Chiyembekezo cha Mtsikana wa ku Russia
Mtsikana wazaka 15 wa ku Ukhta ku Russia, mzinda wa anthu oposa 100,000, womwe uli pamtunda wa makilomita 1,200 kumpoto chakummaŵa kwa Moscow, anafotokoza kuti akufunitsitsa kuti padziko lapansi zinthu zikhale bwino. Analongosola zimenezi m’kalata yotsatirayi yomwe analembera ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Russia:
“Mzanga anandiuza kuti buku lotchedwa Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako limanena za moyo wa Yesu Kristu. Ndimasangalala ndi mabuku, magazini, ndi mabrosha anu. Ndiloleni ndikulongosolereni mmene ndinayambira kuwakonda. Ndinapita ku positi ofesi kukalipira mabilu a wailesi ndi telefoni. Kumeneko ndinapeza trakiti pansi. Ndinaitola, nkukutumula fumbi, ndi kuyamba kuiŵerenga trakitiyo, imene inali ndi mutu wakuti ‘Nchifukwa Ninji Moyo Uli ndi Mavuto Ochuluka Motere?’
“Ndinaŵerenga za mavuto ndi kuvutika kumene anthu ali nako, ndipo koyambirira kwa trakitiyo inasonyeza za lonjezo la moyo watsopano m’Paradaiso. Ndikuyembekeza kuti tsiku lina zidzachitika. Ndimafunitsitsa kuona anthu onse ali okondwa, okhutiritsidwa, ndi athanzi ndiponso ndimafuna kuona achibale omwe anafa. . . . Ndifuna kudziŵa zimene ndingachite kuti ndikhale ndi chiyembekezo chodzakhala m’Paradaiso padziko lapansi. Ndikukupemphani kunditumizira uthenga kapena mabuku ena. Ndidzalipira ndalama za mabukuwo kuphatikizapo ndalama zotumizira.”
Inunso mungathe kulandira mabuku amene akhoza kukuthandizani kukhala ndi chiyembekezo cholimba chokhala ndi maziko ake m’Baibulo cha kukhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi. Ngati mukufuna kulandira brosha yakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena ngati mungakonde kuti wina abwere kunyumba kwanu kuti muzidzaphunzira naye Baibulo, chonde lemberani ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku keyala yoyenera yomwe ili patsamba 5.