Kunenapo za Nyengo
KAYA mumakhala kuti ndiponso kaya ndinu ndani, nyengo imakhudza moyo wanu. Ngati kwaoneka kuti kudzatentha ndipo kudzakhala dzuŵa, mumavala zovala zopepuka. Ngati kwazizira, mumavala jekete ndi chisoti. Kukamagwa mvula? Mumatenga ambulela.
Nthaŵi zina timasangalala ndi mmene kwachera; nthaŵi zina timakhumudwitsidwa. Nthaŵi ndi nthaŵi nyengo imakhala yakupha kukakhala mkuntho, kavulumvulu, chilala, kukagwa chipale chofewa kwanthaŵi yaitali, kapena chimvula. Kaya tiikonda kaya ayi, kaya tiitukwana kaya tingonyalanyaza, nyengo imakhalapo basi, ikumakhudza miyoyo yathu kuyambira tsiku limene tinabadwa kufikira tsiku limene tidzafa.
Nthaŵi ina wina wake anakambapo mawu akuti: “Aliyense amanena za nyengo, koma palibe amene amachitapo kanthu kuti aisinthe.” Ndithudi, nthaŵi zonse zaoneka kuti tilibe mphamvu zosintha nyengo mwanjira ina iliyonse. Komabe, asayansi ambiri sakhulupiriranso zimenezo. Iwo amati kuwonjezereka kwa mphweya wa carbon dioxide ndi mipweya ina mumlengalenga kukupangitsa kuti nyengo isinthe.
Malinga nkunena kwa akatswiri ake, kodi pali kusintha kotani? Mwinamwake yankho lenileni ndi limene anapereka a bungwe la Intergovernmental Panel on Climate Change (IPCC), limene analitenga pa mfundo za akatswiri 2,500 a zanyengo, zachuma, ndi za akatswiri ooneratu za ngozi zakutsogolo a m’maiko 80. M’lipoti lake la 1995, bungwe la IPCC linati dziko lapansi likunka litentha. M’zaka za zana likubwerali, ngati zinthu zipitirira kukhala mmene zilirimu, zikhoza kutheka kuti kutentha kwapadziko kudzawonjezeka ndi 3.5 digiri Celsius.
Ngakhale kuti kutentha kowonjezereka madigiri pang’ono kungaoneke ngati kosadetsa nkhaŵa, kuwonjezereka kwa kutentha pa nyengo yadziko lonse kukhoza kukhala kowononga. Zotsatirazi ndizo zimene ambiri akuona kuti zidzachitika m’zaka za zana likudzali.
Kutentha kopambanitsa m’zigawo zina. M’madera ena mudzakhala chilala chopitirira, pamene mwina mvula izikagwa yamphamvu kwambiri. Kudzakhala mkuntho ndi kusefukira kwa madzi koopsa; mkuntho uzikawononga kwambiri. Ngakhale kuti mamiliyoni amafa ndi kusefukira kwa madzi ndiponso njala, kutentha kwa padziko lonse kudzapangitsa kuti chiŵerengero cha imfa chikwere kwambiri.
Matenda adzachuluka. Matenda a mtima ndiponso imfa zidzachuluka kwambiri. Malinga nkunena kwa bungwe la World Health Organization, kutentha kwapadziko lonse kudzakulitsa dera limene muli matenda a m’madera otentha ofalitsidwa ndi tizilombo monga malungo ndi dengue. Kuwonjezera apo, kuchepa kwa madzi abwino kochitika chifukwa cha kusintha kwa kagwedwe ka mvula ndi chipale chofewa m’madera ena mwina kudzachulukitsa matenda ndi tizilombo toyambitsa matenda tomwe timafalikira m’madzi ndi m’chakudya.
Kuwonongeka kwa malo okhala zinyama. Nkhalango ndi madambo, zimene zimasefa mpweya ndi madzi, zidzawonongeka chifukwa cha kutentha ndi kusintha kwa kagwedwe ka mvula. Mwina kuzidzabuka moto woopsa wolusa wa m’nkhalango.
Kusefukira kwa madzi a m’nyanja. Omwe amakhala m’mphepete mwa nyanja adzayenera kuchoka pokhapokha patachitika ntchito yodya ndalama zambiri yotseka madzi kuti asasefukire. Zilumba zina zidzamira.
Kodi nkoyenera kukhala ndi mantha otero? Kodi nzoonadi kuti dziko layamba kuwonjezereka kutentha? Ngatidi zili choncho, kodi anthu ndiwo achititsa? Popeza zinthu zambiri zili pangozi chotero, nzosadabwitsa kuti akatswiri odziŵa za nyengo akukambitsirana kwambiri za mafunso ameneŵa. Nkhani ziŵiri zotsatirazi zikukamba za mfundo zina zokhudza nkhaniyi ndiponso kulongosola zakuti kaya tiyenera kumadera nkhaŵa za tsogolo la pulaneti lathuli.