Kukondwera ndi Chiwonjezeko Chimene Mulungu Akupereka
1 Akristu m’zaka za zana loyamba anali alaliki a Ufumu achangu. Iwo anakondwera pamene ‘mipingoyo inachuluka m’chiŵerengo chawo tsiku ndi tsiku.’ (Mac. 16:5) Ulaliki wawo wolimba mtima unafalikira kuloŵa m’Asia, Ulaya, ndi Afirika, chotero anatuta okhulupirira ochuluka.
2 Yesu analosera kuti m’masiku otsiriza, ntchito yolalikira idzafika ‘padziko lonse lapansi ndi ku mitundu yonse’! (Mat. 24:14) M’chaka chautumiki cha 1996, tinapitiriza kulandira malipoti a ziwonjezeko zazikulu ndi ziŵerengero zapamwamba zatsopano za ofalitsa kuchokera ku maiko kuzungulira dziko lonse. Mipingo yambiri yatsopano yapangidwa. Chiwonjezeko chofulumira chimenechi chachititsa kuti Nyumba za Ufumu ndi Nyumba za Misonkhano mazana ambiri zimangidwe ngakhalenso kufutukula nthambi zingapo.
3 Utumiki Wathu Waufumu wa August 1996 unasimba za ntchito yaikulu yomanga imene ikuchitika mu Afirika. Ntchito yofanana ikuchitika ku Latin America yense. M’chaka chautumiki cha 1996, Mexico anali ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa 470,098 ndi avareji ya maphunziro a Baibulo 600,751, zofuna kupangidwa kwa mipingo 466 yatsopano! Ntchito yofutukula nthambi yawo ikuyembekezeredwa kutha chakumapeto kwa 1998. Chiwonjezeko chofanana m’maiko ena ambiri sichikulola kuti ntchito zosiyanasiyana zateokrase zomanga ziime.
4 Kulikonse mtengo womangira uli wokwera, ndipo abale athu m’maiko ambiri ali ndi zochepa zimene angapereke mwakuthupi. Komabe, chifukwa cha changu chawo chachikulu cha utumiki wa Yehova, iwo akukuladi mwauzimu ndipo ziŵerengero zawo zikukwera kwambiri. Miyambo 28:27 ikutitsimikiza kuti “wogaŵira aumphaŵi sadzasoŵa.” Kufunitsitsa kwathu kuwathandiza kulipirira zimenezi ndi ndalama zomangira kumachititsa kuti pakhale “kulingana” kwa zinthu zakuthupi, ndi kutheketsa onse kupeza chimwemwe chimene chimadza mwa kupatsa ndi chisangalalo chimene chimadza poona chiwonjezeko chimene Yehova akupereka!—2 Akor. 8:14, 15; Mac. 20:35.
[Chithunzi pamasamba 4, 5]
Nthambi ya Paraguay
[Chithunzi patsamba 4]
Nthambi ya Ecuador
[Chithunzi pamasamba 4, 5]
Nyumba Yowonjezera ya Mexico Ikumangidwa
[Chithunzi pamasamba 4, 5]
Nthambi ya Dominican Republic
[Chithunzi patsamba 4]
Nthambi ya Brazil ndi Nyumba Yowonjezera
[Chithunzi pamasamba 4, 5]
Nthambi ya Uruguay Ikumangidwa
[Zithunzi patsamba 5]
Nyumba za Ufumu za mtengo wotsika zofala ku Latin America
1. Brazil
2. Nicaragua
3. Chile
4. Colombia
5. Mexico
6. Brazil
7. Peru
8. Venezuela
9. Mexico