Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/96 tsamba 7
  • Kulembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu Yopambana Yapadziko Lonse
    Galamukani!—1996
  • Sukulu ya Utumiki Wateokalase Imapindulitsa
    Buku Lolangiza la Sukulu ya Utumiki Wateokalase
  • Sukulu Imene Imatikonzekeretsa Kuchita Zinthu Zimene Zili Zofunika Kwambiri
    Utumiki wathu wa Ufumu—2002
  • Malangizo kwa Oyang’anira Sukulu
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 12/96 tsamba 7

Kulembetsa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki

1 Sukulu Yautumiki Wateokratiki yakhala yothandiza kwambiri pakuphunzitsa miyandamiyanda ya Mboni za Yehova monga atumiki a uthenga wabwino. Ambiri a ife tikukumbukira mantha amene tinali nawo ndi kusakwanira kumene tinali kumva nthaŵi yoyamba pamene tinalembetsa m’sukulu imeneyi, ndipo tsopano tikuvomereza moyamikira kuti latithandiza kukula mwauzimu monga alankhuli ndi aphunzitsi a Mawu a Mulungu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 4:13.) Kodi mwalembetsa m’sukulu yapadera imeneyi?

2 Kodi ndani ayenera kulembetsa? Tsamba 73 la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu limayankha kuti: “Onse amene agwirizana ndi mpingo mokangalika angalembetse, kuphatikizapo anthu ofika pamisonkhano chatsopano, malinga ngati iwo sakukhala ndi moyo umene uli wosagwirizana ndi ziphunzitso zachikristu.” Tikuitanira onse oyeneretsedwa—amuna, akazi, ndi ana—kufikira woyang’anira sukulu ndi kupempha kuti mulembetse.

3 Programu ya Sukulu ya 1997: Programu ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1997 ili ndi ziphunzitso zambiri zosiyanasiyana ndi mbali zosiyanasiyana za kulinganizidwa kwa mpingo. Kuwonjezera pa kukulitsa maluso athu a kulankhula ndi kuphunzitsa, timatengapo phunziro pa ngale zauzimu zambiri zopezeka m’programu yake ya mlungu uliwonse. (Miy. 9:9) Ngati tikonzekera sukulu, kumene kumaphatikizapo kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu, ndipo timasonkhana mokhazikika, programuyi ingatipindulitse kwambiri mwauzimu.

4 Mu 1997 mbali zambiri za kuŵerenga Baibulo m’Nkhani Na. 2 nzazifupi kuposa za m’zaka zapita. Pokonzekera nkhani imeneyi, wophunzira ayenera kulinganiza nthaŵi imene adzaiŵerengeramo ndiyeno kuona kuti ndi zingati za mphindi zisanu za nkhani yake zimene angagwiritsire ntchito pa mawu oyamba ndi mawu omaliza. Zimenezi zidzalola wophunzirayo kugwiritsira ntchito nthaŵi yake yonse ndi kukulitsa luso lake la kuŵerenga ndi la kulankhula nkhani mosayang’ana pa autilaini.—1 Tim. 4:13.

5 Umboni wamwamwaŵi waikidwapo kukhala mkhalidwe wotheka m’maulaliki a m’Nkhani Na. 3, amene azikidwa pa buku la Chidziŵitso. Choncho, mlongo angasankhe kaya ulendo wobwereza, phunziro la Baibulo lapanyumba, kapena umboni wamwamwaŵi monga mkhalidwe wa nkhaniyi. Komabe, chimene chiyenera kugogomezeredwa kwambiri nthaŵi zonse ndicho kaphunzitsidwe kogwira mtima ndipo osati mkhalidwe wake.

6 Kaya muli ndi mwaŵi wa kupereka nkhani ya chilangizo, mfundo zazikulu za Baibulo, kapena nkhani ya wophunzira, mungasonyeze kuyamikira kwanu Sukulu Yautumiki Wateokratiki mwa kukonzekera ndi kuyeseza bwino nkhani yanu, mwa kuipereka motsimikiza mtima ndi mogwira mtima, mwa kusadya nthaŵi, mwa kumvetsera ndi kugwiritsira ntchito uphungu wa woyang’anira sukulu, ndi mwa kuyesetsa kukwaniritsa mbali yanu mokhulupirika nthaŵi zonse. Chotero kulembetsa kwanu m’sukuluyi kudzakhala dalitso ponse paŵiri kwa inu ndi kwa onse opezekapo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena