Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 10/12 tsamba 3
  • Muzilimbikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzilimbikira
  • Galamukani!—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungachite Ngati Simukusangalalanso ndi Sukulu
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kuika Nzeru Kumaphunziro Pasukulu?
    Galamukani!—1992
  • Kodi Ndisiye Sukulu?
    Galamukani!—2010
  • Mfungulo Zopezera Maphunziro Abwino
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 10/12 tsamba 3

Muzilimbikira

Munthu amalimbikira kuchita chinachake ngati waona kuti n’chaphindu.

KODI munthu angapindule bwanji ndi sukulu? Sukulu imathandiza kuti munthu adziwe zinthu kapena kuti akhale ndi nzeru ndipo Baibulo limanena kuti “nzeru zimateteza.” (Mlaliki 7:12) Kodi nzeru zimateteza bwanji? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyerekeze kuti mukudutsa malo enaake oopsa. Kodi mungasankhe kuyenda nokha kapena ndi anzanu amene angakutetezeni ngati mutakumana ndi zoopsa? Zinthu zimene mumaphunzira ku sukulu zili ngati anzanu amene angakuthandizeni pa moyo wanu wonse. Zina mwa zinthu zimenezi ndi izi:

  • Kuganiza bwino. Sukulu imathandiza munthu kuti azitha kuchita zimene Baibulo limanena kuti ndi “kudziwa zinthu komanso kuganiza bwino.” (Miyambo 3:21, Contemporary English Version) Zinthu zimenezi zikhoza kukuthandizani kuti muthane nokha ndi mavuto anu m’malo momangodalira anthu ena.

  • Kukhala bwino ndi anthu. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti aziyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino ngati kuleza mtima ndi kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Popeza munthu akakhala ku sukulu amachita zinthu ndi anthu osiyanasiyana, amakhala ndi mwayi wosonyeza makhalidwe ngati kulolera, kulemekeza ena komanso chifundo. Makhalidwe amenewa angadzamuthandizenso akadzakula.

  • Kukukonzekeretsani zam’tsogolo. Sukulu imathandiza munthu kuti adziwe kufunika kolimbikira ntchito, zomwe zingadzamuthandize kuti adzapeze ntchito mosavuta komanso kuti adzakhalitse pantchitopo. Kuwonjezera pamenepa, sukulu imathandizanso kuti munthu adzidziwe bwino komanso adziwe mfundo zimene amayendera. (Miyambo 14:15) Kudziwa zimenezi kungamuthandize kuti azilimba mtima kuuza ena mwaulemu zimene amakhulupirira.​—1 Petulo 3:15.

Mfundo yofunika kuikumbukira: Monga taonera, sukulu ndiyofunika kwambiri. Koma mukamangoganizira zinthu zomwe sizikusangalatsani pa nkhani ya sukulu mukhoza kuyamba kudana nayo. Choncho, mungachite bwino kuganizira mfundo zimene tazifotokozazi komanso mfundo zina.

Yambani kutsatira malangizo amenewa. Sankhani ndi kuyamba kutsatira mfundo imene ingakuthandizeni kuti muzilimbikira sukulu.

Ana Amanyadira Mphunzitsi Wabwino

“Aphunzitsi omwe ankatiphunzitsa phunziro la Economics anali ophunzira kwambiri moti akanatha kugwira ntchito yapamwamba m’makampani ena. Koma iwo anasankha kugwira ntchito yauphunzitsi, yomwe imaoneka ngati yotsika. Ana a sukulu akawafunsa chifukwa chake anasankha kudzaphunzitsa pasukulu yathu, iwo ankayankha kuti amakonda ntchito yauphunzitsi ndipo ankasangalala kwambiri kuphunzitsa pasukulu yathu kuposa malo ena alionse amene anagwirako ntchito. Nthawi zambiri ana a sukulu sakonda phunziro la Economics, koma tonse m’kalasi mwathu tinkakonda phunziroli chifukwa aphunzitsiwo ankayesetsa kuphunzitsa mosavuta komanso mosangalatsa. Ankatithandizanso kuona mmene nkhani zachuma zingatithandizire. Tinkawakonda kwambiri chifukwa ankatimvetsa, ankatidera nkhawa komanso ankatilimbikitsa. Nthawi ina anawaimbira foni mayi anga n’kuwauza kuti ndinakhoza bwino phunziro lawolo. Sindinakhaleponso ndi mphunzitsi wabwino ngati ameneyu.”​—Anatero Reyon, wa ku United States.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena