Kupenda Kolemba m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki
Kupenda kolemba mabuku atatsekedwa pankhani zokambidwa m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki zogaŵiridwa kuyambira mlungu wa September 2 kufikira December 23, 1996. Gwiritsirani ntchito pepala lina kuti mulembepo mayankho ambiri othekera m’nthaŵi yoperekedwa.
[Tamverani: Mkati mwa kupendaku, gwiritsirani ntchito Baibulo lokha kuyankhira funso lililonse. Magwero a nkhani amene amaikidwa pambuyo pa mafunso ngoti mukadzifufuzire. Manambala a tsamba ndi ndime nthaŵi zonse sangasonyezedwe m’magwero onse a mu Nsanja ya Olonda.]
Yankhani kuti Zoona kapena Kunama m’ndemanga zotsatirazi:
1. “Chilombo” cha mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi chosonyezedwa pa Chivumbulutso 13:1 ndicho Satana Mdyerekezi osatinso wina ayi. [uw-CN tsa. 63 ndime 4]
2. Pamene Yesu anapemphera kuti: “Atate, mukafuna inu, chotsani chikho ichi pa ine,” anali kupempha kupulumutsidwa ku imfa. (Luka 22:42) [gt-CN mutu 117]
3. Satana mwamachenjera amakopa anthu kuti akhutiritse zikhumbo zawo zachibadwa m’njira zolakwa. [uw-CN tsa. 65 ndime 9]
4. Ulosi wa pa Danieli 9:24, 25 umanena za kubadwa kwa Yesu. [kl-CN tsa. 36 ndime 8]
5. Sheol, Hade, ndi Gehena zonse zimaloza ku manda a anthu onse. [uw-CN tsa. 72 ndime 6]
6. “Olamulira a dziko” otchulidwa pa Aefeso 6:12, NW, ndiwo olamulira a ndale olekanitsidwa ndi chiyanjo cha Mulungu. [uw-CN tsa. 63 ndime 4]
7. Yesu anadzudzula ophunzira ake chifukwa cha kumfunsitsitsa za mafanizo amene anapereka ku Nyanja ya Galileya. [gt-CN mutu 43, ndime 21, 22, 25]
8. Kudya thupi la Yesu ndi kumwa mwazi wake kumatanthauza kusonyeza chikhulupiriro kwa munthu m’nsembe yake ya dipo. [gt-CN mutu 55]
9. Malinga ndi Zefaniya 3:9, anthu a Mulungu adzagwirizana m’dziko latsopano chifukwa onse adzalankhula chinenero chimodzi—Chihebri. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 6/1 tsa. 30.]
10. Kukwaniritsa Danieli 12:1, Mikayeli wakhala “akuimirira” kuyambira 1914 pamene anakhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba wa Mulungu; posachedwapa “adzaima” m’dzina la Yehova monga Wankhondo ndi Mfumu yosagonjetseka, kudzetsa chiwonongeko pa dongosolo ili loipa. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w93-CN 11/1 tsa. 23 ndime 23.]
Yankhani mafunso otsatirawa:
11. Kodi “zofunika za amitundu onse” zotchulidwa pa Hagai 2:7 ndani, ndipo ‘zikufika’ motani? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 6/1 tsa. 31 ndime 5.]
12. Kodi “chikhazikiro chake cha dziko lapansi” chinachitika liti? [gt-CN mutu 111]
13. Ngati Nisani 11, 33 C.E., anatha dzuŵa litaloŵa pa Lachiŵiri, ndi liti pamene Nisani 14 anayamba ndi kutha? [gt-CN mutu 112]
14. Kodi nchifukwa ninji ntchito zamphamvu zochitidwa m’dzina la Yesu sizingakhale umboni wotsimikiza wa chiyanjo cha Mulungu kapena chichirikizo chake? [kl-CN tsa. 46 ndime 6-7]
15. Kodi ndi m’njira yotani imene ophunzira a Yesu anali kudzachitira ntchito zoposa zimene iye anachita, malinga ndi kunena kwake pa Yohane 14:12? [gt-CN mutu 116 ndime 6]
16. Kodi nchifukwa ninji Yesu ananena kuti walilaka dziko lapansi pa Yohane 16:33? [gt-CN mutu 116 ndime 37]
17. Kodi nchifukwa ninji Yohane Mbatizi anakuona kukhala koyenera kuvumbula ukwati wachigololo wa Herode Antipa ndi Herodiya amene sanali Ayuda? [gt-CN mutu 51]
18. Mogwirizana ndi Aefeso 5:3-5, kodi ndi pa maziko otani amene Mkristu wozindikira adzakanira nyimbo zina zimene zingakhale ndi malimba okondweretsa, maimbidwe okoma, kapena maliridwe osonkhezera? [uw-CN tsa. 67 ndime 12]
19. Pa Hagai 2:9, kodi ndi kachisi uti amene anali “nyumba iyi,” nanga ‘yoyambayo’ inali iti, ndipo nchifukwa ninji ulemerero wa “nyumba iyi” unali waukulu kuposa wa ‘yoyambayo’? [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w89-CN 6/1 tsa. 30.]
20. Kodi Hoseya 14:2 anali kulimbikitsa Aisrayeli kuchitanji, ndipo ndi motani mmene Mboni za Yehova zikukwaniritsira ulosiwo lerolino? (Aheb. 13:15) [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w94-CN 9/15 tsa. 10 ndime 1-2.]
Perekani liwu kapena mawu ofunika kutsiriza ndemanga zotsatirazi:
21. Pamene Yesu anaweruzidwa mosalungama, ․․․․․․․․ anali bwanamkubwa wa Yudeya, ndipo ․․․․․․․․ anali wolamulira wa Galileya. [gt-CN mitu 121, 122]
22. Tifunikira kulambira Mulungu ․․․․․․․․, tikumasonkhezeredwa ndi mtima wodzala chikhulupiriro ndi chikondi; tiyeneranso kumlambira ․․․․․․․․ mwa kuphunzira Mawu ake. [kl-CN tsa. 45 ndime 4]
23. Ophatikizidwa m’pangano latsopano ndiwo ․․․․․․․․ ndi ․․․․․․․․. [gt-CN mutu 114]
24. Chifuno chachikulu chimene Yesu anadzera padziko lapansi chinali ․․․․․․․․. [gt-CN mutu 122]
25. Mbali zitatu za umboni wosonyeza kuti Yesu anali Mesiya ndizo (1) ․․․․․․․․, (2) ․․․․․․․․, ndi (3) ․․․․․․․․. [5-8, kl-CN mas. 34-8 ndime 6-10]
Sankhani yankho lolondola m’ndemanga zotsatirazi:
26. Pamlandu wa mbali zitatu umene atsogoleri achipembedzo achiyuda anaimba Yesu, malinga ndi zimene zalembedwa pa Luka 23:2, mlandu umene Pilato anada nawo nkhaŵa kwambiri unali wakuti Yesu (anali kupandutsa mtundu wa Ayuda; anali kuletsa kupereka msonkho kwa Kaisara; anali kunena kuti iye mwiniyo ndiye Kristu mfumu). [gt-CN mutu 121]
27. Aja amene amavomereza Baibulo samalambira Utatu chifukwa chakuti (Aigupto akale analambira milungu yambiri; Yehova Mulungu ndiye mmodzi; unatha ndi imfa ya Kristu). [kl-CN tsa. 30 ndime 22]
28. “Masabata” 69 a pa Danieli 9:24, 25 anali autali wa zaka (455; 690; 483). [kl-CN tsa. 36 ndime 8]
29. Yoweli 2:32 anagwidwa mawu ndi (Petro; Yohane; Paulo) pa (Machitidwe 2:40; Aroma 10:13; 1 Timoteo 2:4), pamene akugogomezera kufunika kwa kuitana pa dzina la Yehova. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 4/1 tsa. 20 ndime 16.]
30. Chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu woona chimatitetezera (kuti kulambira kwathu kusaipitsidwe; kuti tisagwidwe ndi matenda a mtundu uliwonse; kwa aja amene amatida). [kl-CN tsa. 47 ndime 9]
Gwirizanitsani malemba otsatirawa ndi ndemanga zondandalikidwa pansipa: Hos. 10:12; 1 Yoh. 2:15-17; Yoh. 13:1-17; Yak. 1:26, 27; Mat. 26:52
31. Kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa Mulungu, kuyenera kukhala osati chabe kosadetsedwa ndi machitachita a dziko komanso kophatikizapo zonse zimene Mulungu amaona kukhala zofunika kwambiri. [kl-CN tsa. 51 ndime 20]
32. Mwa kuchita chabwino m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, tidzatuta kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova. [Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu; onani w96-CN 3/15 tsa. 23 ndime 2-3.]
33. Akristu oona saali mbali ya dziko; chotero, samanyamula zida za nkhondo. [gt-CN mutu 118; onani w94-CN 6/1 tsa. 12.]
34. Monga Akristu oona, tiyenera kupeŵa machitachita alionse amene amasonyeza mzimu wa dziko lotizinga lopanda umulungu. [kl-CN tsa. 50 ndime 17]
35. Monga Akristu tiyenera kukhala okonzekera kutumikira ena popanda tsankhu, mosasamala kanthu za mmene ntchitoyo ingakhalire yapansi kapena yosakondweretsa. [gt-CN mutu 113]
S-97-CN Mal, Moz & Zam #290b 12/96