Zakudya—Nkhani Yaikulu
“TIYE, idya zakudya zako mokondwa,” limatero Baibulo pa Mlaliki 9:7. Ndithudi, kudya sikofunika chabe komanso ndiko chimodzi cha zinthu zosangalatsa kwambiri m’moyo.
Talingalirani za Thomas wazaka 34. Iye amakonda kudya nyama. Ndipo amaidya masiku onse—nthaŵi zambiri kangapo patsiku. Mfisulo wake nthaŵi zambiri umakhala wa mkaka, mazira angapo, buledi kapena buledi wowotcha wopaka bata, ndi soseji kapena nyama yoŵamba yankhumba. Pogulitsira zakudya zosavuta kukonza, amagula mabanzi okhala ndi nyama ndi tchizi pakati, mbatata zokazinga m’mafuta ambiri, ndi ma milk shake. Kumalesitiranti, amasankha nyama yang’ombe monga chakudya chachikulu. Lesitiranti imene amakonda kwambiri imagulitsa nyama yamagalamu 680 ndi mbatata zowotcha zokhala ndi sour cream pamwamba, ndee mmene amazikondera. Keke ya chokoleti yokhala ndi ayezikilimu ya chokoleti pamwamba pake ndicho chakudya chimene amakonda kwambiri atadya zakudya zonse.
Thomas ndi wamtali mamita 1.78 ndipo amalemera makilogalamu 89; akupyola malire ndi makilogalamu 9, malinga ndi zitsogozo zazakudya za boma la United States za mu 1995. “Sindida nkhaŵa ndi thupi langa,” akutero Thomas. “Ndili ndi thanzi labwino kwambiri. Sindinakhalepo tsiku limodzi kuntchito pazaka 12 zapitazi. Nthaŵi zambiri, ndimamva bwino ndi wamphamvu—komatu kusiyapo nditadya nyama yamagalamu 680.”
Komano, kodi zakudya za Thomas zikumuwononga, pang’onopang’ono kumchititsa kuti adzadwale matenda a mtima? M’buku lake lakuti How We Die, Dr. Sherwin Nuland akunena za ‘makhalidwe amene amaphetsa’ ndipo pakati pawo akuphatikizapo zakudya za ‘nyama [kusiyapo ya nkhuku ndi ya nsomba], nthuli zikuluzikulu za nyama yootcha yankhumba, ndi bata.’
Kodi zakudya zina zimachititsa motani matenda a mtima mwa anthu ena? Kodi zili ndi chiyani chimene chili changozi? Tisanakambitsirane mafunsowa, tiyeni tipende mosamalitsa ngozi za kukhala wonenepa kwambiri.
[Chithunzi patsamba 21]
Kodi nchifukwa ninji zakudyazi zakhala nkhani yaikulu?