Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 10/11 tsamba 24-30
  • Zoti Banja Likambirane

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zoti Banja Likambirane
  • Galamukani!—2011
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?
  • Sungani Kuti Muzikumbukira
  • Anthu ndi Mayiko
  • Zithunzi Zoti Ana Apeze
  • MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2012
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2012
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2012
  • Zoti Banja Likambirane
    Galamukani!—2011
Onani Zambiri
Galamukani!—2011
g 10/11 tsamba 24-30

Zoti Banja Likambirane

Kodi Pachithunzipa Pakusoweka Chiyani?

Werengani Miyambo 18:10 ndi 26:17. Kenako yang’anani chithunzichi. Tchulani zinthu zimene zikusowekapo. Lembani mayankho anu m’munsimu. Malizitsani kujambula chithunzichi polumikiza timadonthoto, ndipo chikongoletseni ndi chekeni.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

[Zithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

KAMBIRANANI:

Kodi mavesi amenewa akukuphunzitsani chiyani? Kodi kungodziwa dzina la Mulungu n’kokwanira kuti munthu azikondedwa ndi Mulungu?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 91:2; Miyambo 3:5, 6.

N’chifukwa chiyani muyenera kupewa kulowerera nkhani za ena?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Agalatiya 6:5-7; 1 Atesalonika 4:11; 1 Petulo 4:15.

Kenako werengani Miyambo 26:18, 19. Kodi kuchita nthabwala zopusitsa ena n’kwabwino?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Miyambo 14:13; 15:21; Mateyu 7:12.

ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:

Werengani pamodzi Miyambo 31:10-31. Ngati n’kotheka, sankhani munthu mmodzi kuti ayerekezere ntchito zimene mkazi wabwino amene akufotokozedwa palembali amachita, popanda kutchula mawu. Ena onse m’banjamo azinena ntchito zimene zikuyerekezedwazo. Kambiranani zinthu zimene nonse mungaphunzire kwa mkazi wotchulidwa palembali.

Sungani Kuti Muzikumbukira

Dulani, pindani pakati n’kusunga

KHADI LA BAIBULO 10 SOLOMO

MAFUNSO

A. Solomo sanapemphe kuti Yehova amupatse chuma kapena moyo wautali. Ndiyeno kodi anapempha chiyani?

B. Lembani mawu amene akusowekapo. Solomo ankanena miyambi yokwana _____ ndipo nyimbo zake zinali zokwana ______.

C. Kodi Solomo anapatsidwa dzina linanso liti?

[Tchati]

4026 B.C.E. 1 C.E. 98 C.E.

Kulengedwa kwa Adamu Anakhala ndi moyo Baibulo

cha m’ma 1000 B.C.E. linamalizidwa

kulembedwa

[Mapu]

Mfumukazi ya ku Seba inayenda ulendo wamakilomita pafupifupi 2,400 kuti ikamve nzeru za Solomo

SEBA

Yerusalemu

SOLOMO

ANALI NDANI?

Mwana wachiwiri wa Davide ndi Bateseba. Solomo analamulira dziko la Isiraeli kwa zaka 40. Anamanga nyumba yaikulu yolambiriramo Yehova. (1 Mafumu 5:2-5) Yehova anagwiritsa ntchito Solomo kulemba buku la Miyambo, Mlaliki ndi Nyimbo ya Solomo. Akazi ake achikunja anamuchititsa kuti asiye kutumikira Yehova.—1 Mafumu 11:1-6.

MAYANKHO

A. Mtima womvera.—1 Mafumu 3:5-14.

B. 3,000, 1,005.—1 Mafumu 4:29, 32.

C. Yedediya, kutanthauza “Yehova anam’konda.”—2 Samueli 12:24, 25.

Anthu ndi Mayiko

3. Dzina langa ndi Chloe. Ndili ndi zaka 9, ndipo ndimakhala ku Canada. Kodi mukudziwa kuti ku Canada kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 55,000; 88,000 kapena 110,000?

4. Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ndimakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko, ndipo kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi dziko la Canada.

A

B

C

D

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pachithunzi chilichonse.

Nkhani zina zakuti “Zoti Banja Likambirane” mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

● Mayankho a “ZOTI BANJA LIKAMBIRANE” ali patsamba 24

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 30 NDI 31

1. Nsanja yolimba.

2. Galu.

3. 110,000.

4. A.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena