Kukhumbira Kuuluka
“NDEGE, ina iliyonse, yakwaniritsa kamwambi komwe tinkakonda kunena tidakali anyamata, kuti ‘Chouluka chimatera.’”
Inayamba choncho nkhani ina yolembedwa ndi mlembi wokayikira, m’magazini ya The New York Times ya May 25, 1908—patangopita zaka zosakwana zisanu kuyambira pamene munthu ndi mng’ono wake, ana a Wright, anauluka ku Kitty Hawk, North Carolina, U.S.A. Mlembiyo, mokayikirabe zoti “makina ouluka” atsopanowo omwe anayamba kuoneka mumlengalenga tsiku lina angadzakhale ofunika, anasinkhasinkha zoti “ngati pangapezeke anthu omwe adzafuna kuyandama mumphepo patali kwambiri ndi dziko, ndiye kuti n’ngoŵerengeka.” Ngakhale kuti nkhaniyo inasonyeza kuti n’kotheka kuti mibadwo yam’tsogolo ingadzayamikire maulendo apandege, inatinso “chikhumbo choyenda maulendo ataliatali apandege . . . sichidzatheka.”
Koma malingaliro amenewo anapezeka kukhala olakwa kwambiri! Lero, anthu oposa biliyoni imodzi amauluka “maulendo ataliatali pandege” chaka chilichonse. Eya, pazaka zana limodzi chabe, ndege zasintha, sakuzipanganso ndi zipangizo zamatabwa osalimba, monga mmene ankazipangira kuchiyambi kwa zaka za zana lino; lero kuli ndege zotchedwa jet, zopangidwa ndi zitsulo zokongola, zokhala ndi compyuta mkati, zoyenda m’mwamba makilomita 10 kuchokera padzikoli, ndipo zimanyamula anthu mazana angapo kukawatula kutali kwambiri, anthuwo ali khale ngati m’nyumba.
M’zaka zino za zana la 20, sayansi yokonza ndege yapita patsogolo msanga kwambiri moti yasinthitsa dziko lathuli. Tingonena kuti, munthu sanayambe lero kuyesayesa kuuluka mumlengalenga, komanso sanayambe zaka makumi angapo—kapenanso zaka mazana angapo zapitazo. Chikhumbo choulukachi anthu anali nacho kuyambira kale ndithu.
[Chithunzi patsamba 11]
Lockheed SR-71 Blackbird, jet yaliŵiro loopsa padziko lonse, yothamanga makilomita 3,520 paola
[Chithunzi patsamba 11]
Boeing Stratoliner 307, c. 1940, yonyamula anthu 33, yothamanga makilomita 344 paola
[Mawu a Chithunzi]
Boeing Company Archives
[Chithunzi patsamba 11]
“Flyer,” ya mu 1903, ya munthu ndi mng’ono wake ana a Wright
[Mawu a Chithunzi]
U.S. National Archives photo