Tsamba 2
Ana Ali Pavuto—Kodi Angawateteze Ndani? 3-11
Padziko lonse lapansi ana akusautsidwa, ndipo vutoli likukulabe. Kodi angatetezedwe bwanji?
Ndikuthokoza Yehova Kaamba ka Ana Anga Aamuna Asanu 12
Mayi wina yemwe anafedwa mwamuna wake posachedwapa, akusimba nkhani yosangalatsa ya mmene iye ndi mwamuna wake anaphunzitsira ana awo aamuna asanu kukonda Yehova ndi kum’tumikira.
N’chifukwa Chiyani Sindikutha Kupeza Zinthu Zimene Ndimafuna? 18
Kungakhale kokhumudwitsa kwa achinyamata pamene alibe zinthu zimene amafuna. M’Baibulo muli uphungu womwe ungathandize.