Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 6/08 tsamba 29-31
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
  • Galamukani!—2008
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi pa Chithunzichi Pakusowa Chiyani?
  • Kuchokera M’magazini Ino
  • Zithunzi Zoti Ana Apeze
  • Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2010
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
  • Kodi Mungayankhe Bwanji?
    Galamukani!—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—2008
g 6/08 tsamba 29-31

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi pa Chithunzichi Pakusowa Chiyani?

Werengani Genesis 19:15-17, 23-26. Ndiyeno yang’anani pa chithunzipa. Kodi ndi zinthu zotani zomwe zikusowapo? Lembani mayankho anu pa mizere ili m’munsiyi, ndipo malizitsani kujambula chithunzichi mwa kuika zinthu zomwe zikusowapo.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mkazi wa Loti anakumana ndi zotani, ndipo n’chifukwa chiyani? Kodi mwaphunzirapo zotani pa nkhani imeneyi?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunso awa ndipo tchulani mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.

TSAMBA 6 Kodi makolo ayenera kukhala ofulumira kutani? Yakobe 1:․․․

TSAMBA 7 Kodi mwana wom’lekerera amatani? Miyambo 29:․․․

TSAMBA 10 Kodi Mulungu amamva bwanji akaona munthu aliyense wokonda zachiwawa? Salmo 11:․․․

TSAMBA 20 Kodi tisamakayike kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa chiyani? 1 Yohane 3:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?

Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenaka lembani mayina olondola pa mizereyi.

4. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndine mmodzi wa ana a Yuda amapasa. Mayi anga dzina lawo ndi Tamara, ndipo sindinavekedwe chingwe chofiira.

Werengani Genesis 38:24-30.

5. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Mkazi wanga poyamba anali mkazi wadama wa mumzinda wa Yeriko.

Werengani Yoswa 2:1; Mateyo 1:5.

6. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Mkazi wa chimoabu anadzakhala mkazi wanga.

Werengani Rute 4:9, 10.

◼ Mayankho ali pa tsamba 29

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Mkazi wa Loti.

2. Mwana woyamba wa Loti.

3. Mwana wachiwiri wa Loti.

4. Perezi.—Luka 3:33.

5. Salimoni.—Luka 3:32.

6. Boazi.—Luka 3:32.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena