‘Kudikira Mwachidwi Paradaiso Akudzayo’
Zimenezo nzimene mnyamata wina wazaka 14 wotchedwa Aleksandr ananena m’kalata yomwe analembera ku ofesi yanthambi ya Watch Tower Society ku Russia. Mnyamata wa ku Russia ameneyu anali atapatsidwa makope a Nsanja ya Olonda limodzi ndi mabuku ena omwe Mboni za Yehova zimafalitsa. M’kalata yakeyo anafotokoza kuti:
“Pamene ine ndi makolo anga tinali kupita ku Khabarovsk pasitima yapamtunda a Mboni za Yehova anatiyandikira. Ndiye anatiuza zambiri zonena za maulosi a Baibulo, za masiku otsiriza, ndi za moyo wosatha padziko lapansi.”
Pomaliza mnyamatayo anati: “Nkosangalatsatu kudziŵa kuti posachedwapa kuipaku kudzatha ndi kutinso anthu adzakhala kwamuyaya padziko lapansi! Ndikudikira mwa chidwi nthaŵi imene dzikoli lidzasandutsidwa paradaiso wokongola. Ndingayamikire kwambiri mutandilembera ndi kundiuza mmene phunziro la Baibulo limakhalira.”
Mwinatu nanunso mukufuna mutadziŵa zambiri zimene Mulungu akufuna kudzachita. Ngati mukufuna mungalembe m’kabokosi kali pansipa ndi kukatumiza ku Watch Tower Society, Box 30749, Lilongwe, kapena ku adiresi ina yoyenera patsamba 5.
□ Nditumizireni bolosha lakuti Kodi Mulungu amafunanji kwa Ife?
□ Ndifotokozereni za phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.