerekezeredwa ndi chiyani, kusiyana ndi ‘mawu a Mulungu okhala chikhalire’? (1 Petro 1:24, 25)
7. Kodi ndi m’chipululu chiti mmene Aisrayeli anadya mana nthaŵi yoyamba mmenenso lamulo la Sabata linakhazikitsidwa? (Eksodo 16:1, 13-31)
8. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene mafano sangathe kuchita? (Salmo 115:5-7)
9. Kodi ndani anamanidwa mwaŵi wa kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa chifukwa analephera kuyeretsa Mulungu ndi kumlemekeza ku madzi a Meriba? (Numeri 20:12)
10. Kodi ndi chiŵalo chiti cha thupi chimene chimagwiritsiridwa ntchito kuphiphiritsira kusonyeza nyonga kapena mphamvu? (Yesaya 51:9)
11. Posonyeza ukulu wa unsembe wa Kristu, kodi Paulo anati Levi anaperekanji adakali m’mimba mwa Abrahamu? (Ahebri 7:9, 10)
12. Kodi ndi mawu ati ogwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kusonyeza kuti mfumu ya Israyeli inaimira ulamuliro wa Yehova wateokrase? (1 Mbiri 29:23)
13. Kodi chimodzi ndi chimodzi cha zamoyo zinayi m’masomphenya a Yohane chinafanana ndi chiyani? (Chivumbulutso 4:7)
14. Kodi chinali kudzachitika padziko lapansi nchiyani Mdyerekezi atagwetsedwa kumwamba? (Chivumbulutso 12:12)
15. Kodi anagwiritsira ntchito njira yotani kugaŵa Dziko Lolonjezedwa pakati pa mafuko 12? (Numeri 26:55, 56)
16. Kodi ndi mbalame iti imene maso ake onse aŵiri amapenya kutsogolo, kuikhozetsa kuona chinthu ndi maso onse aŵiri panthaŵi imodzi? (Salmo 102:6)
17. Kodi Timoteo anasonyezanji kwa ena mwa kupitiriza kuchita khama pa zinthu zauzimu? (1 Timoteo 4:15)
18. Kodi Danieli anali ndi malo anji m’boma la Babulo? (Danieli 2:48)
19. Kodi Adamu ndi Hava anasoka chiyani kupanga zovala? (Genesis 3:7)
20. Pogogomezera mfundo yake yonena za kusagwiritsira ntchito lilime molakwa, kodi Yakobo anati mkuyu sungabale chiyani? (Yakobo 3:12)
21. Anthu odwala anangofunikira kukhudza mbali iti ya chovala cha Yesu kuti achire kotheratu? (Mateyu 14:36)
22. Kodi zakumwamba zinakhala zizindikiro za chiyani? (Genesis 1:14)
23. Kodi ndani makamaka omwe ayenera kudziŵika ndi moyo wodzisunga, makhalidwe oyenera ndiponso ntchito zabwino? (Tito 2:2, 3)
24. Kodi Yesaya anati anthu adzakhululukidwa chiyani, kotero kuti “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala”? (Yesaya 33:24)
25. Ngakhale kuti lemba lomwe anagwira mawu, Salmo 140:3, linatcha njoka yaululuyo “mphiri,” kodi Paulo anatchula dzina lotani? (Aroma 3:13)
26. Kodi chilembo chachisanu ndi chimodzi cha alifabeti ya Chihebri nchiyani?
27. Kodi ndi liwu liti logwiritsiridwa ntchito kutchula munthu wosakhala Myuda? (Aroma 2:9, 10; onani King James Version.)
28. Kodi dzina la doko la ku Italiya kumene Paulo anathako mlungu umodzi ndi Akristu anzake paulendo wake wokaonekera pamaso pa Kaisara linali chiyani? (Machitidwe 28:13, 14)
29. Kodi Paulo akutilangiza kusumika maso pa zinthu zotani zamuyaya? (2 Akorinto 4:18)
30. Kodi Akristu ayenera kusachitanji iwo okha, chifukwa Yehova adzachita chimenecho? (Aroma 12:19)
31. Pogogomezera chiwonongeko cha Gehena, kodi Yesu anati nchiyani chimene sichimafa kumeneko? (Marko 9:48)
Mayankho patsamba 24
Mayankho a Mafunsowo
1. Kupanda kwawo chikhulupiriro
2. Timbewu tonunkhira, timbewu tokometsera
3. Nkhosa
4. Eli
5. Malungo ake
6. Udzu umene ufota
7. Chipululu cha Sini
8. Kulankhula, kupenya, kumva, kununkhiza, kugwira, kuyenda
9. Mose ndi Aroni
10. Mkono
11. Limodzi limodzi la magawo khumi
12. “Akhala pa mpando wachifumu wa Yehova”
13. Mkango, ng’ombe, munthu, chiwombankhanga
14. Tsoka
15. Mwa kuchita maere
16. Kadzidzi
17. Kukula mtima kwake
18. Kazembe wamkulu
19. Masamba amkuyu
20. Azitona
21. Mphonje
22. Nyengo, masiku, zaka
23. Amuna ndi akazi okalamba
24. Mphulupulu zawo
25. Mamba
26. Waw
27. Wakunja
28. Potiyolo
29. “Zinthu zosaoneka”
30. Kufuna kubwezera
31. “Mphutsi yawo”