Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 1/8 tsamba 26-27
  • Kodi Mungamuope Bwanji Mulungu Wachikondi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungamuope Bwanji Mulungu Wachikondi?
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumwamba ndi Ukulu wa Yehova
  • Mulungu Wokhululukira
  • Kuopa Chiweruzo cha Mulungu
  • Khalani ndi Mtima Woopa Yehova
    Nsanja ya Olonda—2001
  • Nchifukwa Ninji Tiyenera Kuwopa Mulungu?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kuwopa Mulungu Kodi Kungakupindulitseni?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi N’kuphunziriranji Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 1/8 tsamba 26-27

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mungamuope Bwanji Mulungu Wachikondi?

“WODALA MUNTHU WAKUOPA YEHOVA.”—Salmo 112:1.

NGATI “Mulungu ndiye chikondi” monga momwe Baibulo limanenera, kodi nchifukwa ninji kumuopa kuli koyenerera? (1 Yohane 4:16) Kaŵirikaŵiri chikondi ndi kuopa sizigwirizana. Motero, kodi kuopa kuyenera kukhala ndi mbali yotani mu unansi wathu ndi Mulungu? Nchifukwa ninji kuopa Mulungu wachikondi? Tingamvetsetse bwino nkhaniyi ngati tiona mmene Baibulo limagwiritsira ntchito mawuwo “kuopa.”

M’zinenero zambiri liwu lingakhale ndi matanthauzo osiyanasiyana mogwirizana ndi nkhani yakeyo. Mwachitsanzo, m’zinenero zina munthu anganene kuti: “Ndimakonda nsomba yowotcha,” ndiponso kuti, “Ndimakonda ana anga.” Pali kusiyana kwakukulu pa kukula ndi mtundu wa chikondi chosonyezedwacho. Mofananamo, Baibulo limanena za mitundu yosiyanasiyana ya kuopa. Pamene ligwirizanitsa mawuwo ndi kulambira Mulungu, silisonya ku kuopsa, mantha, kapena kuopa chilango chomayandikira. M’malo mwake, kuopa Mulungu kumapereka malingaliro abwino—mantha aulemu, ulemu ndi kulemekeza kwakukulu. Malingaliro abwino amenewa amaphatikizapo chikondi pa Mulungu ndi kukopeka naye, osati kumuthaŵa kapena kubisala.

Kuopa Mulungu kumachotsa mantha osayenera. Wamasalmo analemba ponena za munthu amene amaopa Mulungu kuti: “Sadzaopa mbiri yoipa; mtima wake ngwokhazikika, wokhulupirira Yehova.” (Salmo 112:7) Palibe chiopsezo chilichonse chochokera kwa anthu kapena kwa Satana iye mwini chimene chingatilande ulemu wathu wakuya kwa Yehova. (Luka 12:4, 5) Sitiyeneranso kuopa kumfikira Mulungu m’pemphero. M’malo mwake, m’nkhaniyi, “chikondi . . . chitaya kunja mantha.”—1 Yohane 4:18.

Kumwamba ndi Ukulu wa Yehova

Mfumu Davide wakale anali munthu woopa Mulungu. Anali ndi mantha aulemu pamene anali kusinkhasinkha za kukongola ndi kucholowana kwa chilengedwe. Anafuula kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.” (Salmo 139:14) Akuyang’ana kumwamba usiku anafuula kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu.” (Salmo 19:1) Kodi muganiza kuti Davide anaopsedwa ndi zimenezi? Mosiyana, zinamsonkhezera kuimbira Yehova nyimbo zomtamanda.

Chidziŵitso chamakono chochuluka cha kuthambo chimatipatsa ife chifukwa champhamvu chokhalira ndi mantha aulemu. Posachedwapa, akatswiri a zakuthambo pakugwiritsira ntchito telesikopo yotchedwa Hubble Space anafufuza kuthambo mozama kusiyana ndi wina aliyense m’mbuyomu. Anasankha malo kumwamba amene, ndi matelesikopo a pansi pano, anaoneka kuti analibe kanthu ndi kusumika Hubble pamalo amene anali aukulu ngati kamchenga kokaonera patali pang’ono. Chithunzi chomwe chinatulukapo chinali chodzaza, osati ndi nyenyezi imodzi ndi imodzi, koma ndi milalang’amba—magulu aakulu okhala ndi nyenyezi mamiliyoni zikwi zochuluka—yoti siinaonedwepo ndi anthu!

Ukulu, chinsinsi ndi kudabwitsa kwa thambo zimasonkhezera mantha aulemu mwa munthu woyang’anitsitsa. Komabe, zodabwitsa zoterozo zimasonyeza chabe ulemerero ndi mphamvu za Mlengi. Baibulo limatcha Yehova Mulungu “Atate wa mauniko” ndipo limatiuza kuti “aŵerenga nyenyezi momwe zili; azitcha maina zonsezi.”—Yakobo 1:17; Salmo 147:4.

Kukula kwa thambo kumaonekeranso mu nthaŵi yotheredwa ndi zochitika za kumwamba. Kuwala kochokera ku milalang’amba yomwe inajambulidwa ndi telesikopo ya Hubble Space kunali kuyenda mumlengalenga kwa zaka mamiliyoni zikwi zochuluka! Poyerekezera ndi kukhalitsa kwa miyamba, kodi kukhalapo kwathu kwa nthaŵi yaifupi ndi kuchepa kwathu sikuyenera kutipatsa mantha aulemu ndi ulemu wakuya kwa Uyo amene anapanga nyenyezi? (Yesaya 40:22,26) Kuzindikira kuti Mulungu amene analenga zonsezi ‘amakumbukiranso munthu ndi kumsamalira’ kumazamitsa chiyamikiro chathu kwa Mlengi wathu ndipo kumatipangitsa kufuna kumdziŵa ndi kumkondweretsa. (Salmo 8:3, 4 NW) Ulemu waukulu ndi chiyamikiro choterecho ndi zimene Baibulo limatcha kuti kuopa Mulungu.

Mulungu Wokhululukira

Tonsefe tilibe ungwiro. Timachimwa, osati mwadala, ngakhale pamene tikuyesetsa kuchita chabwino. Zimenezi zitachitika, kodi tiyenera kuchita mantha kuti sitiyanjidwanso ndi Mulungu? Wamasalmo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.” (Salmo 130:3, 4) Kudziŵa kuti “Mpangi Wamkulu” (NW) ndi wachifundo kwambiri ndi wokhululukira kumasonkhezera chiyamikiro ndi ulemu wakuya mwa alambiri ake.—Yesaya 54:5-8.

Kuopa Mulungu kumatisonkhezera kuchita chabwino ndiponso kusachita zimene Mulungu amati ndi zoipa. Unansi wathu ndi Atate wathu wakumwamba ungayerekezeredwe ndi atate wabwino waumunthu ndi ana ake. Panthaŵi zina ana angaiŵale chifukwa chake atate wawo amawaletsa kumaseŵera mumsewu. Komabe, pamene amakhumbira kuseŵera mpira mumsewu wa magalimoto, kungokumbukira zimene atate wawo anawauza kumawaletsa—mwinamwake kuwatetezera ku imfa. Mofananamo, kuopa Yehova kwa munthu wamkulu kungamletse kuchita kanthu kamene kangawononge miyoyo—wa iye mwini ndi ya ena.—Miyambo 14:27.

Kuopa Chiweruzo cha Mulungu

Kumbali ina, munthu amene chikumbumtima chake sichimletsa kusakondweretsa Mulungu ali ndi chifukwa chokhalira wamantha mwa njira ina. Mulungu ali ndi ufulu wolanga ochita zoipa mwadala ndi osalapa, monga mmene maboma a anthu amalangira opalamula. Kulola kuipa kwa kanthaŵi kwa Mulungu kwapangitsa ena kuumirira panjira yoipa. Koma Baibulo limasonyezeratu kuti tsiku lina posachedwapa Mulungu adzachotsa kuipa konse padziko lapansi. (Salmo 37:9, 10; Mlaliki 8:11; 1 Timoteo 5:24) Oipa osalapa ali ndi chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu. Komatu, kuopa kotereku sikumene Baibulo limalimbikitsa.

M’malo mwake, Baibulo limagwirizanitsa kuopa Yehova ndi zinthu zabwino m’moyo—kuimba, chimwemwe, kukhulupirira, nzeru, moyo wautali, chidaliro, ulemerero, chiyembekezo ndi mtendere, kungonenako zochepa.a Ngati tipitiriza kuyenda moopa Yehova, tidzasangalala ndi madalitso oterowo kosatha.—Deuteronomo 10:12-14.

[Mawu a M’munsi]

a Onani Eksodo 15:11; Salmo 34:11, 12; 40:3; 111:10; Miyambo 10:27; 14:26; 22:4; 23:17, 18; Machitidwe 9:31.

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Mwa chilolezo cha Anglo-Australian Observatory, anajambula ndi David Malin

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena