Zimene Mungachite Kuti Zizikuyenderani ku Sukulu
Pa mawu ali m’munsiwa, kodi ndi mawu ati amene akufotokoza mmene inuyo mumaonera sukulu?
Yotopetsa kapena yosangalatsa?
Yovuta kapena yopindulitsa?
Yosafunika kapena yothandiza?
Ngati inuyo mumaona kuti sukulu ndi yosasangalatsa, kodi mungatani kuti muyambe kuikonda? Ngati mumaikonda, kodi mungatani kuti mupindule nayo kwambiri? Patsamba 3 mpaka 7, pali mfundo zisanu za m’Baibulo, zomwe zingakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino ku sukulu.