Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/96 tsamba 2
  • “Thandizo Panthaŵi Yake”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Thandizo Panthaŵi Yake”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Nkhani Yofanana
  • Londolani Mtendere Waumulungu m’Moyo wa Banja
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Kuuzako Ena Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Kuthandiza Mabanja Kumanga Mtsogolo Mokhalitsa
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Amithenga a Mtendere Waumulungu Asonkhana
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
km 12/96 tsamba 2

“Thandizo Panthaŵi Yake”

1 Nkosangalatsa chotani nanga kulandira thandizo panthaŵi imene tikulifuna! (Aheb. 4:16, NW) Pamsonkhano Wachigawo wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu,” tinasangalala pamene tinapatsidwa zogaŵira ziŵiri zapadera zothandiza panthaŵi yakedi.

2 Buku latsopanolo, Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, linabwera panthaŵi yoyenera. Kwenikweni, likufotokoza zofunika zinayi zimene zimalimbikitsa moyo wa banja wachimwemwe: (1) Kudziletsa, (2) kuzindikira umutu, (3) kulankhulana kwabwino, ndi (4) chikondi. Uphungu woperekedwa m’buku la Chimwemwe cha Banja udzathandiza mabanja onse amene adzaugwiritsira ntchito kupeza mtendere waumulungu. Patulani nthaŵi ya kuŵerenga buku latsopanolo mosamalitsa ndi kuliphunzirira pamodzi monga banja. Zidziŵeni bwino zamkati mwake kotero kuti mukakhale wokonzeka kuligwiritsira ntchito mogwira mtima pamene lidzagaŵiridwa kwa anthu kwa nthaŵi yoyamba, m’March.

3 Brosha latsopano, Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?, lafika panthaŵi yabwino kuti lithandizire kufulumiza ntchito yathu yopanga ophunzira. Pamene kuli kwakuti lingagwiritsiridwe ntchito kwenikweni kuthandiza anthu amene sadziŵa kwambiri kuŵerenga, achikulire ndi ana aang’ono ambiri odziŵa kuŵerenga, adzapindulanso ndi mafotokozedwe ake osavuta kumva a ziphunzitso zoyambirira za Baibulo. Lingakhale zimene zikufunika kwenikweni poyambitsa phunziro monga njira yotsogolera ku buku la Chidziŵitso. Chogaŵira chimenechi chidzathandizadi enanso ambiri kuzindikira mmene angadalitsidwire kwambiri mwa kuchita zimene Mulungu amafuna.

4 Kodi ‘thandizo la panthaŵi yake’ lachikondi la Yehova likutimvetsa bwanji? Davide anafotokoza malingaliro athu molondola kwambiri pamene analengeza kuti ‘sanasoŵe kanthu, moyo wake unatsitsimulidwa, ndipo chikho chake chinasefuka!’ (Sal. 23:1, 3, 5) Mwachimwemwe tikuyembekezera kugaŵa thandizo lauzimu labwino kwambiri limeneli kwa ena ambiri amene moona mtima akukhumba kumdziŵa ndi kumtumikira Mulungu woona, Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena