Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g02 4/8 tsamba 32
  • Ankangowayang’ana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ankangowayang’ana
  • Galamukani!—2002
Galamukani!—2002
g02 4/8 tsamba 32

Ankangowayang’ana

ANYAMATA aŵiri anaima pa lesitilanti inayake kuti adye chakudya chammaŵa m’tauni ina yaing’ono ku Ohio, m’dziko la United States. Mwachizoloŵezi chawo, asanayambe kudya anaŵeramitsa mitu yawo n’kupemphera chamumtima.

Atamaliza kupemphera, mzimayi wina amene ankangowayang’ana anapita patebulo pamene anakhala n’kutenga tikiti yosonyeza ndalama zimene ayenera kulipira pa chakudyacho. Iye anawauza kuti: “Masiku ano timamva zoipa zambiri zokhudza achinyamata padzikoli, motero n’zosangalatsa kwambiri kuona anyamata aŵirinu mukuganiza zoyamba kaye mwathokoza Mulungu musanayambe kudya. Basi chakudya chanuchi ndilipira ndiineyo.”

Anyamatawo anasoŵa chonena komabe anam’thokoza mayiyo. Kenaka anaganiza kuti sibwino kuti mayiyo aziganiza kuti iwo ankangopemphera kwa Mulungu wamba. Motero mnyamata mmodziyo anapita pomwe panali mzimayiyo n’kumuthokozanso kenaka n’kumufotokozera kuti iwo ndi Mboni za Yehova.

Mboni za Yehova zili ndi chizoloŵezi chophunzira Baibulo ndi mabanja awo ndipo zimenezi n’zimene makolo a anyamataŵa anachita. Buku limodzi limene mabanjaŵa anaphunzira ndi lotchedwa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. M’bukuli muli mitu yokwana 19, ndipo mutu wina wakuti: “Mmene Mungayandikirire Kwa Mulungu,” umanena za pemphero.

Mungaitanitse buku la masamba 192 limeneli lomwe limathandiza pophunzira Baibulo polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Nditumizireni buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena