Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 1/8 tsamba 28-29
  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zofunika
  • Mmene Imachitidwira ndi Kosi Yake
  • Kuthandiza Mamiliyoni
  • Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Kulembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Mmene Timapindulira ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 1/8 tsamba 28-29

Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse

IMENEYI si sukulu yosakhala ya boma yokwera mtengo kapena yunivesite ina yotchuka kumene kumapita anthu angapo okha osankhidwa. Ayi, sukulu imeneyi imachitidwa popanda kulipiritsa ophunzira ake. Magawo ake angakhale akuchitidwira pafupi ndi kwanuko. Imatchedwa kuti Sukulu Yautumiki Wateokratiki, ndipo imachitidwa pamalo osonkhanirapo Mboni za Yehova. Anthu pafupifupi mamiliyoni asanu padziko lonse amafika pasukulu imeneyi.

Mungadabwe kuti, ‘Kodi zofunika zake zolembetsera nzotani? Kodi m’sukuluyo amaphunzitsamo chiyani? Kodi imachitidwa motani? Ndipo kodi anthu amapindula nayo motani?’

Zofunika

Pamene kuli kwakuti anthu onse amalandiridwa pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki, awo amene amalembetsa ayenera kukhala ogwirizana ndi ziphunzitso za buku lalikulu lophunziridwa la sukuluyo, Baibulo. Amafunikira kukhala ndi moyo umene umagwirizana ndi zofunika zamakhalidwe a Baibulo. Chotero ophunzirawo sayenera kukhala ndi makhalidwe oipa. Sayenera kukhala mbala, oledzera, adama, osuta fodya, ndi zina zotero.—1 Akorinto 6:9-11.

Sukulu zambiri lerolino zasiya malamulo akavalidwe, koma ophunzira amene amalembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki afunikira kuvala zovala zoyera zoyenera. (1 Timoteo 2:9, 10) Sukuluyi ilibe usinkhu. Ana aang’ono azaka zinayi kapena zisanu amene akhoza kuŵerenga amalembetsa ndipo amakamba nkhani nthaŵi zonse, monga momwe amachitira amuna ndi akazi amene ali m’ma 90.

Mmene Imachitidwira ndi Kosi Yake

Kuti zikhale zofeŵa kwa ofikapo ake, magawo a mphindi 45 a Sukulu Yautumiki Wateokratiki amachitidwa nthaŵi zambiri pakati pa mlungu madzulo. Pambuyo pa malonje achidule operekedwa ndi mlangizi wa sukulu, mlankhuli woyamba madzulowo amapereka nkhani ya mphindi 10 mpaka 15 yozikidwa pa limodzi la mabuku asukulu ophunziridwa. Ndiyeno, kaŵirikaŵiri amafunsa mafunso kwa mphindi zitatu mpaka zisanu pankhani imene wakamba.

Kenako, mphunzitsi wina wokhoza amafotokoza mfundo zazikulu za gawo la kuŵerenga Baibulo kwamlungu ndi mlungu, limene kaŵirikaŵiri limakhala ndi machaputala aŵiri kufikira anayi m’Baibulo. Kupenda kumeneku nkwamphindi zisanu ndi imodzi. Ophunzira amene amayendera limodzi ndi gawo la homuweki limeneli lamlungu ndi mlungu amaŵerenga Baibulo lonse m’kupita kwa nthaŵi.

Mfundo zazikulu za Baibulo zitatha, ophunzira atatu amapereka nkhani, iliyonse yamphindi zisanu. Imodzi imakhala ya kuŵerenga Baibulo pachigawo cha homuweki yogaŵiridwa. Nkhani zina ziŵirizo zimazikidwa pamabuku asukulu amene ophunzira onse amalimbikitsidwa kuŵerenga pokonzekera kalasi. Wophunzira aliyense atakamba nkhani yake, mlangizi wasukulu amayamikira ndipo, kaŵirikaŵiri, amapereka malangizo a kuwongolera.

Uphungu wa mlangizi umazikidwa pa Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki, limene wophunzira aliyense amayembekezeredwa kuliŵerenga mosamalitsa. Kuti awongolere mkhalidwe wina wa kulankhula kaamba ka nkhani yotsatira, wophunzirayo angapemphedwe kukaŵerenganso mutu wina m’buku lolangizalo, monga ngati wakuti “Kuyang’ana Omvetsera ndi Ntchito ya Notsi,” “Mafanizo Oyenerera,” “Ntchito ya Kubwereza ndi Majesicha,” ndi “Kugogomezera Ganizo ndi Kusintha Mawu.”

Pakati pa ena Sukulu Yautumiki Wateokratiki ili ndi kalasi lina lowonjezeredwa la kuwongolera kulemba ndi kuŵerenga. Zikwi makumi ambiri zaphunzira kuŵerenga kapena kuwongolera kuŵerenga kwawo m’makalasi amenewo. Mwachitsanzo, ku Mexico pakati pa 1946 ndi 1994, anthu oposa 127,000 anathandizidwa kudziŵa kulemba ndi kuŵerenga.

Kuthandiza Mamiliyoni

Kuzungulira dziko lonse Sukulu Yautumiki Wateokratiki ikuchirikiza zoyesayesa za makolo za kupereka maphunziro abwino kwa ana awo. Moriah wazaka 16 anati: “Ndinaphunzira kufufuza nkhani mwakuya ndi kuyeseza maulaliki anga. Tsopano gawo lililonse la ntchito limene ndimapatsidwa kusukulu yasekondale limakhala losavuta.”

Matthew wazaka 15, amene analembetsa Sukulu Yautumiki pausinkhu wazaka zisanu ndi ziŵiri, anati: “Ndimakhala ndi mwaŵi waukulu pakati pa ausinkhu wanga pankhani ya kupambana m’maphunziro. Ndapeza maluso ophunzirira ndi kumvetsera ndi kukhoza kukamba nkhani mogwira mtima.” Mkulu wake wazaka 17, Phil, akuwonjezera kuti: “Sukulu Yautumiki Wateokratiki yandichititsa kukhala ndi chidaliro kwambiri. Ndimadziŵa kuti ngati ndipatsidwa gawo, ndingathe kulisamalira.”

Sukulu Yautumiki Wateokratiki yaphunzitsanso anthu achikulire. Michael, amene anafikira zonulirapo zonga kukambira nkhani bungwe loyang’anira ntchito, akufotokoza kuti: “Ndinali ndi mantha aakulu pamene ndinalembetsa Sukulu Yautumiki. Sindilinso wamanyazi. Sukuluyo inapereka mkhalidwe wabwino, chidziŵitso, maluso, ndi chilimbikitso chaumwini chimene ndinafuna kuti ndiwonjoke ku mkhalidwewo.” Kholo lina linati: “Ndiganiza kuti ndabwezeretsa mwaŵi wakuphunzira umene ndinaphonya pamene ndinali wachichepere.”

M’mudzi wina wa ku Latin America, ziŵalo za Department of Education zinafika pa Sukulu Yautumiki Wateokratiki. Zitamvetsera kwa mlankhuli wakumaloko, mmodzi wa alendowo, mkulu wa sukulu, anadzuma kuti: “Nkovuta kuvomereza kuti mwamuna uyu amene tamdziŵa nthaŵi zonse kukhala wosaphunzira ali wokhoza kulankhula kwa omvetsera m’Chispanya [m’malo mwa chinenero chake], koma ndi zimene akuchita.”

Indedi, Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi imodzi ya sukulu zabwino koposa m’dziko! Ingathe kuthandiza achichepere ndi achikulire omwe kupeza maphunziro abwino. Zili monga momwe wachichepere wina ananenera, “Ndingalimbikitse aliyense amene akufuna kulembetsa sukuluyo kuti achite mofulumira.”

[Chithunzi patsamba 29]

Sukulu Yautumiki Wateokratiki ikuthandiza mamiliyoni ambiri kupeza maphunziro abwino

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena