“Magazini Yotsogola”
Kodi munaŵerengapo magazini ya Galamukani!? Kodi magazini ili m’manja mwanuyi mumaiona bwanji? Kodi mumaona kuti nkhani zake nzopindulitsa, zofotokozedwa bwino, ndiponso zotsagana ndi zithunzi zokongola?
Wolemba mabuku wina wodziimira payekha, wa ku Nigeria, analemba kuti: “Ndimaŵerenga Galamukani! nthaŵi zonse, ngakhale kuti si ndine wa Mboni za Yehova. Galamukani! ndi magazini yotsogola. M’magaziniyo ndimapezamo malingaliro ambiri ndikafuna kulemba. Zikuto zake nzokongola ndipo zimapangitsa woŵerenga wopanda tsankho kutsegula msanga masamba ake. M’kope lililonse mumaoneka kuti muli zatsopano zokhazokha; tsamba lililonse limasonyeza kuti olembawo ndi atolankhani aluso. Chifukwa cha nkhani zapanthaŵi yake ndi zolembedwa bwino, kope lililonse lili ndi chidziŵitso chamtengo wapatali ndipo chopindulitsa.”
Tikukulimbikitsani kuŵerenga nkhani za m’kope lino la Galamukani! Ngati mungafune kope lina, pemphani mwa kulembera kalata ku Watch Tower, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi, kapena kulembera ku adresi yoyenera, patsamba 5. Tingakondwe kukutumizirani kope lina, kapena mutapempha, wina angabwere kwanu kudzakambitsirana nanu kuti nthaŵi zimene tikukhalamozi zikutanthauzanji.