Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/09 tsamba 3
  • Chilengedwe N’chogometsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilengedwe N’chogometsa
  • Galamukani!—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Zinthu Zinachita Kulengedwa Kapena Zinangokhalapo Zokha?
    Galamukani!—2009
  • Zimene Zinthu Zakuthambo Zimatiuza
    Galamukani!—2021
  • ‘Pakusoŵeka Chinthu China’—Chiyani?
    Galamukani!—1996
  • Mlengi Angawonjezere Tanthauzo la Moyo Wanu
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Galamukani!—2009
g 12/09 tsamba 3

Chilengedwe N’chogometsa

ASAYANSI atulukira zinthu zambiri zokhudza chilengedwe, ndipo zimenezi zathandiza kuti anthu adziwe zinthu zosiyanasiyana, kuyambira pa zinthu zazing’ono kwambiri mpaka pa zinthu zazikulu zedi. Ngakhale zili choncho, m’chilengedwe muli zinthu zambiri zogometsa zomwe anthufe sitikuzidziwabe mpaka pano.

Dziko lathu lapansili ndi kachigawo chochepa chabe poyerekeza ndi chilengedwe chonse. Komabe, padzikoli pali zinthu zogometsa komanso zokongola kwambiri. Anthu amachita chidwi ndi maluwa okongola, malo osangalatsa, mbalame, agulugufe, kulowa kwa dzuwa, kapena kuona mabwenzi awo akumwetulira.

Anthu ambiri apeza umboni wochuluka womwe umawachititsa kukhulupirira kuti zinthu zonsezi zinachita kulengedwa. Iwo amanena kuti malamulo a m’chilengedwe anachunidwa bwino komanso mosamala kwambiri. Ngati malamulowa akanachunidwa mosiyana, ngakhale pang’ono chabe, padzikoli sipakanakhala zamoyo. Koma popeza kuti malamulo amenewa anachunidwa bwino kwambiri, padziko lapansi pali zinthu zamoyo zambirimbiri.

Wasayansi wina wotchuka, dzina lake Paul Davies, ananena kuti: “Zinthu zakuthambo zimasonyeza kuti zimayenda motsatira kwambiri malamulo a m’chilengedwe . . . Umenewu ndi umboni wakuti zinthuzi sizinakhaleko mwangozi koma m’malomwake zinapangidwa moti zizitsatira malamulo amene anakhazikitsidwa mwanzeru kwambiri.” Asayansi ena amaona kuti zimenezi ndi zoona. Koma ena amatsutsa maganizo amenewa.

Mwachitsanzo, wasayansi wina amene analandirapo mphoto ya Nobel, dzina lake Steven Weinberg, anati: “Tikamadziwa zambiri zokhudza mmene chilengedwe chimagwirira ntchito, m’pamenenso timaona kuti chilengedwechi n’chopanda tanthauzo.” Koma Weinberg anadzitsutsa yekha pamene ananena kuti: “Zinthu za m’chilengedwe zimaoneka kuti n’zokongola kwambiri kuposa mmene zinayenera kukhalira. . . . Choncho m’pake kuganiza kuti pali winawake amene anapanga zinthu zokongolazi n’cholinga choti tizisangalala nazo.”

Ndiye kodi mfundo yolondola ndi iti? Kodi zingatheke kuti zinthu za m’chilengedwe zichunidwe bwino popanda amene anazichuna? Kodi cholinga cha moyo wathu komanso zinthu zonse za m’chilengedwe n’chotani? Kodi anthufe tinangokhalapo mwangozi? Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso amenewa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena