Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g98 6/8 tsamba 18-20
  • Njira Zisanu Zowongolera Moyo Wanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Zisanu Zowongolera Moyo Wanu
  • Galamukani!—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Choyamba: Limani Dimba
  • Chachiŵiri: Muzigula Zambiri
  • Chachitatu: Phunzirani Kusunga Zakudya
  • Chachinayi: Yesani Kuŵeta Ziŵeto Pang’ono
  • Chachisanu: Khalani Audongo
  • N’chifukwa Chiyani Ukhondo Uli Wofunika?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Chakudya Chochokera M’dimba Lanu
    Galamukani!—2003
  • Kodi Mungasamalire Motani Banja?
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Zimene Mungachite Kuti Mukhale Ndi Moyo Wathanzi
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1998
g98 6/8 tsamba 18-20

Njira Zisanu Zowongolera Moyo Wanu

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU CENTRAL AFRICAN REPUBLIC

KUKWERA kwa mitengo ya zinthu, matenda, matenda a njala, umphaŵi—mavuto ameneŵa ndi ofala kwambiri m’maiko omatukuka kumene. Ndipo sikukuoneka kuti papezeka njira yothetsera zimenezi posachedwapa, makamaka m’kaonedwe ka munthu. Ngati mumakhala m’dziko lotukuka kumene, kodi pali china chilichonse chimene mungachite kuti muwongolere moyo wanu? Inde chilipo! Zotsatirazi ndi njira zisanu zimene mungazipeze kukhala zothandiza ndi zosavuta kuchita.

Choyamba: Limani Dimba

“Wolima munda wake zakudya zidzamkwanira,” limatero Baibulo pa Miyambo 28:19. Ndithudi, zingakudabwitseni kuona mmene kamalo kang’onong’ono kangatulutsire zakudya. M’buku lake lotchedwa Le jardin potager sous les tropiques (Munda wa Ndiwo Zamasamba m’Maiko a m’Madera Otentha), mlembi wotchedwa Henk Waayenberg ananena kuti kadimba kokwanira mamita 50 kufika 100 m’mbali zonse kangathe kutulutsa ndiwo za masamba zokwanira banja la anthu asanu ndi mmodzi!

Nkuguliranji zinthu zimene mutha kulima nokha? Malinga ndi nthaka ndi nyengo yakwanuko, mukhoza kulima pafupi ndi nyumba yanu mbewu monga therere, tsabola, spinaki, parsley, lemongrass, anyezi, chinangwa, maungu, mbatata, mzimbe, tomato, zinkhaka, ndi chimanga. Dimba ngati limeneli lingathe kuwonjezera chakudya chimene banja lanu limakhala nacho ndiponso mukhoza kukhala ndi zina zochulukirapo zoti nkumagulitsa.

Ngati muli ndi malo aakulu, mungalingalirenso zobzala mitengo yazipatso zamitundumitundu. Nthaŵi zina mtengo wa zipatso umodzi chabe ungathe kumabereka zoposa zimene inu ndi banja lanu mukhoza kudya. Ngati mutadziŵa kupanga manyowa—mwakuoletsa zomera ndi kudzazigwiritsira ntchito monga feteleza—zidzakuthandizani kuti mukhale ndi zakudya zochuluka. Mitengo ingachite zambiri kuposa kupatsa banja lanu chakudya ndi ndalama zowonjezera chabe. Mitengo mutaibzala mmalo oyenerera ingathe kumapanga mthunzi, kusefa mpweya, ndi kupangitsa malo anu kukhala okongola ndi osangalatsa.

Koma bwanji ngati simudziŵa zambiri ponena zaulimi? Kodi mulibe mabwenzi, anansi, kapena anthu ena amene mumawadziwa ndipo amadziŵa zaulimi? Bwanji osawafunsa kuti akuthandizeni kapena kukupatsani malangizo? Mungathenso kugula kapena kubwereka mabuku onena zaulimi.—Onani nkhani yakuti “Bwanji Osalima Dimba la Ndiwo za Masamba?” mu Galamukani! yachingelezi ya May 22, 1974.

Chachiŵiri: Muzigula Zambiri

Kodi zinthu zofunika monga ufa, mpunga ndi mafuta ophikira, mumagula zochepa chabe? Ngati zili tero, mumasakaza bajeti yanu kwambiri. M’malo mwake, ngati nkotheka, muziyesetsa kugula zakudya zambiri, kusonkherana ndalama mabanja aŵiri, atatu, kapena kuposerapo. Kugula zakudya zambiri kukhoza kukuthandizani kusunga ndalama ngati mugula panthaŵi imene zipatso kapena ndiwo zamasamba zikucha. Nthaŵi zina, mukhoza kugula zinthu zambiri pamtengo wa maoda.

Chachitatu: Phunzirani Kusunga Zakudya

Kugula zambiri panthaŵi imodzi kumapangitsa kuyamba kulingalira zakuti kodi zinthu zosachedwa kuwonongeka nkuzisunga bwanji. Njira yofala kwambiri yosavuta ndi kuyanika zakudya. Azimayi ambiri mu Afirika amapeza zofunika pa moyo wawo mwa kuyanika zipatso, therere, nyemba, squash, nthanga za maungu, ndi masamba ena. Sipafunikira zipangizo zapadera kuti muyanike zakudya. Mukhoza kuyanika chakudyacho pamalo osamalika kapena kuchimangirira, mwina kuchivundikira ndi nsalu yopyapyala kuti pasamatere ntchentche. Mphepo ndi dzuŵa zidzagwira ntchito yonse.—Onani nkhani yakuti “Kodi Mungakhale ndi Moyo ndi Zochepa?” mu Galamukani! yachingelezi ya August 8, 1975.

Chachinayi: Yesani Kuŵeta Ziŵeto Pang’ono

Kodi mungathe kuŵeta nkhuku, mbuzi, nkhunda, kapena ziŵeto zina zanuzanu? M’malo ambiri nyama amadya kamodzikamodzi. Koma mwakungothandizidwa pang’ono ndi ena, mukhoza kuphunzira kuŵeta ziŵeto pang’ono. Kodi mumakonda kudya nsomba? Chabwino, yeserani kuphunzira kupanga kadamu kakang’ono. Nyama, mazira, ndi nsomba zimakhala ndi iron, calcium, mavitameni, maminero, ndi maproteni—ofunika pa thanzi la banja lanu.

Chachisanu: Khalani Audongo

Ukhondo ngwofunikanso kuti banja lanu likhale lathanzi. Uve umapangitsa kuti pakhale makoswe, ntchentche, ndi mphemvu—zomwe zimapangitsa matenda osiyanasiyana. Kukhala waukhondo kumalira nthaŵi ndiponso khama. Koma ndalama zimene mumawonongera pa kupangitsa malo anu kukhala aukhondo nzochepa poyerekeza ndi ndalama zimene mumawononga pogula mankhwala ndi kulipira dokotala. Kukhala waukhondo kumasiyana pamlingo wina wake pakati pa munthu mmodzi ndi wina ndiponso dziko lina ndi linzake. Komabe pali mfundo zingapo zimene zingagwire ntchito kulikonse.

Mwachitsanzo, lingalirani za zimbudzi. M’midzi amazilekerera kuti zikhale zonyansa ndi zowonongeka motero zimapangitsa matenda osiyanasiyana. Ogwira ntchito zaumoyo akhoza kukupatsani malangizo a mmene mungamangire chimbudzi chabwino pamtengo wotsika.

Bwanji za nyumba yanu? Kodi njaukhondo ndi yosamalika? Kodi imanunkhira bwino? Bwanji za khichini lanu? Kodi nlaukhondo? Chakudya chiyenera kukhala chabwino ndi chophikidwa bwino kuti chikhale chopatsa thanzi. Madzi osasamalika amakhala ndi tizilombo toyambitsa matenda. Motero muyenera kusefa kapena kuŵiritsa madzi musanayambe kuwagwiritsira ntchito. Muyenera kutsuka ziŵiya zodyera ndi madzi otentha, ndi kusamba mmanja bwino kwambiri musanagwire chakudya. Sungani madzi m’chosungira choyera ndi chovundikira.

Agalu, amphaka, nkhuku, ndi mbuzi simuyenera kuzilekerera kuloŵa m’khichini—osazilekerera ngati mufuna kukhala ndi malo aukhondo. Nawonso makoswe ndi mbeŵa osazilekerera kuti ziziyenda pa ziŵiya zanu zophikira ndi kumaipitsa zakudya zanu. Vutoli likhoza kuthetsedwa mwakungotchera msampha wamakoswe.—Onani nkhani yakuti “Kukumaniza Chitokoso cha Udongo,” mu Galamukani! ya October 8, 1988.

Ufumu wa Mulungu ndiwo wokha umene udzathetsa mavuto onse a mtundu wa anthu pomalizira pake. (Mateyu 6:9, 10) Komabe padakali pano, mfundo zosavuta kuchita zimenezi zikhoza kukuthandizani kuwongolera moyo wanu.

[Zithunzi patsamba 18]

Limani dimba

[Zithunzi patsamba 19]

Gulani zambiri

[Zithunzi patsamba 19]

Phunzirani kuyanika zakudya

[Zithunzi patsamba 20]

Yeserani kuŵeta ziŵeto pang’ono

[Zithunzi patsamba 20]

Khalani aukhondo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena