Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Sukulu Yautumiki Wateokratiki
1 Woyang’anira Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi mkulu wauzimu amene amagwira ntchito kwambiri pa mawu ndi kuphunzitsa ndiponso tiyenera kumlemekeza ndi kugwirizana naye. (1 Tim. 5:17) Kodi ntchito yake njotani?
2 Laibulale ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki pa Nyumba ya Ufumu imayang’aniridwa ndi iyeyu. Amakonda kwambiri kulimbikitsa aliyense amene ali woyenerera kuti alembetse mu sukulu. Amaonetsetsa kuti walemba molongosoka nkhani zasukulu ndi maina a ophunzira kotero kuti azipatsa anthu nkhani mwadongosolo milungu itatu sukulu iliyonse isanachitike. Amafunika kuudziŵa bwino mpingo, akumalingalira za wophunzira aliyense ndi maluso ake. Ngakhale kuti angakhale ndi mbale wina womthandiza kukonza ndandanda ya sukulu, kugaŵira anthu nkhani moyenerera kumafuna kuti woyang’anira iye mwini ayang’anire zimenezo.
3 Kuti aphunzitse mogwira mtima pasukuluyo, woyang’anira afunika kukonzekera mwakhama mlungu uliwonse, akumaphunzira mosamalitsa nkhani zogaŵiridwazo. Zimenezi zimamtheketsa kuti azipangitsa mpingo kukhala ndi chidwi mu zimene zikuphunziridwa, kuona ngati nkhani yogaŵiridwa yalongosoledwa bwino, ndi kutchula mfundo zofunika zimene zidzaphatikizidwa pa kubwereramo kolemba.
4 Wophunzira aliyense atakamba nkhani yake, woyang’anira amayamikira wophunzirayo ndi kulongosola chifukwa chake mkhalidwe wina wa kulankhula unali bwino kapena chifukwa chake ukufunikira kuwongoleredwa. Pamene wina akufunikira kuphunzitsidwa zina zambiri za mmene angakonzekerere nkhani zake za m’sukulu, woyang’anira kapena wina wouzidwa ndi iye angamthandize payekha.
5 Kuti tipindule mokwanira ndi ntchito yakhama ya woyang’anira Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi alangizi ena alionse amene amatumikira motsogozedwa ndi iye, tifunikira kumapezeka pa sukulu mokhazikika. Tifunikiranso kukamba nkhani zimene timagaŵiridwa ndi kugwiritsira ntchito uphungu umene timalandira ndiponso umene umaperekedwa kwa ophunzira ena. Mwa njirayi, tidzapititsabe patsogolo maluso athu akulalikira uthenga wa Ufumu poyera ndiponso kunyumba ndi nyumba.—Mac. 20:20; 1 Tim. 4:13, 15.