Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 6/8 tsamba 15-16
  • Mabuku a Baibulo Ayamikiridwa m’Maiko Amene Anali Soviet Union

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabuku a Baibulo Ayamikiridwa m’Maiko Amene Anali Soviet Union
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Magazini Amaonekedwe Okongola Ayamikiridwa
  • Mabuku Ena Oyamikiridwa
  • Anthu a ku Russia Akuyamikira Ufulu wa Kulambira
    Galamukani!—2000
  • Anthu Okonda Mtendere Akuyesetsa Kuti Anthu Asaipitse Mbiri Yawo
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Ulendo Wobwereza wa ku Russia
    Galamukani!—1995
  • Chiwonjezeko Chodabwitsa
    Galamukani!—1992
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 6/8 tsamba 15-16

Mabuku a Baibulo Ayamikiridwa m’Maiko Amene Anali Soviet Union

Ndi mtolankhani wa Galamukani! mu Russia

KUCHIYAMBI kwa 1991 Soviet Union wapanthaŵiyo anapangidwa ndi Russia ndi maboma ena 14. Chiyambire panthaŵiyo, mabomawo akhala maiko odziimira paokha. Komabe, Russia ali ndi anthu ochuluka kuposa maiko 14 enawo kuwaphatikiza pamodzi ndipo alinso ndi nthaka yaikulu kuŵirikiza pamodzi maikowo koposa katatu. Pofika mu September 1994, munali Mboni za Yehova zokwanira 117,276 m’maiko amene anali Soviet Union zimene zinali kulalikira kwa anansi awo ziphunzitso za choonadi cha Baibulo.

Lerolino mitokoma yaikulu ya magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! ikusindikizidwa m’Russia mwezi uliwonse owagwiritsira ntchito m’maiko amene anali Soviet Union. Ndiponso, matrakiti ambiri ndi mabuku achikuto cholimba akugaŵiridwa kumeneko. Mfundo yakuti mabuku a Baibulo ameneŵa ayamikiridwa kwambiri ikuonekera bwino lomwe mwa makalata olandiridwa ku ofesi ya Mboni za Yehova ya Russia pafupi ndi St. Petersburg.

Magazini Amaonekedwe Okongola Ayamikiridwa

Mwamuna wina wa chapakati pa Siberia analemba kuti: “Mwangozi yeniyeni ndinaona Nsanja ya Olonda m’manja mwa wantchito mnzanga. Ndinapempha kuti aisonyeze kwa ine. Poyamba ndinangoyang’ana zithunzithunzi zake zokongola zamaonekedwe onse. Ndiyeno ndinaŵerenga zowonjezereka. . . Ndisanazindikire, ndinali nditaŵerenga kale magaziniwo kuchokera kuchikuto mpaka kuchikuto. Mafunso anafunsidwa mwanjira yosangalatsa, yaumoyo, ndi yokambitsirana.”

Mwamuna winanso wa ku Siberia anafotokoza kuti: “Mwangozi ndinalandira kope la magazini anu. Sindikufuna kungokukondweretsani ayi, koma iwo alidi ndi chidziŵitso chimene sindinaŵerengepo chabwino kwambiri chonena za chikhulupiriro.”

Nesi wina wa ku St. Petersburg, mzinda waukulu wachiŵiri mu Russia, analemba kuti: “Ndikuthokozani kwambiri kaamba ka mpambo wa nkhani za Galamukani! wa January 8, 1995 wonena za kupsa ndi ntchito. Nkhani zimenezi sizinachotse mavuto anga koma zinandipatsa chichirikizo chimene ndinali kuchiyembekezera ndi kuchifunafuna.”

Mwana wa sukulu wina wazaka 17 analemba kuti: “Ndili woyamikira kwambiri kwa awo onse amene amafalitsa mabuku abwino otereŵa. Pamene ine ndi mabwenzi anga tinali kutuluka m’nyumba ya kanema, tinaona magazini angapo atasiyidwa pampando wopanda munthu. Tinawatenga. . . . Pamene ndinaŵerenga Nsanja ya Olonda, sindinakhulupirire zimene ndinali kuŵerenga. Kodi mtsogolo mudzakhaladi motero? Pakali pano ndimaŵerenga Mauthenga Abwino ndipo ndikuyesayesa kuwamvetsetsa. Magazini anu amalongosola momvekera bwino kwambiri zimene Baibulo limanena.”

