Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 11/8 tsamba 32
  • Mayiko a India ndi China Akuwonongedwa ndi Fodya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mayiko a India ndi China Akuwonongedwa ndi Fodya
  • Galamukani!—1999
Galamukani!—1999
g99 11/8 tsamba 32

Mayiko a India ndi China Akuwonongedwa ndi Fodya

YOSIMBIDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU INDIA

M’MAYIKO a Kumadzulo, kuwonjezeka kwa kuletsa kunenerera fodya ndi kuphunzitsa anthu za mmene kusuta kumawonongera thanzi, kwachititsa makampani a fodya akuluakulu kutembenukira ku mayiko a Kummaŵa kuti agulitse fodya wawoyo. Kufufuza kumene kunachitika mothandizidwa ndi Banki Lalikulu la Padziko lonse kunaonetsa kuti mwina pofika chaka cha 2010 anthu amene akufa chifukwa cha kusuta fodya ku China angadzafike pa 1 miliyoni pachaka. Magazini yotchedwa British Medical Journal inanena kuti anthu 100 miliyoni a ku China osafika zaka 29 adzafa chifukwa chosuta fodya.

Bungwe la zaumoyo padziko lonse la World Health Organization likutsimikizira kuti, dziko la China, komanso la India, limene lili ndi anthu pafupifupi 1 biliyoni, likhala ndi “matenda ambiri ndiponso ofala mwamsanga obwera chifukwa cha fodya.” Malipoti amati kumeneko, pafupifupi ana 20 miliyoni amayamba kusuta chaka chilichonse. Kwa zaka zambiri, munthu wina wa Kummwera kwa India sanali kuchotsa fodya pakamwa. Analemba kalata kwa ofalitsa a Galamukani! pothokoza chifukwa cha nkhani ya m’magaziniwa imene inamuthandiza kusiyiratu kusuta. Inali nkhani yakuti “Mutha Kusiya—Ifenso Tinasiya!” imene inatuluka m’kope la December 8, 1998.

Kodi n’zifukwa zotani zimene munganenere kuti muyenera kusiya kusuta fodya? Zifukwa zina zofunika kuziganizira zili patsamba 25 la bulosha lamasamba 32 lotchedwa Kodi Mulungu Amafunanji Kwa Ife? Mungaitanitse yanu polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi yasonyezedwayo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ano.

□ Nditumizireni bulosha la Kodi Mulungu Amafunanji Kwa Ife?

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulele.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena