Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/08 tsamba 26
  • Mapazi a Nalimata

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mapazi a Nalimata
  • Galamukani!—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru za Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Zamoyo Zimatiphunzitsa Chiyani?
    Galamukani!—2006
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2008
  • Kodi Ndi Ndani Anayamba Kuzipanga?
    Kodi Zamoyo Zinachita Kulengedwa?
Onani Zambiri
Galamukani!—2008
g 4/08 tsamba 26

Analengedwa Mwaluso

Mapazi a Nalimata

◼ Asayansi amachita chidwi kwambiri ndi luso la nalimata lotha kuyenda bwinobwino pakhoma kapena kudenga lanyumba koma osagwa. Kodi buluzi waluso lodabwitsali amatha bwanji zimenezi?

Baibulo limati buluzi “amagwira ndi manja ake.” (Miyambo 30:28, NW) Mapazi a nalimata ali ngati manja, ndipo amathandiza kuti nalimata aziyenda bwinobwino pa malo a see. Chala chilichonse cha nalimata chimakhala chokakala ndipo chimakhala ndi titsitsi tambirimbiri. Katsitsi kalikonse kali ndi timphanda tambirimbiri tosaoneka ndi maso athu. Timphanda timeneti tili ndi mphamvu zomata zimene zimathandiza kuti nalimatayo azitha kuyenda bwinobwino pakhoma, kudenga, ngakhalenso pa galasi koma osagwa.

Ofufuza akufuna kupanga zomatira zogwira ntchito ngati mapazi a nalimata, kuti zizitha kumatirira ngakhale pa zinthu zosalala.a Magazini ina inati: “Mwa zina, zomatirazi angathe kumazigwiritsira ntchito kuchipatala. Mwachitsanzo, angathe kupangira mabandeji otha kumata ngakhale atanyowa. Angathenso kupangira zinthu zina zomatira pachilonda m’malo mosokapo.”—Science News.

Mfundo zochepa zimene taonazi zikusonyeza kuti nalimata analengedwadi mwaluso n’chifukwa chake amatha kuchita zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

a Asayansi akufufuzanso mitundu ina ya nkhanu zimene zimatulutsa timadzi tonanda, tothandiza kuti nkhanuzi zizitha kumamatira ku zinthu zosiyanasiyana m’madzi.

[Chithunzi patsamba 26]

Mmene nalimata amaonekera kumimba kwake

[Chithunzi patsamba 26]

Titsitsi tosaoneka ndi maso ta m’mapazi a nalimata

[Mawu a Chithunzi patsamba 26]

Gecko: Breck P. Kent; close-up: © Susumu Nishinaga/Photo Researchers, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena