Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 6/8 tsamba 17-18
  • Chiswe Bwenzi Kapena Mdani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chiswe Bwenzi Kapena Mdani?
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Linga la Chiswe
  • Chikhalidwe cha Chiswe
  • Mabwenzi Kapena Adani?
  • Chulu cha Chiswe
    Galamukani!—2008
  • Ndiwo Zokoma Zomwe Sitidzaziiwala
    Galamukani!—2012
Galamukani!—1995
g95 6/8 tsamba 17-18

Chiswe Bwenzi Kapena Mdani?

NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! MU KENYA

“KUMBE! Mchwa!” Anafuula motero mtumiki wina Wachikristu pamene iye ndi ena ananyamula dziŵe lamatabwa lonyamulika. Iwo anafuna kuligwiritsira ntchito monga dziŵe lobatizira pamsonkhano wadera wa Mboni za Yehova ku Kenya. Komabe, anadabwa pamene anapeza kuti mbali yaikulu ya thabwalo inadyedwa. Nchifukwa chake ananena mawu okhumudwa. Atatembenuzidwa, mawuwo amatanthauza kuti: “O-oo! Chiswe!”

Mwinamwake palibe kachilombo kena kamene kaŵirikaŵiri kamawononga zinthu ngati chiswe chaching’onocho. Koma kodi kachilombo kameneka kalidi mdani wa munthu? Kuti tiyankhe, tiyeni tipende chiswe mosamalitsa.

Linga la Chiswe

Ku Kenya, anthu nthaŵi zambiri amaona nyumba zazitali za chiswe. Zimenezi ndi zinthu zonga chumuni zimene zimatalika mamita asanu mpaka asanu ndi imodzi kuchokera pansi. Zuluzo, zofanana ndi mphala yakonkire, zimamangidwa mwaluso kwambiri kwakuti chiswe chatchedwa akatswiri omanga. Kodi sitimadabwa polingalira kuti tizilombo tating’onong’ono timeneto timamanga nsanja zazitali zoterozo zochititsa chidwi, ngakhale kuti timayenda pang’onopang’ono—ndipo ntakhungu?

Mkati mwa chulucho muli zipinda ndi njira zambimbiri. Mzinda wapiringupiringu umenewu ulinso ndi ngalande, moloŵera mphepo, ndiponso zoziziritsa zokwanira. Mpweya wotentha umatulukira pamwamba pa chulu kudzera m’timaenje. Mpweya wozizira umaloŵera pansi. Kuziziritsa kwina kumachitika mwa njira yapafupi ya kukamuka kwa chinyontho: Chiswecho chimawaza makoma awo madzi mwa kuwalavulira. Pamene madziwo akamuka, amaziziritsa mpweya umene umathandiza chiswe chonsecho. Chifukwa chake nyumba ya chiswe imakhalabe ndi tempichala yabwino ya 30 digiri Celsius maola 24 patsiku!

Chikhalidwe cha Chiswe

Chodabwitsanso kwambiri ndicho chikhalidwe cha chiswe. Zulu zina zili ndi midzi, kapena zisa zadongosolo, zokhala ndi nzika pafupifupi mamiliyoni asanu. M’malo mokhala chachipolowe, chisa chimodzi chili chitsanzo chabwino cha dongosolo. Banja la chiswe lili ndi mitundu itatu, ndiko kuti, antchito, asilikali, ndi obala. Antchito ndiwo amamanga zulu, akumagwiritsira ntchito malovu awo monga simenti.

Asilikali ndiwo oipa kwambiri m’banjamo. Pokhala ndi mbanwa ndi mano awo akuthwa monga zida zawo, iwo amadikirira lingalo kuletsa adani, onga linthumbu. Amachitanso ulonda kutetezera antchito pamene atuluka kunja kwa chulu kukafuna chakudya. Patakhala kufunikira, asilikaliwo amathira nkhondo yamankhwala; anabere awo apadera amagwira ntchito ngati kamfuti kamadzi, akumatulutsa madzi aululu wakupha.

Kodi asilikaliwo amalipidwa bwanji pa mautumiki awo? Eya, mbanwa zawo zichita ngati kuti nzazikulu kwambiri kwakuti iwo sakhoza kutafuna chakudya chawo. Chotero msilikali akamva njala, iye amangokhudza mutu wa wantchito ndi nyanga zake. Mwakutero amakhala akunena kuti, “Tandidyetsa!” Wantchito amachita zimenezo mwa kuika chakudya chobzikula m’kamwa mwa msilikaliyo.

M’chipinda cha chimake cha chiswe, chimene chili mumdima wandiwe yani, mumakhala obala—mwamuna ndi mmanthu wachulu. Mmanthu wachuluyo ngwamkulu kwambiri kuposa mwamuna wake wamng’onoyo. Mimba yake, yokhuta mazira, ili umboni wa mphamvu zake zazikulu zakubala. Kwanenedwa kuti patsiku angaikire mazira kuyambira pa 4,000 mpaka 10,000. Nchifukwa chake ena atcha mmanthu wachuluyo “makina aotomatiki oikira mazira.”

Komabe, makolo a chiswe amenewo alibe nthaŵi yambiri ya kukhala paokha pakuti amatumikiridwa ndi gulu la antchito la chiswe. Ameneŵa amazinga mmanthuyo, akumasamalira zofuna zake zamwamsanga ndi kumpatsa chakudya. Pamene aikira mazira, antchitowo amawanyamula ndi mbanwa zawo kupita nawo kuchipinda choswera.

Mabwenzi Kapena Adani?

Pamene kuli kwakuti ndi anthu oŵerengeka amene angakane kuti tizilombo timeneti ntochititsa chidwi, ochuluka amatiyesabe tilombo towononga—adani! Dr. Richard Bagine, mkulu wa Invertebrate Zoology Department of the National Museum ya Kenya, anauza Galamukani! kuti: “Nzoona kuti anthu amaona chiswe monga gulu la tilombo tosakaza zinthu koposa. Koma asayansi amaona chiswe mosiyana nawo. Kuthengo, chiswe chimathandiza kwambiri zomera ndi nyama.

“Choyamba, chimaduladula zomera zakufa kukhala misanganizo wamba. Mwanjira imeneyi, chiswe chimabwezeretsa m’nthaka manyowa amene zomera zifuna. Chachiŵiri, icho ndi chakudya chofunika kwambiri. Chimadyedwa pafupifupi ndi mbalame yamtundu uliwonse ndi nyama zambiri zoyamwitsa, zokwawa, zokhala kumtunda ndi m’madzi, ndi tizilombo tina. Anthu ambiri kumadzulo ndi kumpoto kwa Kenya nawonso amakonda kwambiri kukoma kwake kwambiriko; icho chili ndi mafuta ndi maproteni ambiri. Chachitatu, chimathandizira kupanga dothi. Chiswe chimasanganiza dothi lapansi ndi lapamwamba pomanga ndi pokonza zisa zawo. Chimanyenya zidutswa zazikulu za zomera zakufa kukhala tizidutswa, chikumapanga manyowa. Poyenda m’nthaka, chimapanga tinjira toyendamo mpweya ndi madzi amene mitsitsi ya zomera imafuna. Motero chiswe chimachirikiza mkhalidwe wa nthaka, mpangidwe wake, ndi kubala kwake.”

Komabe, kodi nchifukwa ninji chiswe chimaloŵerera m’malo a anthu? Dr. Bagine akuti: “Kwenikweni, anthu ndiwo asamukira m’madera ake a chiswe nachotsa zomera zochuluka zimene chiswe chimadya. Kuti chikhale ndi moyo chiswe chiyenera kudya, ndipo nthaŵi zambiri chimadya zomera zakufa. Chitalandidwa zimenezi, chiswe chimadya zinthu zopangidwa ndi anthu, monga nyumba ndi nkhokwe.”

Chotero ngakhale kuti chiswe nthaŵi zina chingaoneke kukhala kalombo kowononga zinthu, sichili mdani wathu ayi. Inde, chili umboni wodabwitsa wa nzeru zakulenga za Yehova. (Salmo 148:10, 13; Aroma 1:20) Ndipo m’dziko latsopano la Mulungu likudzalo, pamene munthu adzaphunzira kukhala pamtendere ndi nyama, iye mosakayikira adzafikira pakuona chiswe chaching’onocho monga bwenzi, osati mdani.—Yesaya 65:25.

[Zithunzi patsamba 17]

Chulu cha chiswe chodziŵika chonga nsanja

Chithunzi mkati: Chiswe chantchito

[Chithunzi patsamba 18]

Msilikali wa chiswe, ndi mutu wake waukulu ndi anabere amene amatulutsa mankhwala akupha, ali wokonzeka kutetezera gulu la chiswe

[Chithunzi patsamba 18]

Mmanthu wachulu, mimba yake yotupa ndi mazira

[Chithunzi patsamba 18]

Mmanthu wachulu ndi antchito ake

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena