Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/96 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 12/96 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu December: New World Translation ndi buku la Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1984 isanafike limene mpingo ungakhale nalo m’stoko. Mipingo imene ilibe mabuku ameneŵa ingagaŵire Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano February: Gwiritsirani ntchito buku lililonse lamasamba 192 lakale. March: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

◼ Mipingo iyenera kuyamba kuoda mabaundi voliyumu a The Watchtower ndi Awake! a 1996 pa oda yawo ya mabuku ya December. (Onani Mpambo wa Zofalitsa za Watch Tower, ndime 7, 19-21.) Mabaundi voliyumu adzakhalapo m’Chingelezi. Mpaka pamene mabaundi voliyumu adzakhalapo ndi kutumizidwa, ameneŵa adzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mpambo wolongedzera katundu wa mipingo. Mabaundi voliyumu ndi zinthu za oda yapadera.

◼ Woyang’anira wotsogoza kapena wina wosankhidwa ndi iye ayenera kupenda maakaunti a mpingo pa December 1 kapena mwamsanga pambuyo pake. Perekani chilengezo ku mpingo pamene zimenezi zachitidwa.

◼ Tsopano mungamatenge mabuku ndi katundu wina wa mpingo ku nyumba ya Amishonale imene ilinso depo ya Sosaite yoyang’anizana ndi pomwetsera mafuta galimoto ku Namiwawa ku Blantyre. Choncho, depoyo idzakhala yotseguka Lachiŵiri ndi Lachinayi lililonse mmaŵa kuyambira pa 7:30 a.m. mpaka 12 masana. Chonde musapite kukatenga katundu panthaŵi ina iliyonse mkati mwa mlungu.

◼ Chikumbutso cha mu 1998 chidzakhalako pa Loŵeruka, April 11, dzuŵa litaloŵa. Tsiku la phwando la Chikumbutso cha mu 1998 laperekedwa pasadakhale kotero kuti abale apangiretu makonzedwe a malo osonkhanira m’maholo amene alipo kumene kuli mipingo yambiri imene imagwiritsira ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo iyenera kupeza malo ena.

◼ Chifukwa chakuti chochitikacho nchofunika, posankha wokamba nkhani ya Chikumbutso, bungwe la akulu liyenera kusankha mmodzi wa akulu oyeneretsedwa kwambiri m’malo mongosinthana kapena kugwiritsira ntchito mbale mmodzi ndi mmodzi chaka chilichonse.

◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:

Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku ka 1997—Chicheŵa, Chingelezi

Mboni za Yehova ndi Maphunziro—Chicheŵa, Chingelezi

Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?—Chicheŵa

Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako—Chicheŵa, Chingelezi

Mabaundi voliyumu a Watchtower a 1992—Chingelezi

Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1997—Chicheŵa, Chingelezi,

Mapulasitiki a Mabaji

◼ Makaseti Omvetsera Omwe Alipo:

Imbirani Yehova Zitamando (Alubamu imodzi yokhala ndi makaseti 8)—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena