Kodi Zipembedzo Zonse Zimatsogolera kwa Mulungu?
Mamiliyoni ambiri a anthu amakhulupirira kuti zipembedzo zonse ndi misewu yosiyanasiyana yopita kumalo amodzi. Nkhani ndi yakuti, ziphunzitso, miyambo, ndi milungu ya zipembedzo ndi yofanana. Mwachitsanzo, taonani fano la m’zaka zazana lachisanu ndi chitatu C.E. la m’nthanthi zachihindu, la ku Kerala, India.
Chodabwitsa nchakuti ng’ombe zinkalambiridwa m’zipembedzo zambiri zakale. Mwachitsanzo, malinga ndi Diodorus Siculus, wolemba mbiri yakale wachigiriki wa m’zaka zazana loyamba B.C.E., Moleke mulungu wa a Amoni nayenso anali ngati munthu koma anali ndi mutu wang’ombe.
Nchifukwa ninji pakhala kufanana kwambiri motere m’zipembedzo zosiyanasiyana kuzungulira dziko lonse lapansi? Kodi zipembedzo zonsezi zinayambira malo amodzi? Kodi zangokhaladi chabe misewu yosiyanasiyana yopita kumalo amodzi? Kodi Mulungu amazivomereza zonsezo?
Nkhani yosangalatsa ya chiyambi ndi kukula kwa zipembedzo zikuluzikulu za m’dziko lapansi m’buku lakuti Mankind’s Search for God imayankha mafunso amenewo. Ngati mukufuna kulandira buku limeneli kapena kuti wina adzakuchezereni panyumba panu kuti mudzakambitsirane zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena ku keyala yoyenera patsamba 5.