Tinathaŵa Mabomba—Patatha Zaka 50!
“Pano paphulika mabomba posachedwapa. Aliyense akabisale!”
NDI mawu amenewo ine ndi amuna anga tinachenjezedwa ndi wapolisi kuti tichoke m’nyumba ndi kuthaŵira m’phanga lobisalamo lomangidwa ndi simenti lomwe linali pafupi. Chilengezocho chinali chodzidzimutsadi. Chifukwatu sitinali m’dera lankhondo; tinkachezera anzathu pa chimodzi cha zisumbu zokongola kumapeto kwa Marshall Islands, mu Micronesia.
Tinabwera kudzacheza ndi mnzathu wina ndi amuna ake kwa mlungu umodzi pakachisumbu ka Tõrwã. Mkaziyo ndiye yekha anali Mboni ya Yehova pakachisumbuko, choncho tinkafuna kumthandiza kulalikira kwa anthu a kumeneko.
Mwachibadwa anthu a ku Marshall ngaubwenzi ndipo amakondweretsedwa kukambitsirana za Baibulo. Popeza kuti buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi linali litangotulutsidwa kumene m’chinenero cha kumeneko, tinali ndi mwaŵi wogaŵira makope ambiri. Onse amene anali kufuna bukuli anatitsimikizira kuti adzaŵerenga ndipo sadzaliyesa ken karawan, kapena kuti “chithumwa cha mwaŵi,” kuti azithamangitsira ziŵanda. Mwamwambo anthuwa amakonda kupinda pepala la m’Baibulo ndi kuliika m’botolo, nkumangirira botololo kudenga kapena mumtengo womwe uli pafupi, pakuti amati zimathamangitsa mizimu yoipa.
Kwa masiku angapo tinkakhala bwinobwino, koma litafika Loŵeruka, mwamsanga tinazindikira kuti lidzasiyana ndi masiku enawo. Mmaŵa patsikuli, tinayamba tasangalala ndi kusambira m’madzi oyera ndi ofunda a m’thamandalo. Pamene tinkachoka kugombeko tinaona sitima yapamadzi, yodera ndi yooneka kukhala mpingu. Mosakhalitsa tinadziŵa cholinga chake. Wapolisi wina anatiuza kuti gulu la asirikali asanu ndi aŵiri a ku America linabwera kudzaphulitsa mabomba akale pachisumbucho. Kuti aliyense atetezedwe, anthu a pachisumbucho anafunika kukhala tsiku lonselo m’mapanga amene anamangidwa panthaŵi ya Nkhondo Yadziko II ndi Ajapani, osati m’nyumba zawo.
Mapanga amenewo, amene okacheza ku Tõrwã amawaona mwamsanga atafika, ndi umboni wakuti zinali zoopsa mmbuyomu. Chisumbuchi patali chimaoneka monga paradaiso, koma pafupi zimadziŵikiratu kuti kukongola kwake kukuipitsidwa ndi zipsera za nkhondo imene inatha zaka 50 zapitazo. Pachisumbuchi pali zokumbutsa Nkhondo Yadziko II zambiri popeza kuti panthaŵiyo Ajapani anamangapo msasa wawo waukulu wa nkhondo ya m’mlengalenga. Paliponse pali zotsalira za nkhondo za dzimbiri—ndege zankhondo, mfuti zamiyendo zoimikidwa, ndi zida zophulitsira sitima zapamadzi—zobisika m’maudzu ndi mitengo.
Komabe, ndi mabomba otsalira amene amachititsa mantha kwambiri. Panthaŵi yankhondoyo, asirikali a United States anaponya mabomba, mabomba a moto, ndi maroketi oposa matani 3,600 mu Tõrwã, ndipo Ajapani anali ndi nkhokwe zawo za mabomba ndi zida kumeneko. Ngakhale kuti nkokayikitsa kuti bomba lotha zaka 50 lingaphulike, mabomba nthaŵi zonse ngoopsa kwambiri, nchifukwa chake magulu ochotsa mabomba abwera pachisumbuchi kasanu konse kuchokera mu 1945, chaka chimene nkhondoyo inatha.
Tinakayikira ngati chenjezolo linalidi loona, choncho tinapita kukalankhula ndi gulu lochotsa mabombalo kumalo kumene linatsikira sitima. Iwo anati sikokha kuti chenjezolo nloona, komanso kuti mabomba adzayamba kuphulika ola lisanathe! Tinauzidwa kuti ngati sitikufuna kubisala m’phanga tiyenera kuchoka pachisumbucho nthaŵi yomweyo.
Mnzathuyo anaganiza zotsalira ku Tõrwã ndipo anakabisala m’phanga lalikulu lokonzeramo mfuti pamodzi ndi mabanja ena ambiri. Kenako anadzatiuza kuti mazenera omwe ali m’phangalo ndi kokha ziboo zomwe onkawombererapo mfuti ndipo munali kutentha kwambiri, anthu anapanikizananso kwabasi. Kutha tsikulo mmenemo, kunamkumbutsa zaka zankhondo ndipo anavomera kuti pamene anali mwana ankasangalala mabomba akamaphulika, koma tsopano anali kuopsa kwambiri.
Amuna ake anavomera kutipititsa ku Wollet Island, makilomita asanu ndi atatu kuchokera ku Tõrwã, m’kabwato ka injini. Patangopita mphindi zoŵerengeka titanyamuka tinamva chiphokoso cha kuphulika kwa bomba. Titayang’ana ku Tõrwã, tinaona utsi uli tolo pafupi ndi nyumba zogona za anthu a pachisumbupo. Osakhalitsa linanso linaphulika, kenaka lachitatu, lalikulu kwambiri linaphulikanso.
Tinatha tsiku lonselo tikulalikira ku Wollet, ndipo nthaŵi ndi nthaŵi tinali kudzidzimutsidwa ndi mabomba ophulika kutali. Miyezi ingapo pasadakhale, mabomba akaleŵa anafufuzidwa ndipo anaika chizindikiro pamene anali. Mabomba anapezedwa paliponse—m’mphepete mwa nyanja, kumtunda kubwalo la ndege, ndipo ngakhale panyumba za anthu! Gulu lochotsa mabombalo linasonkhanitsa pamodzi timabomba tating’ono nkutiphulitsira pamodzi kuti lichepetse nthaŵi za kuphulika kwa mabombawo.
Dzuŵa linali pafupi kuloŵa pamene tinkafika ku Tõrwã. Tikuyandikira, tinaona kuti utsi womwe unkaoneka nthaŵi zonse pamene anthu anali kuphika sunkaonekanso. Tinadziŵa kuti sizinali bwino. Mwadzidzidzi, kabwato kena kanathamangira kumene kunali ife ndi kutichenjeza kuti tisayandikire. Bomba lina lalikulu lomwe linali m’madzi pafupi ndi miyala ikuluikulu linali lisanaphulitsidwebe. Choncho, pakuloŵa kwa dzuŵa mmene tinali kuchoka chakumtundako, tinaona chinthu chimene anthu ambiri amene ali ndi moyo lerolino sanachionepo—kuphulika kwa bomba la m’madzi la Nkhondo Yadziko II limene linathuvutsa madzi ndi utsi mamita mazana ambiri m’mwamba!
Chosangalatsa nchakuti palibe amene anavulala patsikulo ku Tõrwã. Kodi gulu lochotsa mabombalo linachotsa mabomba onse otsalira pachisumbucho? Mwina ayi. Mtsogoleri wa gululo anati akuganiza kuti anthu a pachisumbucho angakapezebe mabomba ena akale mtsogolo. Pamene tinali kutsiriza ntchito yathu yolalikira pa Tõrwã, zimenezitu zinatipatsa nkhani yabwino yokambitsirana ndi anthu. Unalidi mwaŵi kuuza anthu a pachisumbuŵa za nthaŵi pamene Ufumu wa Yehova ‘udzaletsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi.’—Salmo 46:9.
Yosimbidwa ndi Nancy Vander Velde
[Chithunzi patsamba 25]
Bomba losaphulika