Mwamuna wina wazaka 26 anati: “Ndili woyamikira kwambiri pa nkhani yakuti ‘Kodi Kudzipha Ndiko Yankho?’ mu Galamukani! wa April 8, 1994. Chifukwa cha chikhoterero changa cha kuchita tondovi ndi chizoloŵezi cha kuchita pyotopyoto, nthaŵi zambiri ndaganiza za kudzipha. Koma Mawu a Mulungu ndi mapemphero kwa Yehova anandiletsa kuthetsa moyo wanga. Nkhani imeneyi inalimbitsa chikhulupiriro changa pa chifundo cha Mulungu ndi chikhulupiriro changa chakuti Mulungu adzandithandiza kuchita ndi mavuto anga. Iye amaona kulapa kwanga. Amafuna kuti ndikhale ndi moyo. Ndimuyamikira kaamba ka chichirikizo chimene wandipatsa kupyolera m’nkhani iyi.”

Ponena za nkhani imodzimodziyo ya mu Galamukani!, mtsikana wina wazaka 15 anafotokoza kuti: “Magazini ameneŵa andithandiza kwambiri m’moyo wanga. Pamene ndinali ndi zaka zisanu ndi zitatu, ndinayamba kumva kuti panalibe amene anandifuna. Makolo anga analibe nthaŵi yolankhula nane, ndipo ndinayesa kuthetsa mavuto anga pandekha. Ndinadzipatula pandekha. Ndinkalongolola nthaŵi zonse ndi achibale anga. Ndiyeno m’maganizo mwanga munafika lingaliro la kudzipha. Ndinali wokondwa chotani nanga pamene ndinakumana ndi Mboni za Yehova!”

Mkazi wina wa ku dera la Russia la ku Ulaya anati: “Tsiku lina ndinamvetsera makambitsirano a Baibulo a anyamata aŵiri pasiteshoni ya basi. Ndinachita chidwi ndipo ndinawafikira. Anyamata ameneŵa anandipatsa kope la Nsanja ya Olonda. Mokondwa ndipo ndi chisangalalo, ndinaŵeranga magaziniwo, ndipo ndikufuna kudziŵa zochuluka ponena za Baibulo. Ndingakonde kugwirizana nanu kupyolera mwa magazini anu, ndipo ndikufuna kuphunzira ndi kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse.”

Mabuku Ena Oyamikiridwa

Mkazi wina wachichepere wa ku Caucasus analemba kuti: “Mkazi wina anabwera ku ofesi yathu ndi kuyamba kutiuza za msonkhano winawake. Ndinaona chimwemwe ndi chisangalalo chimene anali nacho, ndipo ndinachita chidwi. Tsiku lotsatira anandipatsa buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Ndinaliŵerenga mwamsanga ndi chidwi chachikulu. Chinali chinthu chodabwitsa kwenikweni. Ndinaona kuti pambuyo pa kupupulika mumdima, ndinapeza khomo lopereka ku kuunika. Pambuyo pofunafuna kwanthaŵi yaitali, ndinapeza mayankho pa mafunso anga onse m’buku limodzi chabe. Ichi ndi chisangalalo chosaneneka.”

Mwamuna wina wa ku Central Asia ananena kuti: “Ndine chiŵalo cha Good News Church yaulaliki. Ife tilikufa ndi njala ya mabuku auzimu. Tikukupemphani kutitumizira mofulumira mabuku, mabrosha, ndi timabuku zakuti tiphunzire ndi kugaŵiranso ena.”

Munthu wina wa ku Armenia, pafupi ndi Black Sea, analemba kuti: “Ndinaŵerenga brosha lakuti Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, ndipo kunali ngati kupuma kampweya kabwino. Tsopano ndapeza mabuku omwe adzandithandiza kuphunzira Baibulo. Ndikukupemphani chonde kuti munditumizire mabuku ophunzira otere.”

Mkazi wina wa ku Siberia anati: “Mmodzi wa Mboni za Yehova anafika panyumba pathu ndi kusiya buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Ngakhale kuti ndakhala wokana mulungu chiyambire ndili kusukulu, zimene ndinaŵerenga zinandilimbikitsa kusinkhasinkha mozama ndi kuyamba kuphunzira Baibulo.”

Mayi wina wa ana aŵiri anasonyeza chiyamikiro chake cha buku limodzimodzilo ponena za moyo wa Yesu Kristu ndi kufotokoza kuti: “Nlomveka kwa ana ndi lowakondweretsa kwambiri. Limadzutsa chikhumbo chowonjezereka cha kuphunzira Baibulo ndi kuŵerenga mabuku achipembedzo. Bukulo lafalitsidwa modabwitsa ndipo nlopangidwa bwino kwambiri.”

Chaka chatha, anthu 34,608 m’maiko amene anali Soviet Union anasonyeza chiyamikiro cha zimene anali kuphunzira mwa kubatizidwa. Mafuno athu ndi akuti mabuku ozikidwa pa Baibulo ameneŵa ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova agaŵiridwe mokwanira ndi mwaunyinji m’mbali imeneyi ya dziko, ndi kuti anthu zikwi zowonjezereka achitepo kanthu pa ziphunzitso za choonadi cha Baibulo zopezeka mmenemo!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena