Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
1 Anthu amapita ku sukulu kukaphunzira zimene zidzawathandiza kuchita zomwe amafuna pamoyo wawo. Komabe, ndi chiyani chingakhale chofunika kwambiri pamoyo wa munthu kuposa kutamanda amene anatipatsa moyo komanso kuthandiza ena kuphunzira zolinga zake ndi njira zake? Palibe. Cholinga cha Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ndi kutikonzekeretsa kuti tiphunzitse anthu ena chikhulupiriro chathu. Choncho, ngati tipezeka pa sukuluyi mlungu uliwonse, tidzapeza luso limene limatikonzekeretsa kuchita zinthu zofunika kwambiri pamoyo wathu.
2 “Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2003” inaikidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha. Ndandandayi inafotokoza bwinobwino mmene sukuluyi izichitikira. N’kothandiza kwambiri kuisunga m’buku lanu la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, limene muyenera kumabwera nalo mlungu uliwonse ku Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Onani mbali zina za ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2003.
3 Luso la Kulankhula: Kuyambira mu January, msonkhano uliwonse udzayamba ndi nkhani ya mphindi zisanu yonena za luso la kulankhula kapena mbali ina ya kuŵerenga, kuphunzira kapenanso kuphunzitsa. Woyang’anira sukulu ndi amene azidzakamba nkhani zoyambirira zimenezi kapena angam’patse mkulu wina woyenerera kukamba nkhani imeneyi. Wokamba nkhaniyi azidzafotokoza tanthauzo ndiponso kufunika kwa luso la kulankhula. Ndiyeno, azidzafutukula nkhaniyi mwa kufotokoza zitsanzo za m’Malemba ndiponso azidzasonyeza mmene tingagwiritsire ntchito luso limeneli, azidzatsindika momwe kuchita zimenezi kungapititsire patsogolo utumiki wathu wakumunda.
4 Nkhani Na. 1: Abale opatsidwa nkhani yolangiza akulangizidwanso kuti ayenera “kusonyeza phindu la mfundo zimene akufotokoza.” Izi zikutanthauza kuwasonyeza anthu pampingopo momwe angagwiritsire ntchito zimene akuphunzirazo. Ngati mwapatsidwa nkhani imeneyi, onani masamba 48 ndi 49 a buku la Sukulu ya Utumiki kuti muone momwe mungakonzekerere nkhaniyi, ndiponso ŵerengani masamba amene mlozera nkhani wa bukuli watchula pamutu wakuti “Kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba.”
5 Ndandanda ya Kuŵerenga Baibulo: Ngati m’mbuyomu mumalephera kutsatira kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu, bwanji osatsimikiza mtima kutsatira ndandandayi chaka chino? Amene achite zimenezi adzamaliza kuŵerenga Malemba Achigiriki Achikristu pakutha pa chaka. Ubwino woyamba kuŵerenga Baibulo ndi Malemba Achigiriki Achikristu uli patsamba 10, ndime 5, m’buku la Sukulu ya Utumiki.
6 Mfundo Zazikulu za Kuŵerenga Baibulo: Nkhani imeneyi tsopano izikhala ya mphindi teni kuti omvetsera azipereka ndemanga zimene apeza pa kuŵerenga Baibulo kwa mlungu umenewo. Opatsidwa nkhani imeneyi azisunga nthaŵi imene apatsidwa. Nkhani imeneyi izikhalako mlungu uliwonse, ndi mlungu wa kubwereza kwa pakamwa womwe. Poŵerenga machaputala a mlunguwo, yang’anani mfundo zimene zingakuthandizeni paphunziro lanu la banja, mu utumiki wanu, kapena pamoyo wanu. Kodi Yehova anasonyeza makhalidwe ati pochita zinthu ndi anthu ena komanso mitundu ya anthu? Kodi n’chiyani chimene mwaphunzira chimene chalimbitsa chikhulupiriro chanu ndi kukulitsa kuyamikira kwanu Yehova? Khalani womasuka kunena ndemanga pa mfundo iliyonse ya m’machaputalawo, ngakhale mavesi amene aŵerengedwe mu Nkhani Na. 2, popeza mbale wokamba nkhani imeneyi sadzanena chilichonse pa mavesiwo akatha kuŵerenga.
7 Nkhani Na. 2: Wophunzira woyamba mlungu uliwonse aziphunzira kuŵerenga pamaso pa anthu. Kuŵerengaku kuzichokera pa kuŵerenga Baibulo kwa m’mlunguwo koma pa mapeto amwezi kuŵerengako kuzichokera mu Nsanja ya Olonda. Wophunzirayo aziŵerenga mavesi amene wapatsidwa popanda kukamba mawu oyamba kapena omaliza. Mwanjira imeneyi, aziika maganizo ake onse pa luso la kuŵerenga.—1 Tim. 4:13.
8 Nkhani Na. 3 ndi Na. 4: Zina mwa nkhani zimenezi mfundo zake zambiri zatengedwa m’buku la Kukambitsirana kuposa nkhani zina; zina zili ndi mutu wa nkhani wokha. Amene apatsidwa nkhani zimene zili ndi mfundo zochepa kapena zimene zili ndi mutu wa nkhani wokha, adzakhala ndi mwayi wokamba nkhani zawozo mogwiritsira ntchito zimene apeza pofufuza m’mabuku athu achikristu. Izi zidzathandiza alongo kunena mosavutika zinthu zogwirizana ndi othandizira awo.
9 Mitundu ya Makambirano: Monga anenera patsamba 45 la buku la Sukulu ya Utumiki, woyang’anira sukulu angakuuzeni mtundu wa makambirano. Ngati sananene, ndiye kuti alongo angasankhe pa m’ndandanda wa makambirano patsamba 82. Ngati mlongo akamba nkhani imodzi pakatha miyezi iŵiri iliyonse, ndiye kuti mitundu ya makambirano 30 imeneyo ndi yokwanira kuigwiritsira ntchito kwa zaka zisanu. Alongo amene asankha mtundu wa makambirano Na. 30, wakuti “Mtundu wina wa makambirano woyenerana ndi kwanuko,” ayenera kulemba mtunduwo pansi kapena kuseri kwa pepala lopatsidwira nkhani la (S-89). Woyang’anira sukulu adzalemba tsiku limene wophunzira wakamba nkhani yake patsamba 82 la buku lake pafupi ndi mtundu wa makambirano amene wagwiritsira ntchito. Angachite zimenezi pamene akulemba fomu yolangizira ya wophunzirayo.
10 Fomu Yolangizira: Fomu yanu yolangizira ili m’buku lanu la Sukulu ya Utumiki. Ili pamasamba 79 mpaka 81. Chotero, mukatha kukamba nkhani iliyonse, muzipereka buku lanulo kwa woyang’anira sukulu. Woyang’anira sukulu afunika kusunga mfundo zolangizira zimene ophunzira akugwirirapo ntchito.
11 Kubwereza kwa Pakamwa: Kubwereza zophunzira mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu kuzikhala kongokambirana. Kuzichitika kamodzi pakatha miyezi iŵiri iliyonse ndipo kuzikhala kwa mphindi 30. Mafunso ogwiritsira ntchito pa kubwerezaku azipezekabe mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Ngati mlungu woti muchite kubwerezaku muli ndi msonkhano wadera kapena mukuchezeredwa ndi woyang’anira dera, ndiye kuti nkhani za mlungu wotsatira muzizikamba mlungu umenewu ndipo kubwerezako kuzichitika mlungu winawo.
12 Makalasi Aang’ono: Mipingo imene ili ndi ophunzira oposa 50 mu sukuluyi, akulu angasankhe zokhala ndi makalasi aang’ono. “Makonzedwe ameneŵa angakhale a nkhani zonse za ophunzira kapena ziŵiri zomalizira.” (Sukulu ya Utumiki, tsa. 285) Malingaliro omalizaŵa ndi a mipingo imene ili ndi alongo ambiri koma abale okamba nkhani zoŵerenga ali ochepa. Akulu ayenera kusankha abale oyenerera kuti azichititsa m’makalasi ameneŵa.
13 Mlangizi Wothandiza: Monga ananenera mu ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, bungwe la akulu n’limene limasankha mlangizi wothandiza kuti azipereka malangizo am’seri kwa akulu ndi atumiki otumikira amene amakamba mfundo zazikulu za Baibulo ndiponso nkhani zolangiza. Mbale amene waikidwa kuti azichita zimenezi ayenera kukhala waluso, amene akulu anzake angalemekeze malangizo ake. Malangizo ake ayenera kukhala abwino, aziyamikira luso labwino la kulankhula ndi kuphunzitsa ndiponso azifotokoza mfundo imodzi kapena ziŵiri zimene wokamba nkhaniyo akufunika kuwongolera. Mbale amene amakambakamba nkhani sikofunika kumulangiza nthaŵi iliyonse imene iye wakamba nkhani. Komabe, mbale wolangizayo ayenera kuzindikira kuti ngakhale abale amene tsopano amakamba nkhani za onse angathandizidwe kupita patsogolo.—1 Tim. 4:15.
14 Zofunika Kuona: Kodi n’chiyani chingathandize mlangizi kupenda nkhani? Bokosi lachitatu m’mitu yambiri mwa mitu 53 imene ili ndi manambala mu buku la Sukulu ya Utumiki lili ndi chidule cha zimene ayenera kuona pamene munthu akukamba nkhani. Woyang’anira sukulu ayeneranso kuona zinthu zina zofunika kuzikumbukira kapena mfundo za m’bukuli zimene zingamuthandize kudziŵa mwamsanga kuti nkhaniyo inasanjidwa bwanji ndiponso yakambidwa motani. Mwachitsanzo, onani mafunso ali pamwamba patsamba 55 ndiponso onani mfundo zili pa ndime yomaliza patsamba 163.
15 Lembani M’malo Amene Sanalembedwe Kanthu: Ngakhale kuti kumapeto kwa bukuli kuli malo aakulu oti munthu angalembepo, buku la Sukulu ya Utumiki lili ndi malo angapo opanda kanthu amene mungalembepo notsi zanu pa phunziro lanu laumwini ndiponso pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. (Onani masamba 77, 92, 165, 243, 246, ndi 250.) Onetsetsani kuti mlungu uliwonse mwabwera ndi bukuli. M’tsatireni wokamba nkhani yotsegulira pamene akukamba nkhani yake. Siyani bukulo lili lotsegula mpaka sukuluyo itatha. Lembani malingaliro amene woyang’anira sukulu wanena. Mvetserani njira zophunzitsira, mafunso, zitsanzo, mafanizo, zinthu zooneka, ndiponso kusiyanitsa zinthu kumene okamba nkhani agwiritsira ntchito. Mwa kulemba notsi zabwino, mudzakumbukira ndi kugwiritsira ntchito mfundo zabwino zambiri zimene munatola m’sukuluyi.
16 Yesu Kristu anadziŵa kuti kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi mwayi waukulu zedi umene munthu angakhale nawo. Ndiyo inali ntchito yake yeniyeni. (Marko 1:38) Iye anati: “Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu . . . chifukwa ndinatumidwa kudzatero.” (Luka 4:43) Mofanana ndi amene avomera kum’tsatira, ifenso tatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino, ndipo nthaŵi zonse timayesetsa kuwongolera luso la “nsembe [yathu] yakuyamika.” (Aheb. 13:15) Kuti tikwaniritse zimenezi, tiyeni titsimikize mtima kukhala nawo nthaŵi zonse pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, sukulu imene idzatithandiza kukonzekera kuchita zinthu zimene zili zofunika kwambiri pamoyo wa munthu.