Chithandizo pa Maphunziro a Kakhalidwe
Mphunzitsi wina ku Zimbabwe, anaona kuti pa Koleji ya Nyatsime, pamene amaphunzitsa, pali “Maphunziro a Kakhalidwe.” Iye anafotokoza mavuto amene anali nawo m’banja navomereza kuti anafuna thandizo kuti awathetse.
Pofotokoza zimene zinachitika pambuyo pa ukwati wake, anati: “Mavuto anangoyamba tisanakhalitse mpaka tinaganiza zopatukana mu November 1989.” Panalinso mavuto ena. Analemba kuti: “Ndine mwana wamkulu pa onse mwa amayi, omwe anali akazi aakulu a atate. Pamene ndinali m’chaka chachiŵiri chophunzira uphunzitsi, atate anamwalira, kundisiya ndikusamalira abale ndi alongo anga 16.”
Kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kunathandiza mphunzitsi ameneyu kuthetsa mavuto ake. Anabwererana ndi mkazi wake ndipo ali achimwemwe. Iye analemba kuti: “Ineyo ndi mkazi wanga tadziŵa mwa zovuta zimene tinakumana nazo kuti kulimbikira kwa munthu pofuna kuthetsa mavuto ake popanda Mulungu nkwachabe.” Nanga bwanji zothandiza ophunzira ake pamavuto awo?
Iye analemba kuti: “Ndinauza ahedimasitala ndi aphunzitsi ena kuti buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza nlabwino kuphunziramo. Onse anavomereza, ndipo kusukulu anandipatsa oda ya mabuku 56, amene ndapereka kale kusukulu.”
Tikhulupirira kuti inunso mudzapindula kwambiri ndi buku limeneli la zithunzithunzi zokongola la masamba 320 lothandiza pamaphunziro. Ngati mukufuna kulandira kope lake kapena ngati mukufuna kukhala ndi phunziro la Baibulo la panyumba laulere, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 33459, Lusaka 10101, kapena kukeyala yoyenera patsamba 5.