Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 9/8 tsamba 18-23
  • Kutumikira Mulungu Poyang’anizana ndi Imfa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kutumikira Mulungu Poyang’anizana ndi Imfa
  • Galamukani!—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ndinadalitsidwa Pophunzira Kwambiri
  • Kagulu Katsopano Kachipembedzo
  • Kumangidwa Kwanga Koyamba
  • Msonkhano Woyembekezeredwa kwa Nthaŵi Yaitali
  • Zochitika Ndili Pafupi Kubatizidwa
  • Chizunzo Chiyambiranso
  • Zaka Zisanu ndi Zinayi za Kuvutika
  • Ufulu, Koma N’kumangidwanso
  • Kumasulidwa, Komabe N’kumazunzidwa
  • Potsiriza Pake Tinapeza Ufulu Wakulalikira!
  • Ndinali Wandale Tsopano Ndinasanduka Mkristu Wosakhudzidwa N’zandale
    Galamukani!—2002
  • Mulungu Wakhala Mthandizi Wathu
    Galamukani!—1999
  • Kuchokera ku Umphaŵi Wadzaoneni Kumka ku Chuma Chochuluka
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kuvomera Yehova Akamatipempha Kumadzetsa Mphoto Zambiri
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—1999
g99 9/8 tsamba 18-23

Kutumikira Mulungu Poyang’anizana ndi Imfa

YOSIMBIDWA NDI JOÃO MANCOCA

Pa June 25, 1961, asilikali anasokoneza msonkhano wathu wachikristu mu mzinda wa Luanda, ku Angola. Anthu makumi atatu tinakatsekeredwa m’ndende ndi kumenyedwa koopsa kotero kuti asilikaliwo ankadzatizonda pa theka la ola lililonse kuti aone ngati wina wafa. Ena tinawamva akunena kuti Mulungu wathu ayenera kukhala woona, popeza kuti tonse tinapulumuka.

TITAMENYEDWA motero, ine ndinakhala m’ndende ya São Paulo kwa miyezi isanu. Kenaka kwa zaka zisanu ndi zinayi zotsatira, ndinali kusamutsidwira kundende zosiyanasiyana ndipo ndinkamenyedwa kwambiri, kusasamalidwa, ndiponso kupanikizidwa ndi mafunso. Mosakhalitsa nditangomasulidwa kuchokera pamene ndinamangidwa mu 1970, ndinamangidwanso, ndipo apa ndinatumizidwa ku msasa wotchuka chifukwa cha kupha wa São Nicolau, umene tsopano ukutchedwa kuti Bentiaba. Ndinakhazikidwa kumeneku kwa zaka zokwanira ziŵiri ndi theka.

Mwina mungafune kudziŵa chifukwa chimene ine pokhala nzika yosunga malamulo ndinamangidwa motero chifukwa chouza ena zikhulupiriro zanga za m’Baibulo ndi kumenenso ndinayambira kuphunzira za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

Ndinadalitsidwa Pophunzira Kwambiri

Ndinabadwa mu October 1925 pafupi ndi tauni yotchedwa Maquela do Zombo, kumpoto kwa Angola. Pamene atate anamwalira mu 1932, amayi ananditumiza kwa achimwene awo ku Belgian Congo (pano akuti Democratic Republic of Congo) kuti ndizikakhala nawo. Si zimene amafunadi kuchita, koma analibe njira ina iliyonse yondisamalira.

Amalume anali a Bapatisiti, ndipo ankandilimbikitsa kuŵerenga Baibulo. Ngakhale kuti ndinaloŵa mpingo wawo, njala yanga ya uzimu sinathetsedwe ndi zimene ndinali kuphunzira, ndiponso sizinandilimbikitse kutumikira Mulungu. Komabe, amalume angaŵa ananditumiza kusukulu ndipo anandithandiza kuti ndiphunzire kwambiri. Mwa zina, ndinaphunzira kuyankhula Chifalansa. M’kupita kwa nthaŵi ndinaphunziranso kuyankhula Chipwitikizi. Nditamaliza sukulu, ndinapeza ntchito yoyendetsa makina oulutsira mawu pa wailesi ku nyumba youlutsira mawu yaikulu ku Léopoldville (pano akuti Kinshasa). Kenaka, pamene ndinali ndi zaka 20 ndinakwatira Maria Pova.

Kagulu Katsopano Kachipembedzo

Chaka chomwecho, cha 1946, ndinayamba kutsatira munthu wina wa ku Angola wophunzira kwambiri amene amatsogoza gulu lakwaya ndipo anali wachipembedzo cha Bapatisiti. Anali kufunitsitsa kuphunzitsa ndi kutukula anthu a chiyankhulidwe cha Chikikongo amene anali kukhala kumpoto kwa Angola. Anali atapeza kabuku kotembenuzidwa m’Chipwitikizi kotchedwa The Kingdom, the Hope of the World, (Ufumu, Chiyembekezo cha Dziko) kamene kanafalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society ndi kugaŵiridwa ndi Mboni za Yehova.

Wotsogolera gulu lakwaya ameneyu anatembenuzira kabuku kameneka m’Chikikongo ndi kumakagwiritsa ntchito pokambirana za m’Baibulo mlungu uliwonse ndi gulu la anthu a ku Angolafe amene tinali kugwira ntchito ku Belgian Congo. M’kupita kwa nthaŵi, mtsogoleri wa gulu lakwaya ameneyu analembera kalata ku likulu la Watch Tower Society ku United States ndipo anapatsidwa mabuku ena. Komabe, zimene anali kutiuza ife zinali zosakanikirana ndi za matchalitchi ena. Motero, sindinkatha kusiyanitsa bwinobwino pakati pa Chikristu choona ndi ziphunzitso zosakhala za m’malemba za Dziko Lachikristu.

Komabe, ndinaona kuti uthenga wa m’Baibulo umene unali m’zofalitsa za Watch Tower Society unali wosiyana ndi chilichonse chimene ndinamvapo ku Tchalitchi cha Bapatisiti. Mwachitsanzo, ndinaphunzira kuti Baibulo limagogomezera kwambiri kufunika kwa dzina la umwini la Mulungu, Yehova, ndi kutinso Akristu oona amadzitcha moyenera kuti Mboni za Yehova. (Salmo 83:18; Yesaya 43:10-12) Kuphatikizanso apo, mtima wanga unasangalatsidwa ndi lonjezo la m’Baibulo la moyo wosatha pa dziko lapansi kwa amene adzatumikira Yehova mokhulupirika.—Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3-5.

Ngakhale kuti chidziŵitso changa cha choonadi cha Baibulo chinali chochepa, ndinali kudzimva ngati mneneri Yeremiya, amene ankalephera kuletsa chikhumbo chake chachikulu chakuti ayankhule za Mulungu wake, Yehova. (Yeremiya 20:9) Anthu a m’gulu lathu la phunziro la Baibulo anayamba kupita nane ndikamakalalikira kunyumba ndi nyumba. Mpaka ndinali kuchititsa misonkhano yapoyera pakhomo pa amalume anga. Ndimagwiritsa ntchito makalata olembedwa pa taipi poitana anthu. Panthaŵi ina anthu okwana 78 anapezekapo. Choncho panayambika gulu latsopano lachipembedzo lotsogozedwa ndi mtsogoleri wa ku Angola wa gulu lakwaya uja.

Kumangidwa Kwanga Koyamba

Ine sindinali kudziŵa kuti gulu lililonse lachipembedzo limene zochitika zake zinali zogwirizana ndi Watch Tower Society linali loletsedwa ku Belgian Congo. Motero pa October 22, 1949, ena a ife tinamangidwa. Tisanakazengedwe mlandu, woweruza anandiitanira pambali ndipo anayesa kupeza njira yakuti andimasule, chifukwa chakuti anali kudziŵa kuti ndinali kugwira ntchito m’boma. Koma kuti ndimasulidwe ndinayenera kusiya gulu limene linayamba chifukwa cha kulalikira kwathuko, ndipo ndinakana kutero.

Patatha miyezi iŵiri ndi theka akuluakulu a boma anaganiza zotitumiza kwathu ife amene tinali a ku Angola. Koma pamene tinafika ku Angola, nawonso akuluakulu a boma la Apwitikizi anali kukayikira ntchito yathu ndipo anatipatsa ufulu wochepa. Anthu enanso a gulu lathuli anafika kuchokera ku Belgian Congo, ndipo mpaka tinakwana anthu oposa 1,000 ofalikira m’dziko lonse la Angola.

Kenaka atsatiri a mtsogoleri wachipembedzo wina wotchuka Simon Kimbangu anaphatikizidwa m’gulu lathulo. Anthu ameneŵa sanali kufuna kuphunzira mabuku a Watch Tower Society, chifukwa chakuti amakhulupirira kuti Baibulo lingathe kulongosoledwa ndi munthu wotha kuyankhula ndi mizimu basi. Anthu ambiri m’gulu lathu anali kuvomerezana nawo maganizo ameneŵa, ngakhalenso mtsogoleri wa gulu lakwaya uja, amene amaonedwabe monga mtsogoleri wathu. Ndinali kupemphera mosaleka kuti Yehova atipatse woimira weniweni wa Watch Tower Society. Ndinali kukhulupirira kuti zinthu zitatero ndiye kuti gulu lathu lonselo lidzayamba kukhulupirira kuti livomereze choonadi cha m’Baibulo ndi kusiya kuchita zinthu zosagwirizana ndi malemba.

Ochepa chabe mwa ife tinali kulalikira ndipo anthu ena a m’gulu lathu anali kudana nazo zimenezi. Choncho anakatineneza kuboma ndi kutinamizira kuti tinali atsogoleri a gulu linalake landale. Chifukwa cha zimenezi mu February 1952 angapo a ife tinamangidwa, kuphatikizapo Carlos Agostinho Cadi ndi Sala Ramos Filemon. Tinatsekeredwa m’chipinda chopanda mazenera. Komabe, mlonda wina wabwino anatibweretsera chakudya kuchokera kwa akazi athu ndiponso taipi kuti tithe kupanga makope ambiri a timabuku ta Watch Tower Society.

Patatha milungu itatu tinapititsidwa ku Baia dos Tigres, dera lina lachipululu kummwera kwa dziko la Angola. Akazi athu anapita nafe. Tinapatsidwa chilango cha zaka zinayi tikugwira ntchito ya kalavula gaga, ndipo tinkagwira ntchito ku kampani ina yopha nsomba. Ku Baia dos Tigres kunalibe doko la mabwato amene timaphera nsombawo, choncho akazi athu anali kuyenda maulendo ambirimbiri molimbana ndi madzi kuchokera mmaŵa mpaka usiku kumasenza matumba akuluakulu a nsomba kuchokera m’mabwatowo.

Mu msasa wa ndende umenewu tinapeza anthu ena a gulu lathu ndipo tinayesa kuwakopa kuti apitirize kuphunzira Baibulo. Koma iwo anasankha kutsatira Toco, mtsogoleri wa oimba uja. Ndipo kenaka anayamba kutchedwa kuti Atoco.

Msonkhano Woyembekezeredwa kwa Nthaŵi Yaitali

Tili ku Baia dos Tigres tinapeza adiresi ya nthambi ya Watch Tower Society ya Northern Rhodesia (pano akuti Zambia) ndipo tinawalembera kalata yowapempha kuti atithandize. Kalata yathu inatumizidwa ku nthambi ya South Africa imene inatilembera kalata yotifunsa chimene chinatichititsa kuti tisangalatsidwe ndi choonadi cha m’Baibulo. Likulu la Watch Tower Society ku United States linauzidwa za ife, ndipo linatumiza munthu wina wapadera woliimira kuti adzakumane nafe. Munthu wake anali John Cooke, mmishonale amene anali atakhala zaka zambiri m’mayiko achilendo.

