Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g99 12/8 tsamba 32
  • Wosakhulupirira Mulungu Apeza Mayankho

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wosakhulupirira Mulungu Apeza Mayankho
  • Galamukani!—1999
Galamukani!—1999
g99 12/8 tsamba 32

Wosakhulupirira Mulungu Apeza Mayankho

“NKHANI zofalitsidwa m’magazini anu a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! n’zabwino bwanji! Makope anu a posachedwapa sungathe kungowayang’ana chabe! Amayankha mafunso ambiri ndipo amapereka mtendere wa mumtima.”

Zimenezi n’zimene ananena woŵerenga wina wa kummwera kwa India. Iye ndi Mhindu, koma pomulera bambo ake anam’phunzitsa kukhala wosakhulupirira Mulungu. Iye anati: “Sindinapeze cholinga cha moyo. Chiphunzitso cha Darwin cha chisinthiko chinali chosamveka. Mafunso onga akuti Kodi Mulungu ndani? Kodi n’chifukwa chiyani dzikoli lili loipa? Kodi timapita kuti tikafa? Kodi mizimu ilikodi? Akhala akundisautsa kwa zaka zambiri.

Atapeza mayankho a mafunso ake kuchokera m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, woŵerenga ameneyu analembetsa magazini onse aŵiri ndiponso analembetsa magazini ena a mlongo wake monga mphatso, ndipo tsopano amagaŵira magaziniŵa kwa anthu amene wakumana nawo. Pokhala kuti iye ndi wotola zithunzi komanso waluso lojambula zinthu pamanja, amayamikira zithunzi za m’maganizi ameneŵa zimene “zimalankhula zokha.” Mwa kuŵerenga magazini abwinoŵa, mungakhale m’modzi wa anthu miyandamiyanda padziko lonse amene mafunso awo anayankhidwa ndipo anapeza mtendere wa mumtima.

Ngati mungafune kudziŵa zambiri ponena za Mulungu ndi chifuno chake kwa ife, tidzakhala okondwa kukutumizirani kwaulere bulosha lomwe lagaŵiridwa konsekonse lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi? Ingolembani zofunika pa silipi lotsatirali ndipo tumizani ku adiresi yosonyezedwa pamenepo kapena ku adiresi yoyenera pa maadiresi osonyezedwa patsamba 5 la magazini ano.

□ Nditumizireni kope la bulosha lakuti Kodi Mulungu Amatisa- maliradi? Lembani chiyankhulidwe chimene mukufuna.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

CHIKUTO, Masamba 2-9 ndi 32: Einstein: U.S National Archives photo; Galimoto ya Ford ya mtundu wotchedwa Model-T: Kuchokera m’mabuku a Henry Ford Museum & Greenfield Village; Kugwa kwa Chuma Kwakukulu: Dorothea Lange, FSA Collection, Library of Congress; Mfumu Nicholas II ndi banja lake: Kuchokera m’buku lakuti Liberty’s Victorious Conflict; Nyumba ya League of Nations: U.S. National Archives photo; Churchill: The Trustees of the Imperial War Museum (MH 26392); Sitima ya Nkhondo: U.S. Navy photo; Mabomba a Atomu: USAF photo; Gandhi: Culver Pictures; Munthu ali pamwezi: NASA photo; Kuwononga Mpweya: Godo-Foto; Mao Tse-tung: Culver Pictures; Ana a ku Africa: FAO photo/F. Botts; Chifanizo cha Lenin: Juraatis/Sipa Press; Chombo Chouluka: NASA photo; Archduke Ferdinand: Kuchokera m’buku lakuti The War of the Nations; Lenin: Musée d’Histoire Contemporaine-BDIC

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena