Khalani ndi Diso la Kumodzi
1. Kodi kukhala ndi diso la kumodzi kumatanthauza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani kuli kofunika?
1 Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anafotokoza mmene diso lophiphiritsira kapena lauzimu lingakhudzire moyo wathu. Iye anati: “Chifukwa chake ngati diso lako lili la kumodzi, thupi lako lonse lidzakhala loŵalitsidwa. Koma ngati diso lako lili loipa, thupi lako lonse lidzakhala lodetsedwa.” (Mat. 6:22, 23) Diso la kumodzi ndi limene limayang’ana pa cholinga chimodzi—kuchita chifuno cha Mulungu—popanda kusokonezeka ndi nkhaŵa yopitirira muyeso ya zinthu zakuthupi. (Mat. 6:19-21, 24-33) Kodi n’chiyani chimene chingatithandize kukhala ndi diso la kumodzi?
2. Kodi Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tiyenera kuona zinthu za kuthupi motani?
2 Kukhala Okhutira: Kupezera banja zofunika pamoyo ndi udindo wa m’Malemba umene munthu ali nawo. (1 Tim. 5:8) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tifunika kumka tifunafuna zinthu zapamwamba kapena zinthu zatsopano zimene zangotuluka kumene. (Miy. 27:20; 30:8, 9) M’malo mwake, Malemba amatilimbikitsa kukhala okhutira ndi zinthu zofunika kwambiri pamoyo monga “zakudya ndi zofunda.” (1 Tim. 6:8; Aheb. 13:5, 6) Kumvera langizo limeneli kungatithandize kuti tiziona zinthu m’njira yoyenera.
3. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tipeŵe kudzilemetsa tokha?
3 Tingachite bwino kupeŵa kudzilemetsa ndi ngongole zosafunikira ndi chuma kapena ntchito zimene zingafunikire nthaŵi yambiri ndi chisamaliro chochuluka. (1 Tim. 6:9, 10) Kodi tingachite chiyani kuti tipeŵe zimenezi? Ngati tikufuna kuchita zinazake, tiziyamba tapemphera mofatsa za nkhaniyo ndi kupenda moona mtima ngati kuchita zimenezo sikudzasokoneza ntchito zathu zauzimu. Ndiyetu yesetsani kuika zinthu zauzimu pa malo oyamba m’moyo wanu.—Afil. 1:10; 4:6, 7.
4. N’chifukwa chiyani tifunika kupeza njira zokhalira ndi moyo wosafuna zambiri?
4 Khalani ndi Moyo Wosafuna Zambiri: Njira ina imene ingatithandize kupeŵa kukonda chuma ndiyo kuyesetsa kupeza njira zimene tingakhalire ndi moyo wosafuna zambiri. Mbale wina amene anaona kuti banja lake likhoza kukhala bwinobwino popanda zinthu zina zakuthupi zosafunikira kwenikweni anati: “Panopa ndimatha kuchita zinthu zambiri mu mpingo kutumikira abale anga. Ndakhulupirira kuti Yehova amadalitsa atumiki ake onse akamaika kulambira koona patsogolo pa zofuna zawo.” Kodi inunso mungakonde kupeza madalitso ochuluka mwa kukhala ndi moyo wosafuna zambiri?
5. N’chifukwa chiyani tifunika kuchita khama kuti tikhale ndi diso la kumodzi?
5 Kuchita khama n’kofunika kwambiri kuti tithe kulimbana ndi mphamvu ya Satana, dziko lake lokonda chumali, ndi kupanda ungwiro kumene tili nako. M’malo molola maso athu kuyang’ana uku ndi uku, tiyeni tiwalunjikitse pa kuchita chifuniro cha Mulungu ndi pa chiyembekezo chathu chamtengo wapatali cha moyo wosatha.—Miy. 4:25; 2 Akor. 4:18.