Mbale Cooke atafika ku Angola, anakhala milungu ingapo akuluakulu a boma la Apwitikizi asanamulole kuti akumane nafe. Anafika ku Baia dos Tigres pa March 21, 1955, ndipo analoledwa kukhala nafe kwa masiku asanu. Anali kulongosola Baibulo mokhutiritsa kwambiri, ndipo ine ndinatsimikiza kuti analidi kuimira gulu lokha loona la Yehova Mulungu. Patsiku lotsiriza la ulendo wake, Mbale Cooke anakamba nkhani yapoyera ya mutu wakuti “Uthenga Uwu Wabwino wa Ufumu.” Anthu okwanira 82 anafikapo, kuphatikizapo bwanamkubwa wa ku Baia dos Tigres. Aliyense amene analipo analandira pepala lokhala ndi nkhani imeneyi italembedwa pa taipi.

Pa miyezi isanu imene anakhala ku Angola, Mbale Cooke anakumana ndi anthu ochuluka otsatira Toco, kuphatikizaponso mtsogoleri wawo. Komabe ambiri a iwo sanali kusangalatsidwa kuti akhale a Mboni za Yehova. Choncho ine ndi anzanga tinaona kuti kunali koyenera kudziŵitsa akuluakulu aboma maganizo athu. Tinachita zimenezi polemba kalata, yokhala ndi deti la June 6, 1956, ndipo inali yopita kwa “Wolemekezeka Bwanamkubwa wa Chigawo cha Moc̗âmedes.” Tinanena kuti ife tsopano sitikugwirizana konse ndi otsatira a Toco ndipo tizionedwa monga “anthu a Bungwe la Mboni za Yehova.” Ndipo tinapemphanso kuti tipatsidwe ufulu wa kulambira. Koma m’malo mwakuti chilango chathu chichepetsedwe, chinawonjezeredwa ndi zaka ziŵiri.

Zochitika Ndili Pafupi Kubatizidwa

Potsiriza pake tinamasulidwa mu August 1958, ndipo pobwerera ku mzinda wa Luanda, tinapezako gulu laling’ono la Mboni za Yehova. Panali patatha chaka chimodzi Mervyn Passlow, mmishonale amene anatumizidwa ku Angola kuti akaloŵe m’malo mwa John Cooke, atathandiza gululo kumachita zinthu mwadongosolo, koma ife tisanafikeko iyeyu anali atathamangitsidwa kale m’dzikoli. Kenaka, mu 1959, Harry Arnott, mmishonale wina wa Mboni za Yehova, anatiyendera. Komabe iyeyu anamangidwa atangofika pa bwalo la ndege, ndiponso ife atatu amene tinapita kukamulandira tinamangidwanso.

Aŵiri enawo, Manuel Gonc̗alves ndi Berta Teixeira, amene anali Mboni za Chipwitikizi zongobatizidwa kumene, anamasulidwa atachenjezedwa kuti asachititsenso misonkhano ina iliyonse. Mbale Arnott anathamangitsidwa, ndipo ine ndinachenjezedwa kuti ndikangokana kulemba dzina langa m’kalata yawo, kusonyeza kuti si inenso wa Mboni ndiye kuti andibwezera ku Baia dos Tigres. Patatha maola asanu ndi aŵiri a kufunsidwa, ndinamasulidwa koma osalemba dzina langa n’komwe. Patangopita mlungu umodzi ndinabatizidwa, ndipo anzanga enanso Carlos Cadi ndi Sala Filemon anatero. Tinali kuchita lendi chipinda chogona ku Muceque Sambizanga, dera losauka la kunja kwa mzinda wa Luanda, limene linadzakhala malo a mpingo woyamba wa Mboni za Yehova ku Angola.

Chizunzo Chiyambiranso

Anthu okondwerera ochuluka anayamba kufika ku misonkhano. Ena anali kubwera kuti atipeze zifukwa ndi kukatineneza, koma misonkhanoyo inkawasangalatsa ndipo kenaka amakhala a Mboni za Yehova! Ndale zinali kusintha, ndipo zinthu zinativuta mowonjezereka pamene anthu ofuna boma lodziimira anaukira pa February 4, 1961. Ngakhale kuti tinali kunamiziridwa zinthu zambirimbiri, pa March 30 tinatha kuchita Chikumbutso cha imfa ya Kristu, ndipo kunabwera anthu okwana 130.

M’June pamene ndinali kuchititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda, msonkhano wathu unasokonezedwa ndi asilikali apolisi. Akazi ndi ana anasiyidwa, koma amunawo 30 amene analipo anatengedwa, monga mmene asonyezera mawu oyambawo. Tinamenyedwa mosalekeza kwa maola aŵiri ndi zibonga. Kwa miyezi itatu yotsatira ndinali kusanza magazi. Sindinali kukayikira kuti ndifa; ndiponsotu amene anandimenyayo ananenetsa kuti ndifa. Ena ambiri amene anamenyedwawo anali achatsopano, ophunzira Baibulo osabatizidwa, motero ndinali kuwapempherera mosalekeza kuti: “Yehova, samalani nkhosa zanu.”

Chifukwa cha kuchirikizidwa ndi Yehova, palibe aliyense amene anafapo, zimene zinadabwitsa asilikaliwo kwambiri. Ena mwa asilikali ameneŵa mpaka anatamanda Mulungu wathu, chifukwa amati ndi amene anachititsa kuti tikhalebe ndi moyo! Ambiri a ophunzira Baibulo ameneŵa m’kupita kwa nthaŵi anakhala Mboni zobatizidwa, ndipo ena pano akutumikira monga akulu achikristu. Mmodzi wa iwo Silvestre Simão, ali mu Komiti ya Nthambi ya Angola.

Zaka Zisanu ndi Zinayi za Kuvutika

Monga mmene ndinanenera pachiyambi paja, ndinavutika m’njira zambiri pa zaka zisanu ndi zinayi zotsatira ndipo ndinali kupititsidwa m’ndende kapena misasa ya chilango yambirimbiri. M’malo onseŵa ndinali kulalikira kwa akaidi omangidwa pa zifukwa za ndale, amene lero ambiri ndi Mboni zobatizidwa. Mkazi wanga Maria, pamodzi ndi ana athu ankaloledwa kupita nane.

Pamene tinali pa msasa wachilango wotchedwa Serpa Pinto, akaidi andale anayi anagwidwa akuyesa kuthaŵa. Anazunzidwa mpaka anafa akaidi onse akuona kuti awaopseze kuti asaganize zothaŵa ngakhale pang’ono. Woyang’anira msasawo kenaka anandiopseza ineyo, Maria ndi anawo akuona, amvekere: “Ndikangokupezanso ukulalikira, uphedwa monga taphera aja omwe amafuna kuthaŵa.”

Kenaka, mu November 1966, tinaikidwa ku ndende imene kunali kufera anthu kwambiri yotchedwa São Nicolau. Pamene tinafika kumeneko, ndinagwidwa nthumanzi nditaona kuti amene amayang’anira msasa umenewo anali Cid, mkulu amene ku ndende ya São Paulo anandimenya mwakuti ndife! Anthu ambiri anali kuphedwa mwezi uliwonse, ndipo banja langa linali kukakamizidwa kuonerera kupha anthu kwa nkhalwe kumeneku. Chifukwa cha zimenezi Maria anasokonezeka mutu ndipo mpaka lero sali bwino kwenikweni. M’kupita kwa nthaŵi ndinapeza chilolezo kuti iye pamodzi ndi ana athu apite ku Luanda, kumene ana anga aakazi aakulupo, Teresa ndi Joana, anakawasamalira.

Ufulu, Koma N’kumangidwanso

Ndinatulutsidwa chaka chotsatira, mu September 1970, ndipo ndinapezananso ndi banja langa ndi abale onse ku Luanda. Ndinatuluka misozi kuona mmene ntchito ya kulalikira inapitira patsogolo pa zaka zisanu ndi zinayi zimene ine kunalibe. Pamene ndinatengedwa kupita ku ndende mu 1961, mpingo wa ku Luanda unali ndi magulu anayi ang’onoang’ono. Koma panthaŵiyi kunali mipingo inayi ikuluikulu yokhala ndi dongosolo labwino ndiponso inali kuthandizidwa miyezi isanu ndi umodzi uliwonse ndi woimira woyendayenda wa gulu la Yehova. Ndinali wosangalala kwambiri kuti ndinamasulidwa, koma ufulu wanga sunakhalitse.

Tsiku lina mkulu wa gulu la apolisi limene tsopano limatchedwa Police for Investigation and Defense of the State (PIDE) anandiitana. Atandinyengerera, mwana wanga wamkazi Joana akuona, anandipatsa chikalata chakuti ndisayine. Munalembedwa ntchito zosiyanasiyana zokhudza kukhala kazitape wa PIDE ndiponso malonjezo a mapindu a zachuma ambiri amene ndingapeze ngati nditachita ntchito imeneyo. Nditakana kusayina, ndinaopsezedwa kuti ndidzabwezeredwa ku São Nicolau, kumene ndinauzidwa kuti sindidzatulutsidwanso.

Mu January 1971, patangotha miyezi inayi yokha ndili pa ufulu, nkhani yoopsayi inachitidwadi. Onse pamodzi, analipo akulu achikristu 37 ochokera ku Luanda ndipo anatumizidwa ku São Nicolau. Kumeneko tinali m’ndende mpaka mu August 1973.

Kumasulidwa, Komabe N’kumazunzidwa

Mu 1974 ufulu wachipembedzo unaperekedwa ku Portugal, ndipo pambuyo pake ufulu umenewu unafalikira kumayiko ena olamulidwa ndi dziko la Portugal. Pa November 11, 1975, dziko la Angola linalandira ufulu wodzilamulira kuchoka ku dziko la Portugal. Zinali zosangalatsa kwambiri kwa ife pamene m’March chaka chomwechi tinakhala ndi misonkhano yathu yadera yoyamba mwaufulu! Ndinapatsidwa mwayi wokamba nkhani yapoyera pa misonkhano yosangalatsa imeneyi pa bwalo la maseŵera la Sports Citadel ku Luanda.

Komabe, boma latsopanolo linali kudana ndi kusaloŵerera kwathu pandale. Ndipo nkhondo yachiŵeniŵeni inapitirira mu Angola yense. Zinthu zinafika povuta kwambiri motero Mboni zachizungu zinakakamizidwa kuthaŵa m’dzikomo. Abale atatu amene tinali akomweko tinaikidwa kukhala oyang’anira ntchito ya kulalikira ku Angola, motsogozedwa ndi nthambi ya ku Portugal ya Mboni za Yehova.

Posachedwa dzina langa linayamba kutuluka m’manyuzipepala ndipo linali kulengezedwa pawailesi. Amanena kuti ndinali woimira olamulira a mayiko akunja ndi kuti ndine amene ndikupangitsa kuti Mboni za ku Angola zizikana kuloŵa nawo nkhondo. Chifukwa cha zimenezi, ndinaitanidwa kuti ndikaonekere kwa bwanamkubwa wamkulu kwambiri wa chigawo cha Luanda. Mwaulemu, ndinamulongosolera kuti Mboni za Yehova pa dziko lonse lapansi siziloŵerera m’ndale, ndipo kuti zimenezi ndi zimene atsatiri ake oyamba a Yesu Kristu anali kuchita. (Yesaya 2:4; Mateyu 26:52) Nditamuuza kuti ndinali nditakhala zaka zopitirira 17 m’ndende m’nthaŵi ya ulamuliro wa atsamunda, iye anaganiza zakuti asandimange.

Masiku amenewo, pamafunika kulimba mtima kuti munthu ukhale Mboni ya Yehova ku Angola. Chifukwa chakuti nyumba yanga anali kuizonda, tinasiya kuigwiritsa ntchito pochita misonkhano. Koma monga mmene mtumwi Paulo ananenera, ‘tinali osautsika monsemo, koma osapsinjika.’ (2 Akorinto 4:8) Sitinafookepo mu utumiki wathu. Ndinapitirizabe ntchito ya kulalikira, kutumikira monga mtumiki woyendayenda ndi kulimbikitsa mipingo m’zigawo za Benguela, Huíla, ndi Huambo. Pa nthaŵi imeneyo ndinali kudziŵika ndi dzina lina, Mbale Filemon.

Mu March 1978 ntchito yathu yolalikira inatsekedwanso, ndipo anthu odalirika anandiuza kuti anthu ena otengeka maganizo pa kusintha zinthu akupangana zakuti andiphe. Choncho ndinakabisala m’nyumba ya wa Mboni wina wa ku Nigeria amene anali kugwira ntchito ku ofesi ya kazembe wa ku Nigeria ku Angola. Patatha mwezi, zinthu zitasintha, ndinapitiriza kutumikira abale monga woyang’anira dera.

Ngakhale kuti panali kuletsa komanso nkhondo, anthu zikwizikwi a ku Angola anamvetsera ulaliki wathu. Chifukwa cha kuchuluka kwa anthu amene anali kukhala Mboni, komiti ya dziko inaikidwa kuti isamalire ntchito ya kulalikira ku Angola, moyang’aniridwa ndi nthambi ya dziko la Portugal. Nthaŵi imeneyi, ndinayenda maulendo angapo kupita ku Portugal, kumene atumiki odziŵa bwino anali kundiphunzitsa zinthu zofunika kwambiri, ndiponso ndinali kulandira chithandizo cha mankhwala.

Potsiriza Pake Tinapeza Ufulu Wakulalikira!

Pamene ndinali ku misasa yachilango, akaidi a zandale anali kundiseka n’kumanena kuti sindidzamasulidwa ngati nditi ndipitirize kulalikira. Koma ndinali kuwayankha kuti: “Nthaŵi sinakwane yakuti Yehova atsekule chitseko, koma akadzatero, palibe munthu amene adzachitseke.” (1 Akorinto 16:9; Chivumbulutso 3:8) Chitseko cha mwayi wolalikira popanda kuletsedwa chimenecho chinatseguka pululu pambuyo pa kugaŵanika kwa dziko la Soviet Union mu 1991. Kuyambira pamenepa tinayamba kukhala ndi ufulu wa kulambira wochulukirapo ku Angola. Mu 1992 ntchito ya Mboni za Yehova inakhazikitsidwa mwalamulo. Ndipo potsiriza pake mu 1996 nthambi ya Mboni za Yehova inakhazikitsidwa ku Angola ndipo ine ndinasankhidwa kukhala m’Komiti ya Nthambiyo.

Kwa zaka zambiri zimene ndinakhala m’ndende, banja langa lakhalabe likusamalidwa mwa njira inayake. Tinali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo asanu adakali ndi moyo. Mwana wathu wokondedwa Joana anamwalira chaka chatha ndi matenda a kansa. Ana athu anayi pano ndi Mboni zobatizidwa, koma mwana wathu winayo sanabatizidwebe.

Pamene Mbale Cooke anatiyendera mu 1955, panali anthu a ku Angola anayi amene anali kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Lero m’dzikoli muli ofalitsa Ufumu oposa 38,000, ndipo akuchititsa maphunziro a Baibulo oposa 67,000 mwezi uliwonse. Ena mwa amene akulalikira uthenga wabwino ndi anthu amene poyamba anali kutizunza. Imeneyitu ndi mphotho yaikulu kwambiri, ndipo ndine woyamikiradi kwa Yehova chifukwa chondisunga ndi kundilola kuti ndikwaniritse chikhumbo changa chachikulu cha kufalitsa mawu ake!—Yesaya 43:12; Mateyu 24:14.

[Mapu patsamba 20, 21]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Democratic Republic of Congo

Kinshasa

Angola

Maquela do Zombo

Luanda

São Nicolau (pano akuti Bentiaba)

Moçâmedes (pano akuti Namibe)

Baia dos Tigres

Serpa Pinto (pano akuti Menongue)

[Mawu a Chithunzi]

Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.

[Zithunzi pamasamba 22, 23]

M’munsi: Ndili ndi John Cooke mu 1955. Sala Filemon ndi uyo ali kumanzere

Kumanja: Kukumananso ndi John Cooke patatha zaka 42

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi mkazi wanga, Maria

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena