Linapangidwadi Mwaluso
Diso la Njuchi
◼ Pulofesa Luke Lee, wa pa yunivesite ya California, ku United States, anati: “Kapangidwe kake n’kogometsa kwambiri.” Pulofesayu anali kufotokoza za diso la tizilombo ngati njuchi.
Taganizirani izi: Diso la tizilombo tina monga njuchi ndi tombolombo limatha kuona kutsogolo, kumbuyo ndiponso m’mbali pa nthawi imodzi. Disoli limatha kulumikiza zithunzi zosiyanasiyana zimene likuonazo moti limaona zinthu zambirimbiri panthawi imodzi.
Asayansi akufufuza njira zowathandiza kupanga makamera m’njira yotsanzira diso la njuchi. Akufunanso kuti makamerawa akhale amphamvu kwambiri, aang’ono zedi komanso otha kujambula mbali zonse. Makamerawa angathe kuwagwiritsa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, madokotala angathe kuwagwiritsa ntchito pounikira m’mimba mwa munthu. Akuti makamera otere adzakhala “aang’ono kwambiri” moti wodwalayo azidzangowameza. Akawameza azidzajambula zithunzi zosiyanasiyana m’mimbamo n’kumazionetsa pa kompyuta.
Gulu lina la akatswiri asayansi lapanga diso lokhala ndi tizipangizo toposa 8,500 tothandiza kuti lizitha kuona zinthu kwambiri. Tizipangizo tambiri chonchi timangokwana malo ochepa zedi ngati kansonga ka singano. Ngakhale kuti anthu atulukira luso la pamwamba chonchi, diso la njuchi komanso la tizilombo tina totere linapangidwa mogometsa kwambiri. Mwachitsanzo, diso la tombolombo lili ndi tizigawo pafupifupi 30,000 timene timalithandiza kuti liziona patali.
Ndiye kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi diso lopangidwa mwaluso chonchi linangokhalapo lokha kapena linachita kulengedwa?
[Chithunzi patsamba 26]
Kachigawo kadiso la njuchi kamaoneka chonchi pa makina oonera zinthu zing’onozing’ono
[Mawu a Chithunzi patsamba 26]
Background: © Stephen Dalton/Photo Researchers, Inc.; close-up: © Raul Gonzalez Perez/Photo Researchers, Inc.