“Dziko Lokhala Mwaufulu ndi Mogwirizana”
Kodi mumakhulupirira kuti zimenezi zidzachitika? Mayi wina wa ku Florida, U.S.A., analemba kuti: “Trakiti lanu lakuti “Kodi Anthu Onse Adzakondanapo? ndilo umodzi wa mauthenga olimbikitsa kwambiri amene ndaŵerengapo. Ndinaliŵerenga mobwerezabwereza. Nthaŵi zonse ndikaŵerenga ndimasangalala—chifukwa cha mfundo yonena za dziko lokhala mwaufulu ndi mogwirizana.”
Ngati inunso mukufuna umboni wakuti anthu akhoza ndipo adzakhala mwaufulu ndi mogwirizana, lemberani ku Watch Tower Society, Box 30749, Lilongwe 3, Malaŵi. Kapena ku adiresi yoyenera mwa zomwe zili patsamba 5. Tidzakutumizirani brosha la masamba 32 lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Tikhulupirira kuti chigawo 10, chakuti “Dziko Latsopano Lokongola Koposa la Mulungu,” chidzakusangalatsani.