Kalata Yapadera Yopita kwa Makolo Awo
Atsikana aŵiri a ku Spain posachedwapa analemba kalata yoyamikira kwa makolo awo. Zina mwa zimene analemba ndi izi:
Kwa makolo athu okondedwa, Pepe ndi Vicenta:
Tiyambire pati? Pali zinthu zambiri zimene tikufuna kunena, ndipo m’povuta kuzinena m’mawu apang’ono chabe. Tikufuna kukuthokozani chifukwa cha zaka 17 ndi 15 zimene takhala ndi moyo, zaka zimene tasamalidwa ndi kukondedwa kwambiri.
Takhala tikudziŵa zofuna zanu ndi malamulo anu. Nthaŵi zina sitinkamvetsa chifukwa chomafikira kunyumba panthaŵi yoikika, koma tsopano, titaona zimene zawachitikira anzathu amene analibe nthaŵi yoikika yotere, tazindikira kuti tinatetezedwa ndi malamulo amenewo.
Chitsanzo chanu cha kusaphonya misonkhano yachikristu ku Nyumba ya Ufumu, pokhapokha ngati pali zifukwa zenizeni, chatithandiza kwambiri, monga momwe kulalikira nanu Lamlungu kwatithandiziranso. Lamlungu mmaŵa uliwonse sitimachita kufunsa ngati tipite ku utumiki wakumunda. Timangodziŵiratu kuti tipita basi!
M’kuleredwa kwathu taphunziranso kuchereza alendo. Anthu ambiri akhala akufika kunyumba kwathu, ndipo nthaŵi zonse mumawapatsa chisamaliro chabwino koposa. Taziona zimenezi monga ana, ndipo tikuyamikira kuti tili ndi makolo apadera.
Palibe aliyense amene amatidziŵa monga inu. Ndinu mabwenzi apamtima, amene timakukhulupirirani kotheratu.
Potsiriza, tikufuna kukuuzani kuti timakukondani. Ndinu makolo athu, ndipo sitingakusinthanitseni ndi ena alionse. Ngati zikanatheka kusankhanso makolo athu ndi kakhalidwe kathu, mosakayikira, tikanasankhanso inu, ndipo tidakakhalanso moyo womwewo.
Timakukondani kwambiri, ndife ana anu,
ESMERALDA NDI YOLANDA