Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 9/04 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira September 13
  • Mlungu Woyambira September 20
  • Mlungu Woyambira September 27
  • Mlungu woyambira October 4
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 9/04 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira September 13

Nyimbo Na. 43

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Ngati mfundo zimene zili pa tsamba 4 zingathandize m’gawo la mpingo wanu, zigwiritseni ntchito posonyeza chitsanzo cha mmene tingagaŵirire Nsanja ya Olonda ya September 15 ndi Galamukani! ya October 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena. Pambuyo pa chitsanzo chilichonse tchulani mfundo imene ili yothandiza m’chitsanzocho. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 15: “Khalani ndi Diso la Kumodzi.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwa. Ngati nthaŵi ilipo, kambiranani malemba osagwidwa mawu.

Mph. 18: Zimene Amanena Amene Amaona Ntchito Zathu Zabwino. (1 Pet. 2:12) Nkhani ndi kukambirana ndi omvera yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2002, masamba 12 mpaka 14, ndime 14 mpaka 20. Pemphani omvera kupereka ndemanga zokhudza mmene ntchito zathu zabwino zakhudzira anthu amene amaziona m’dera lanu.

Nyimbo Na. 162 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 20

Nyimbo Na. 88

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kambani mfundo zikuluzikulu za m’kalata yochokera ku nthambi yomwe ili patsamba loyambirira la Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Limbikitsani onse kuŵerenga Numeri 16:1-35 pokonzekera Msonkhano wa Utumiki wa mlungu wa October 4.

Mph. 15: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Nkhani yokambidwa ndi mkulu yozikidwa pa lipoti la mpingo la chaka cha utumiki cha 2004. Kambani kwambiri mbali zolimbikitsa za lipotilo ndipo yamikirani anthu mumpingowo chifukwa cha ntchito yabwino imene anachita. Fotokozaninso za ntchito yaikulu imene apainiya achita. Tchulani mbali imodzi kapena ziŵiri zimene mpingo ungafunikire kugwirirapo ntchito chaka chamaŵa.

Mph. 20: Timadziŵika Chifukwa cha Ukhondo wa Pathupi ndi Panyumba. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 2002, masamba 19 mpaka 21. Phatikizanipo chitsanzo cha mkulu akusonyeza wofalitsa mmene angathandizire wophunzira Baibulo mwanzeru kuti aone kufunika kosunga m’nyumba ndi panja pali paukhondo. Agwiritse ntchito phunziro 9, ndime 5, m’bulosha la Mulungu Amafunanji.

Nyimbo Na. 103 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 27

Nyimbo Na. 221

Mph. 15: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a September. Sonyezani chitsanzo cha mmene tingagaŵirire Nsanja ya Olonda ya October 1 ndi Galamukani! ya October 8. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 10: Mawu a Yehova Ndi Amoyo. Nkhani. Kuti tipindule mokwanira bwino ndi pulogalamu yoŵerenga Baibulo mlungu ndi mlungu m’Sukulu ya Utumiki, nkhani za mutu wakuti “Mawu a Yehova Ndi Amoyo” zayamba kuikidwa m’magazini ena a Nsanja ya Olonda. Mwa kugwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ya September 15, 2004, masamba 24 mpaka 27, fotokozani mbali zina ndi zina za nkhani zimenezi. Pambuyo pofotokoza mwachidule zimene zili m’nkhaniyo, mbali yakuti “Kuyankha Mafunso a M’Malemba” ikufotokoza mbali zina za m’Malemba zimene zili zovuta. Ndemanga za pakamutu kakuti “Zimene Tikuphunzirapo” zikusonyeza phindu lake la zimene taŵerenga. Fotokozani zitsanzo zochepa chabe kuti musonyeze mmene nkhani zimenezi zitithandizire kumvetsa mozama Mawu a Mulungu. Limbikitsani onse kugwiritsa ntchito thandizo latsopano limeneli pamene tikuyamba kuŵerenga buku la Deuteronomo mlungu wamaŵa.

Mph. 20: “Gwiritsani Ntchito Bwino Baibulo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. M’mawu anu oyamba, gwiritsani ntchito ndemanga zopezeka m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 145, ndime 2 ndi 3. Phatikizanipo zitsanzo ziŵiri zachidule, chimodzi chosonyeza ulendo woyamba ndipo chinacho ulendo wobwereza, kuonetsa mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zimene zaperekedwazo.

Nyimbo Na. 38 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu woyambira October 4

Nyimbo Na. 5

Mph. 5: Zilengezo za pampingo.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 25: “Tiyenera Kulemekeza Ulamuliro wa Yehova.” Ŵerengani Yuda 11, kambani mawu oyamba osakwana mphindi ziŵiri. Ndiyeno kambiranani ndi omvera pogwiritsa ntchito mafunso onse amene aperekedwa m’nkhaniyo. Tsindikani mfundo yakuti ngati tikufuna kuyanjidwa ndi Yehova, tiyenera kupeŵa mzimu wopanduka wa Kora ndi kutsatira chitsanzo cha ana ake amene sanalole chilichonse kukhala choyamba m’malo mwa kukhulupirika kwawo kwa Yehova.

Nyimbo Na. 99 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena