Kodi Galu Wanu Sangavulaze Ana?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU SOUTH AFRICA
SYDNEY wazaka ziŵiri anayenda pafupi kwambiri ndi galu waukali wamtundu wa Rottweiler yemwe anali womangirira. Galuyo anamuukira Sydney, nkumvulaza kumutu, ndipo pafupifupi kukhadzula khutu lake lakumanzere. Adzafunikira kumamsokerera minofu kwa zaka zingapo.
Chifukwa anthu ambiri akugwiritsira ntchito agalu monga chitetezo, kukumveka malipoti ochuluka oti agalu akuukira ana. Agalu ena amene amadziŵika kuti amaluma ana ndiwo amtundu wa Rottweiler, Doberman pinscher, bullmastiff, Alsatian, ndi bullterrier. Ku South Africa ofufuza ena poipenda nkhaniyi, apeza kuti unyinji wa ana amenewo amalumidwa ndi agalu owadziŵa. Pafupifupi theka la iwo analumidwa ndi agalu a anansi awo, ndipo mwana mmodzi mwa anayi alionse analumidwa ndi agalu a pakhomo pawo pompo. Pa onsewo, okwanira 10 peresenti basi analumidwa ndi agalu ongodziyendera. Kaŵirikaŵiri wolumidwayo, kapena popanda kuzindikira, amakhala atamputa galuyo mwa njira ina. Mwachionekere, eni agalu limodzi ndi makolo angaletse agalu awo kuukira anthu ngati angakhale osamala kwambiri.
Mphunzitseni Mwanayo
Ambiri amene amaphunzitsa agalu amanenetsa kuti ana aang’ono ndi agalu asamasiyidwe okha popanda wachikulire wowayang’anira. Ana aang’ono samadziŵa mokhalira ndi nyama. Muyenera kuwaphunzitsa. Choncho, anthu ambiri ali ndi lamulo lakuti ngati palibe wachikulire wowayang’anira, agalu ndi ana aang’ono asasiyidwe m’malo amodzi. M’buku lakuti Childproofing Your Dog, wophunzitsa agalu Brian Kilcommons akulongosola kuti: “Pazochitika zimene timamvazi, mavuto ambiri amakhala pamene achikulire sakuona.”
Kaŵirikaŵiri, nyama zimafunikira kutetezeredwa kwa ana! Tsiku lina Kilcommons anamuitana kudzathandiza pamene galu wa banja lina anafuna kuluma mwana. Bambo wopsa mtimayo anafotokoza kuti mwana wake wazaka ziŵiri ndi theka anathamangira galu anali goneyo namponda kwambiri. Galuyo, atamvadi ululu, anafuna kumluma mwana uja. Apa galuyo anasonyeza kudziletsa koyamikirika posamluma mwanayo. Wophunzitsa agaluyo akulangiza makolo kuti: “Musamlole mwana wanu kuchitira galu chimene simukanamlola kuchitira mwana wina.”
Mphunzitseni mwana wanu kusamala bwino nyama. Mphunzitseni kuti asamaputa galu. Makolo afunikira kukhala maso kuona ngozi iliyonse imene ingachitike pamene ana ndi agalu ali pamodzi. Ngati mwaona kuti galu akuyesa kumthaŵa mwana kapena kubisala, mletseni mwanayo asamlondole iyayi. Ngati mwanayo amtsatirabe mpaka nkumtsekereza galu uja, kudzichinjiriza kwake ndiko kuuwa, kuzazira, ngakhale kuluma kumene. Makolo ayenera kulanga nthaŵi zonse, kuti onsewo galu ndi mwana azidziŵa kuti khololo likutanthauzadi zimene likunena.
Musachite naye galuyo ngati si wanu. Mwamuna ndi mkazi wake omwe ali ndi galu atabala khanda lawo loyamba, angayambe kumnyalanyaza galu uja ndi kumamuingitsira kukhonde. Pamene kuli kwakuti nkoyeneradi kusamala, wophunzitsa agalu Richard Stubbs akulangiza kuti: “Musachite naye galuyo ngati si wanu. M’malo mwake, chitani naye galuyo monga mwa masiku onse ndithu, ndipo msamaleni bwino.”
Lingalirani mmene mwana wanu adzachitira ndi agalu achilendo. Akaona munthu wosamdziŵa akuyenda ndi galu pamsewu, kodi ayenera kutani? Kodi ayenera nthaŵi yomweyo kuthamanga kukamsisita galu uja? Mphunzitseni kuti asamatero iyayi. Aziyamba wapempha chilolezo cha mwini galuyo. Ndiyeno mwini galuyo akavomera, mwanayo angamyandikire galu uja pang’onopang’ono, kuti asamdzidzimutse. Adzidziŵikitse mwa kuimirira chapatali pang’ono nkumalankhula modekha ndi galuyo. Galu waubwenzi adzamyandikira mwana wanu. Agalu amene akudziyendera okha pamsewu ndi bwino kusawayandikira.—Onani bokosi lakuti “Galu Amalankhula ndi Thupi,” tsamba 14.
Mphunzitseni Galuyo
Nthaŵi zonse mtamandeni galu wanu ndipo tsimikizani kutero. Kumlanga kapena mawu aukali sizimafulumiza kuphunzira koma m’malo mwake zimakuchedwetsa. Nkwabwino kuti galu aphunzire kubwera pamene mwamuitana ndiponso kumvera malamulo onga “khala!” Galuyo amaphunzira kugonjera mbuyake, ndipo zimenezo zingamtheketse mwini galuyo kumlamulira pamikhalidwe yovuta. Mawu osavuta amachita bwino kwambiri. Gwiritsirani ntchito amodzimodziwo. Pamene galu wanu wachita zimene mukufuna, mpatseni mphoto nthaŵi yomweyo monga kumtamanda, kumsisita, kapena mponyereni fupa. Kuti galuyo adziŵe chifukwa chimene mukumtamandira, mpatseni mphotoyo nthaŵi yomweyo atangochita chinthucho. Chinthu china chofunika ndicho kubwerezabwereza mpaka atazoloŵera ndithu.
Ngati mwagula galu, kaya nkhanda kapena wamkulu amene, afunikira kumthandiza kuzoloŵerana ndi ana. Ana amasiyana ndi akulu. Ngaphokoso kwambiri ndipo amachita zinthu mosaganizira ndipo angangomthamangira galu uja, zimene mwina zingamuwopseze. Zingakhale bwino kuchizoloŵeretsa chifuyo chanu khalidwe losakhazikika longa limenelo. Ngati anawo achokapo, mzoloŵeretseni galuyo mapokoso adzidzidzi. Chitani kuphunzitsako kungokhala maseŵera. Mlamuleni mofuula galuyo, ndiye mthamangireni. Kenako, nthaŵi yomweyo mfupeni galu wanu. Onjezani mphamvu ya kufuula kwanu pang’onopang’ono. Mtamandeni ndi kumsisita galu wanu. Posakhalitsa adzayamba kuwakonda maseŵerawo.
Ana aang’ono amakonda kukupatira agalu, koma muyenera kuwaphunzitsa kuti asamatero, chifukwa agalu ena amachita mantha mukawakupatira. Ngati ana anu amkupatira galu wanu, mphunzitseni kumalola zimenezo. Mkupatireni galu wanu kwa kanthaŵi, ndiyeno mpatseni fupa ndi kumtamanda. Mwapang’onopang’ono zimkupatirani kwa nthaŵi yotalikirapo. Ngati galu wanuyo azaza kapena kuchita ukali, itanani wophunzitsa agalu waluso adzathandize.
Galu Waukali
Agalu ena amaoneka aukali mwachibadwa ndipo angakhale angozi kwa anthu apabanjapo. Agalu amphongo ndiwo amasonyeza ukali woterowo.
Galu wovutitsa samakonda kumgwira, makamaka malo onga kumaso ndi khosi. Komabe, nthaŵi zina galuyo angabwere kwa inu, kukugundani, kapena kuika mapazi ake pamiyendo yanu, kuli “kupempha” chisamaliro. Galuyo angamalonde malo ena panyumbapo amene amaona ngati ndi akeake, osalola ngakhale apabanjapo kudzerapo. Kaŵirikaŵiri samafuna kuti wina agwire zinthu zonga zidole ndipo amazaza kapena kuleka kutafuna pamene wina akuyandikira galuyo adakaseŵera nazo.
Kuti akusonyezenidi kuti ndiwo akutsogolera, agalu oterowo amanyalanyaza dala malamulo anu akudziŵa. Amawakankha ana pofuna kuti iwowo akhale oyamba kuloŵa pakhomo. Ndiponso amakonda kulumphira anthu. Brian Kilcommons akuti, kameneko ndiko “kachitidwe kolamulira” ndipo “osati kukwera iyayi.” Akuchenjeza kuti chimenechi “nthaŵi zonse nchizindikiro choti galuyo akuganiza kuti ndi iye amene akulamulira. Poteropo muchenjere nayedi angakuvutitseni.” Galuyo amadzazoloŵeranso kuluma dzanja la mbuye wake kuti amsamale.
Zizindikiro zimenezi za ukali musazinyalanyaze iyayi. Ukaliwo sudzangotha wokha; mwina ungangowonjezeka, ndipo ana panyumbapo angakhale pangozi. Anthu ambiri ophunzitsa agalu amalangiza kuti galu woteroyo azingomfula, mosasamala kanthu kuti kaya ngwamphongo kapena ngwamkazi, chifukwa kutero nthaŵi zonse kumathandiza kuchepetsa ukali.
Si bwino kumtokosa galu waukali kuti musonyeze kuti mbuye ndi yani. Kulimbana naye ndi kumlanga mwaukali kungakhale kwa ngozi. Mwa njira zina zochenjera, mungamsonyeze galuyo kuti ndani akulamulira.
Nthaŵi zonse galu waukali akakupezani ndi kufuna kuti mumsamale ndipo inu nkumsamaladi, mumampangitsa kukhulupirira kuti akulamulira ndi iye. Choncho ngati galu woteroyo akufuna chisamaliro, musamsamale iyayi. Banja lonse lizichita naye mofananamo. Poyamba galuyo angadabwe ndipo ngakhale kuuwa ndi kukuyang’anani mokopa, koma musamsamalebe iyayi. Pamene wachoka kapena wakagona pamalo ake, imeneyo ndiyo nthaŵi tsopano yoti mumsamale pang’ono. Mwa njira imeneyi galu wanu amaphunzira kuti wotsogolera ndi inuyo ndipo ndi inunso amene mumasankha nthaŵi yomsamala.
Maseŵero olimbana onga makani okokana ndi kugwetsana zingamlimbikitse galuyo kufuna kumalamulira ndipo muyenera kuwapeŵa. M’malo mwake, chitani maseŵera opanda zolimbana.
Zingakhale bwino kuti galu asamagone m’chipinda chanu chogona. Chipinda chogona makolo ndicho malo olemekezeka, ndipo kugona mmenemo kungampangitse galuyo kudziona ngati wowaposa ana apanyumbapo. M’malo mwake, ikani chogonapo galuyo m’khichini kapena m’nkhwimba yake yapanja. Kaŵirikaŵiri galu waukali amayamba kuwaluma ambuyake m’zipinda zawo zogona zomwezo.
Ngati galu wanu sakuphunzirapo kanthu pa zimene mukuyesayesa kumphunzitsa, kapena ngati amakuwopsezani pomphunzitsa kumene, kapena panthaŵi ina iliyonse, itanani wophunzitsa agalu wodziŵa bwino kuti akuthandizeni. Wavetelinale wanu angakuthandizeni kumpeza. Choyamba lankhulani naye wophunzitsa agaluyo za njira zake zophunzitsira, ndipo tsimikizani kuti mwakondwa nawo maluso ake musanamlembe ntchito. Wophunzitsa agalu Richard Stubbs akuchenjeza kuti: “Pamene kuli kwakuti galu waukali angamvere katswiri wophunzitsa agalu, zimenezo sizitanthauza kuti angachite zofanana kwa mbuye wake.” Mwini galuyo ayenera kutsimikiza kuti adzakhoza kumlamulira galu wake atayamba kuvuta.
Agalu oŵerengeka amakhalabe aukali ngakhale pambuyo powaphunzitsa bwino kwambiri, ndipo kuwasungabe kumaika banjalo pachiswe. Mutayesayesa zonse zimene mungathe, mwina mungaone kuti ndi bwino kungomgulitsa galuyo kuti mupeŵe kudzavulala. Nkwanzerunso kuonana ndi wavetelinale kapena wophunzitsa agalu kuti akupatseni uphungu. Mungathe kumpezera galu wanuyo nyumba ina, koma mudzayenera kumuuza mbuye watsopanoyo mmene galuyo anali kukuvutitsirani.
Wophunzitsa agalu Peter Neville akulangiza kuti: “Pochita ndi agalu aukali pali malangizo atsatanetsatane omwe mufunika kuwatsatira bwinobwino ndiponso mufunika kusamala poona kuti ndani amene adzakhalabe pangozi ndi kuganiziranso ukulu wa ngoziyo. Ngati nkosatheka kumtetezera munthu wina m’banjamo amene ali pangozi kwambiri, ndiye galuyo ndi bwino kungomgulitsa kwa mbuye watsopano yemwe mwasankha mosamala, kapena kungomupha.”
Ana angaphunzire ndipo zingawathandize kukhala ndi mtima wabwino ngati panyumba pali galu. Mwa kuyang’anira zinthu mosamala, makolo angathandize kuchititsa kuti zonse zimene ana awo angamakumbukire ponena za zifuyo zawo nzabwino zokhazokha.
[Bokosi patsamba 14]
Galu Amalankhula ndi Thupi
Zochita za galu waukali zimasonyeza kupanda kwake ubwenzi. Mwa kumphunzitsa mwana wanu kuzindikira kulankhula kwa galu ndi thupi, mungamthandize kupeŵa ngozi.
● Galu waukali amayesa kuoneka ngati wamkulu. Ubweya wa pakhosi lake umanyamuka. Galuyo amazaza kapena kuuwa mchira wake uli jo m’mwamba. Ngati mchirawo akuugwedeza mwamphamvu ndi mwachangu, sikuti akusonyeza ubwenzi iyayi. Galu ameneyo ingomsiyani.
● Galu wamantha amaŵeramitsa mutu ndi makutu, mchirawu ataupindira pakati pa miyendo yake. Mukamuyandikira galu ameneyo, amafufuma chifukwa cha mantha. Ameneyonso ingomsiyani.
● Galu wofatsa amaima chiriri mutu osautukula kwambiri kapena kuutsitsa kwambiri, atayasama, ndipo mchira ukugwedera cha mmunsimunsi, koma wosangoti pansi zolii. Kugwedeza kwake mchira nchizindikiro cha ubwenzi. Palibe upandu kuchita naye ubwenzi galu ameneyo.
(Zochokera m’buku lakuti Childproofing Your Dog, lolemba Brian Kilcommons ndi Sarah Wilson.)
[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]
Chitetezo Ngati Panyumba Pali Galu
1. Yang’anirani ana aang’ono ndi agalu omwe.
2. Phunzitsani mwana wanu kuti asamaputa galu.
3. Pemphani chilolezo cha mwini galu musanamsisite.
4. Phunzitsani galu wanu kumvera malamulo osavuta.
5. Mzoloŵeretseni kumkupatira galu wanu.
6. Peŵani maseŵero olimbana.