Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/99 tsamba 2
  • Bokosi la Mafunso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Bokosi la Mafunso
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Malangizo kwa Oyang’anira Sukulu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1999
km 4/99 tsamba 2

Bokosi la Mafunso

● Kodi payenera kupita nthaŵi yaitali motani kuti wophunzira apatsidwenso nkhani ina m’Sukulu ya Utumiki Wateokalase?

Chimodzi cha zolinga zazikulu za Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndi kuphunzitsa okamba nkhani zapoyera. Pachifukwa chimenechi, Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki Wateokalase imakhala ndi nkhani zambiri zoyenera kukambidwa ndi abale.

Komabe, cholinga china chofunika cha sukuluyi ndi kuphunzitsa anthu a Yehova onse kukhala alaliki ndi aphunzitsi abwino mu utumiki wachikristu. N’chifukwa chake kuli koyeneranso kuti alongo azilembetsa m’sukuluyi.

Kuti apindule kwambiri ndi sukuluyi, onse amene analembetsa ayenera kumalandira nkhani za ophunzira nthaŵi ndi nthaŵi. Tikupereka lingaliro lakuti wophunzira aliyense azipereka nkhani patatha miyezi itatu. Ngati kwanuko zingatheke, abale angapatsidwe nkhani zowonjezeka. Sikoyenera kuti akulu amene amapereka nkhani yachilangizo ndi mfundo zazikulu za Baibulo azipatsidwanso nkhani za ophunzira.

Kwazaka pafupifupi theka la zana, Sukulu ya Utumiki Wateokalase yathandiza mamiliyoni a anthu kupita patsogolo mwauzimu ndiponso kudziŵa kulankhula bwino polalikira uthenga wa Ufumu. Onse akulimbikitsidwa kugwiritsa ntchito bwino makonzedwe apadera a Yehova Mulungu ameneŵa. Cholinga chathu chiyenera kukhala chakuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu, antchito ‘opanda chifukwa cha kuchita manyazi, olunjika nawo bwino mawu a choonadi.’—2 Tim. 2:15.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena