Zamkatimu
December 2009
N’chifukwa Chiyani Mulungu Analenga Zonsezi?
Asayansi ambiri sagwirizana ndi maganizo akuti pali winawake amene anapanga dzikoli ndiponso kuti anali nalo cholinga. Komabe, pali mfundo zomveka zosonyeza kuti pali winawake amene anapanga anthu ndiponso dzikoli ndipo anali nalo cholinga.
4 Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa Kapena Zinangokhalapo Zokha?
9 N’chifukwa Chiyani Tili ndi Moyo?
11 Kodi Nyenyezi Imene Inatsogolera “Anzeru a Kum’mawa” Inali Yotani?
15 Nyama Zikuluzikulu za M’nyanja
22 Ubwino Wosonyezana Chikondi
30 Mlozera Nkhani wa Magazini a Galamukani! a 2009
32 Analimba Mtima Kufotokoza Zimene Amakhulupirira
Kodi Mungathetse Bwanji Njala Yanu Yauzimu? 12
Ena amaganiza kuti angathetse njala yawo yauzimu pochita miyambo yosiyanasiyana yachipembedzo kapena yachikhalidwe. Kodi njira iliyonse yothetsera njala yanu yauzimu ndi yovomerezeka? Werengani nkhaniyi kuti mumve zimene Baibulo limanena.
Chimene Chinandichititsa Kusiya Kukonda Nkhondo 24
Werengani nkhani yochititsa chidwi ya munthu wina amene ankakonda nkhondo kwambiri koma kenako anasiya atapeza zochita zina zabwino.