Chulu cha Chiswe
Chimapangidwadi Mwaluso
◼ Anthu amati chulu cha chiswe n’chodabwitsa kwambiri ndipo zimenezi n’zomveka. Chuluchi chimamangidwa ndi dothi komanso malovu a chiswe, ndipo chimatha kutalika mamita 6. Khoma lake limakhala lokhuthala masentimita 45. Ndipo dzuwa likaomba khomalo limauma ngati lamangidwa ndi simenti. Zulu zina zimamangidwa usiku umodzi wokha.
Pakatikati pa chulucho pamakhala makechiswe amene amaikira mazira ambirimbiri tsiku lililonse. Kenako mtundu wina wa chiswe chosaona komanso chopanda mapiko umatenga mazirawo n’kupita nawo malo oyenera. Chiswechi chimayang’anira mazirawo mpaka adzaswe. Komabe, chodabwitsa kwambiri ndi mmene mpweya umayendera mkati mwa chulu.
Taganizirani izi: Chimakhala ndi mauna ena amene amachititsa kuti mkati mwake musamatenthe kwambiri kapena kuzizira kwambiri nyengo yakunja ikasintha. Mwachitsanzo, m’dziko la Zimbabwe nyengo imatha kusintha kwambiri. Usiku kumatha kuzizira mpaka madigiri seshasi awiri pamene masana kumatha kutentha kufika madigiri seshasi 38. Koma mkati mwa chulu simusintha. Nthawi zonse mumakhala motentha madigiri seshasi 31. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?
Mpweya wozizira umalowera m’mauna a pansi ndipo wotentha umatulukira pamwamba. Mpweya wozizirawo ukalowa umazungulira mkati monsemo. Ndiyeno chiswe chimatsegula kenako n’kutseka maunawo malinga ndi mmene nyengo ilili kunja. Zimenezi zimathandiza kuti mkatimo musatenthe kwambiri kapena kuzizira kwambiri kuti muzimera mtundu winawake wa bowa amene chiswecho chimadya.
Anthu amachita chidwi kwambiri ndi mmene mpweya umayendera mkati mwa chulu moti pomanga nyumba ina ya maofesi ku Zimbabwe anatengera pulani ya chulu cha chiswe. Nyumba imeneyi imagwiritsa ntchito magetsi ochepa kwambiri pofuna kutenthetsa kapena kuziziritsa zipinda zake.
Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi chiswe chimene chimatha kukonza chulu choterechi chinangokhalako chokha, kapena chinachita kulengedwa?
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
Top: Stockbyte/Getty Images; bottom: Scott Bauer/Agricultural Research Service, USDA