Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • sg phunziro 2 tsamba 9-13
  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa
  • Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Nkhani Yofanana
  • Malangizo kwa Oyang’anira Sukulu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Bokosi la Mafunso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Sukulu Yautumiki Wateokratiki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
Onani Zambiri
Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
sg phunziro 2 tsamba 9-13

Phunziro 2

Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa

1-5. Kodi ndi maphunziro otani amene sukulu yautumiki imapereka potithandiza mu utumiki wathu kwa Mulungu?

1 Ndi motani mmene Yehova amatiphunzitsira atumiki akefe kukhala ogwira mtima mu utumiki? Amatero kupyolera m’gulu lake. M’maiko ambiri kuphunzitsako kumayambira pa luso loyambirira lenilenilo la kuŵerenga. Kwa awo amene aphunzira kuŵerenga ndi kulemba, sitepi lotsatira ndilo kulembetsa m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase.

2 Sukulu imeneyi imaphunzitsa zautumiki kwaulere. Imathandiza mpingo m’njira ziŵiri: (1) Wophunzira aliyense amapatsidwa pologalamu ya phunziro imene imam’thandiza kukulitsa luso la kusonkhanitsa nkhani, kuiumba ndi kuikamba kwa ena mwatsatanetsatane; ndipo (2) mpingo wonse umalandira chidziŵitso chopindulitsa kwambiri papologalamu ya mlungu uliwonse. Zotsatirapo zimakhala chiyamikiro chokulirapo pa zinthu zauzimu, komanso ntchito yautumiki imawongokera.

3 Pologalamu imeneyi m’dziko lililonse imakonzedwa ndi ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society ndipo ndandanda ya chaka ndi chaka imaperekedwa. Pologalamuyo imadalira mabuku opezeka m’chinenero kapena zinenero za dzikolo. Kwakukulukulu imazikidwa pa Baibulo.

4 Nkhani zingapo zothandiza zimalankhulidwa ndi ophunzira mlungu uliwonse. Yaikulu pa zonse imatchedwa nkhani yolangiza ndipo ili yotalikirapo kuposa zinazo. Imapatsidwa kwa mbale wokhoza bwino, kotero kuti mpingo upindule kwathunthu. Nkhani zinazo n’zazifupi ndipo zingapatsidwe kwa mwamuna kapena mkazi malinga ndi zimene ndandanda ya sukulu ikusonyeza. Imodzi mwa nkhani zofupikirapo za ophunzirazo, malinga ndi ndandanda ya m’dzikolo, ingakhale kuŵerenga Baibulo. Nkhani zinazo zidzakambidwa mwa kufutukula mutu wa nkhani woperekedwa ndipo mwina zidzatengera mkhalidwe winawake woyenera, ngati kuli koyenerana ndi nkhaniyo. Nkhani zolankhulidwa ndi alongo kaŵirikaŵiri zidzakhala za mkhalidwe wa kulalikira mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, mwinamwake kukambirana pa ulendo wobwereza kapena pambuyo pa phunziro la Baibulo, umboni wamwamwayi, kapena kukambirana ndi apabanja lake kapena wofalitsa wina.

5 M’mipingo yaing’ono ya akazi okhaokha nkhani zonse zikhozabe kukambidwa. Motani? Mwa njira ya kusimba nkhani, kukambirana kwa alongo aŵiri, mafunso ndi mayankho kapena kungoŵerenga nkhani yofalitsidwayo.

6. Kodi ndi ziyeneretso zotani zimene zimafunika kwa woyang’anira sukulu?

6 Woyang’anira sukulu. Woyang’anira Sukulu ya Utumiki Wateokalase amaikidwa mumpingo uliwonse. Ayenera kukhala mphunzitsi wokhoza. Afunikira kukhala wodziŵa bwino choonadi cha Baibulo komanso chinenero cha ochuluka a ophunzira ake. Afunikira kukhala wosamala ndi wachifundo. Mwauzimu, ayenera kukhala “mwamuna mkulu.” Ali ndi udindo wokulembani m’sukulu, kukupatsani nkhani ndi uphungu wolimbikitsa mokoma mtima.

7. Ndi zinthu zotani zimene amazilingalira pogaŵira nkhani?

7 Woyang’anira sukulu amasunga maina a olembetsa, makamaka kuti aziwagwiritsa ntchito powapatsa nkhani. Kaŵirikaŵiri nkhani zimenezo zimapatsidwa pafupifupi milungu itatu pasadakhale, mwa chidziŵitso cholembedwa. Zimenezi zimakupatsani nthaŵi yoti mupende ndi kukonzekera nkhaniyo kuti mudzailankhule bwino. Woyang’anira sukulu amadziŵa kuti muli anthu a maphunziro osiyanasiyana mumpingo, motero amapatsa nkhani akumakumbukira zimenezo. Amayesa kusapatsa wophunzira wamng’ono kwambiri nkhani yosayenerana ndi msinkhu wake. Ndipo amayesa kupereka mwayi wofanana kwa wophunzira wolembedwa aliyense wolankhula nkhani m’pologalamuyo.

8. N’chifukwa chiyani ophunzira okamba nkhani amapatsidwa chizindikiro pamene adya nthaŵi?

8 Ndithudi, pamene sukulu ikuchitidwa, siyenera kupitirira nthaŵi yake. Chotero, pamene nkhani za ophunzira zipitirira nthaŵi, woyang’anira sukulu kapena wom’thandiza adzapereka chizindikiro. Wophunzirayo ayenera kutsiriza sentensi imene akulankhula ndiyeno achoke papulatifomu.

9-12. Kodi woyang’anira sukulu amaonetsa motani chidwi chake pakupita patsogolo kwa awo amene amakamba nkhani komanso onse mumpingo?

9 Woyang’anira sukulu amapatsa uphungu wophunzira aliyense pamene mpingo wonse ukumvetsera, kuti enanso limodzi ndi mlankhuliyo apindule nawo uphunguwo. Kuyamikira kumakhala koyenera nthaŵi zonse. Ndipotu phunguyo adzakhala ndi chidwi chofuna kukulimbikitsani. Uphungu wothandiza udzaperekedwa pa mfundo zakutizakuti zondandalikidwa pa silipi la Uphungu wa Kulankhula, mfundo zimene inu mwapemphedwa kugwirirapo ntchito. (Onani tsatanetsatane wake m’Phunziro 20.) Woyang’anira sukulu adzayesetsa kudziŵa zosoŵa zanu panokha monga wophunzira, ndipo adzakhala wofunitsitsa kuona kupita kwanu patsogolo.

10 Alinso ndi chidwi chofuna kuonetsetsa kuti onse mumpingo akupindula ndi gawo lililonse la sukuluyo. Adzakulimbikitsani kuti mutengemo mbali malinga ndi kukhoza kwanu, kuyankhapo pa kubwereramo kwapakamwa kwa nthaŵi zonse komanso kumatenga mbali pakubwereramo kolemba kwa nthaŵi ndi nthaŵi. Ngati simunalembetse, adzakulimbikitsani kutero, komanso adzakuthandizani pazovuta zanu ndi kukusonyezani mmene inunso mungakhalire wotamanda Yehova wogwira mtima.

11 Woyang’anira Sukulu ya Utumiki Wateokalase alinso ndi mwayi wokuthandizani monga wophunzira wolembetsa ngati mukufuna chithandizo pankhani zanu, akumafika kunyumba kwanu pamene kuli kotheka. Ngati walephera kupeza nthaŵi yabwino yoti achite zimenezo, adzapempha abale achikulire mwauzimu ndi alankhuli achidziŵitso kuti akuthandizeni. Inunso makolo, mutha kuthandiza mwa kupereka chithandizo choterocho kwa ana anu, osati kuwakonzera nkhani, koma kupereka malingaliro ndi njira zofufuzira kuti akonzekere bwino. Ngati mukuphunzitsa wofalitsa watsopano mu utumiki wakumunda, mungapemphedwe kuthandiza ameneyo kukonzekera nkhani zake m’sukulu yateokalase.

12 Laibulale ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase pa Nyumba ya Ufumu imayang’aniridwa ndi woyang’anira sukulu. Iye adzathandiza atsopano kuwasonyeza mmene angapindulire ndi nkhokweyo ya chidziŵitso cha Baibulo. Ayenera kuyesetsa kuti m’mashelufu mukhale mabuku onse aposachedwapa a Sosaite, kudzanso mabuku ena oonamo, akuti ophunzira ndi ena azigwiritsa ntchito.

13-17. Kodi kupita patsogolo kwa ophunzira kumaonekera motani kwa ena?

13 Mapindu kwa ophunzira. Pamene mupatsidwa nkhani m’sukulu, ilandireni mwachidwi monga yochokera kwa Yehova kudzera m’gulu lake. Mofananamo, landirani ndi kugwiritsa ntchito modzichepetsa uphungu woperekedwa. Malingaliro amene phunguyo akupatsani mungawagwiritse ntchito ponse paŵiri pamene mulankhula masiku onse ndinso mu utumiki wanu. Mwa kuyesetsa mwakhama kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito chidziŵitso choperekedwa m’sukulu imeneyi, mudzapindula kwenikweni.

14 Amene amapezekapo mokhazikika pa pologalamu ya sukulu ndi kutengamo mbali amaona kuti mayankho awo pamisonkhano amawongokera kwambiri, ndipo utumiki wawo wakumunda umakhala wogwira mtima kwambiri. Sukuluyo imaphunzitsanso ophunzira achimuna kakonzekeredwe ndi kakambidwe ka nkhani kamene kamalimbikitsa ndi kusonkhezera omvetsera, kaya ndi pamsonkhano wautumiki kapena nkhani zapoyera. Ambiri, chifukwa cha kuphunzira pa Sukulu ya Utumiki Wateokalase, akhala okhoza kupereka chifukwa chabwino chodzikanira pamaso pa mabwalo a milandu ndi olamulira, pamenenso ena akhoza kulankhula pasukulu kapena pamaso pa magulu a anthu.

15 Pamene wophunzira agwiritsa ntchito uphunguwo pakulankhula kwake kwa masiku onse, adzapezanso kuti m’kupita kwa nthaŵi, zizoloŵezi zokhomerezeka mozama za malankhulidwe osayenera zidzazimiririka. Kaya kukhale kuntchito, kusukulu kapena kwina kulikonse, kuphunzira kwathu monga Mboni za Yehova kumaonekera msanga kwa otiona. Zili ngati mmene magazini ina yotchuka inanenera kuti: “Pamiyezi yoŵerengeka chabe, Mboni zatsopano zimaphunzira Baibulo kwambiri kuposa mmene Akristu ochuluka amachitira kwa moyo wawo wonse. Ndipo sizimachitika mwangozi kuti pafupifupi zonse zimakhala alankhuli osadodoma ndi aluso.”

16 Ndi bwino kuti aliyense wa ife mumpingo akhale ndi cholinga kuti tidziŵe mmene tikupitira patsogolo mu utumiki. Tingalinganize zolinga zimenezo malinga ndi mmene tikupitira patsogolo m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Mwachitsanzo, kodi mukuona kuti mumakhala ndi vuto kuti mubwerere kwa okondwerera kuyankha mafunso awo? Nkhani zambiri zimene zimaperekedwa ndi zitsanzo pasukulu zili zothandiza m’mikhalidwe imeneyo.

17 Kuti mupeze phindu lalikulu, musaone sukuluyo ngati maphunziro wamba a mphindi 45 a mlungu ndi mlungu. M’malo mwake, ngati muli wophunzira wakhama, mudzafuna kutsatira pologalamu ya kuphunzira ndi kukonzekera kunyumba, kuphatikizapo kuŵerenga Baibulo ndi kufufuza kwina kofunikira. Si ophunzira okamba nkhani okha amene adzapeza chidziŵitso ndi luso monga atumiki a Yehova, koma tonsefe osonkhana pa misonkhano ya sukulu tidzatero ngati tikonzekera phunziro la mlunguwo pasadakhale.

18-20. Pamene tili opereŵera paluso linalake, n’chifukwa chiyani sitiyenera kulola zimenezo kutiletsa kutenga mbali mokwanira m’sukuluyo?

18 Tonsefe tikulimbikitsidwa kuchita zonse zotheka, tisakuiŵala cholinga chenicheni cha sukuluyo. Sindicho kuonetsera luso lathu la kulankhula. Kapena kuonetsa zofooka ndi zolephera za ena. Ndithudi, ukulu wa phindu limene mudzapeza m’sukulu udzadalira cholinga chathu chotengera mbali m’sukulu imeneyi. Iyo ndi gawo la maphunziro ochokera kwa Yehova. Iye akutiphunzitsa ndi kutilangiza za chifuniro chake. Wophunzira aliyense asade nkhaŵa ndi mmene ena angamuonere, pakuti sitikuyesa kukondweretsa anthu kapena kutsatira miyezo ya anthu ya kaphunzitsidwe ndi kalankhulidwe. Nkhani kwa ife yagona pa kupeza chiyanjo cha Yehova ndi dalitso lake pa ntchito yathu yautumiki.

19 Zoona, abale ndi alongo ena angamve mmene anamvera Mose pamene anati kwa Yehova: ‘Ine sinditha kulankhula bwino, ngakhale kuyambira dzulo ngakhale kuyambira kale.’ (Eks. 4:10) Koma ngati muli ndi chikhulupiriro chakuti palibe chosatheka ndi Mulungu, mudzagonjetsa malingaliro amenewo. (Mat. 19:26) Ndiponso, dziŵani kuti kupita patsogolo kulikonse paluso lanu la kulankhula Mawu a moyo kuli ndi phindu lake. Ngakhale kupita patsogolo kwakung’ono kungachititse munthu wina kuloŵa panjira ya ku moyo, nanga chimenecho si chinthu chosangalatsa?

20 Cholinga chachikulu cha Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndicho kuphunzitsa ntchito yautumiki. Khalanitu mmodzi mwa anthu ambirimbiri amene mokhazikika amapezekapo ndi kufunafuna mapindu ake, ndiyeno Yehova adalitsetu zoyesayesa zanu za kupita patsogolo.—Afil. 3:16.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena