Kuuzako Ena Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
1 Banja Ndilo Kagulu Ka Anthu, Ndipo Mabanja Ambiri Amapanga Midzi, Mizinda, Maboma, Ndi Mitundu. Lero Banja Lili Pamavuto Amene Silinaonepo Kale. Pali Zododometsa Zambiri Zomwe Zikusokoneza Chimwemwe Cha Banja. Tikuyamikira Chotani Nanga, Kuti Yehova, Mkonzi Wa Banja, Watipatsa Malangizo Otithandiza Kupeza Chimwemwe Pabanja! Amene Amatsatira Zitsogozo Zake Amaona Kuti Mavuto Amachepa Ndipo Amakhala Ndi Banja Labwino. M’mwezi Uno Wa September Tili Ndi Mwaŵi Wogaŵira Ena Buku Lakuti Chinsinsi Cha Chimwemwe Cha Banja. Yambirirani Ndinu Kuwafikira Anthu Ndi Nkhani Ya Moyo Wabanja. Khalani Waubwenzi, Wotsimikiza, Ndi Wozindikira. Kodi Munganenenji?
2 Mungayambe mwa kufunsa funso longa ili:
◼ “Kodi mukuona kuti mabanja ambiri akulephera kupirira mavuto pa moyo wawo? [Yembekezerani yankho.] Malipoti akusonyeza kuti anthu ambiri ali m’mavuto panyumba. Kodi mukuganiza kuti nchiyani chimene chingathandize mabanja kuti akhale olimba ndi kupeza chimwemwe? [Yembekezerani yankho.] Popeza ndi Mulungu anayambitsa banja, kodi sikwanzeru kugwiritsira ntchito zitsogozo zimene watipatsa? [Ŵerengani 2 Timoteo 3:16, 17.] Malangizo opindulitsa amenewo andandalikidwa m’buku lino, lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.” Ndiyeno mfunseni munthuyo limene akuganiza kuti ndilo vuto lofala pabanja, m’sonyezeni mutu umene ukunena za vuto limenelo, ndipo perekani bukulo pa chopereka cha K12.00.
3 Paulendo wobwereza, mungakhale ndi cholinga choyambitsa phunziro la Baibulo mwa kunena kuti:
◼ “Ndalingalira zimene munanena pankhani ya moyo wabanja, ndiye ndakubweretserani kanthu kena kamene ndikuganiza kuti mungakondwere nako. [Sonyezani brosha la Mulungu Amafunanji, pitani patsamba 16, ndi kuŵerenga mafunso asanu ndi limodzi ali pamwamba.] Nzachidziŵikire kuti aliyense m’banjamo ayenera kuchita mbali yake kuti banjalo likhale lachimwemwe. Ngati muli ndi mphindi zoŵerengeka chabe, ndingakusonyezeni mmene mungapindulire kwambiri ndi chidziŵitso chimenechi.” Ndiyeno yambani kuphunzira phunziro 8.
4 Njira ina yoyambira makambitsirano ndiyo yongotchula vuto lina, mwina mwa kunena kuti:
◼ “Ngakhale kuti aliyense amafuna kukhala ndi mtendere wa maganizo, zikuoneka kuti mabanja ambiri samaupeza nkomwe. Mukuganiza kuti nchiyani chimene chingawathandize kupeza chimwemwe chenicheni? [Yembekezerani yankho.] Kalekale, Baibulo linavumbula mtundu wa mavuto amene tizikumana nawo m’mabanja lero. [Ŵerengani 2 Timoteo 3:1-3.] Komabe, Baibulo limauzanso mabanja zimene ayenera kuchita kuti athetse mavuto ameneŵa ndi kupeza chimwemwe chokhalitsa. Mapulinsipulo ake afotokozedwa m’buku lino, lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.” Ndiyeno msonyezeni bokosi la kubwereramo kumapeto a mutuwo, liŵerengeni, ndipo gaŵirani bukulo pa chopereka cha K12.00.
5 Pamene mwabwererako, gwiritsirani ntchito brosha la “Mulungu Amafunanji” kuti muyambe phunziro. Munganene kuti:
◼ “Ndinasangalala ndi kufunitsitsa kwanu kuphunzira mapulinsipulo a Baibulo amene amagwira ntchito pa moyo wa banja. Anthu amene anawayesapo asonyeza kuti zinthu zinawayendera bwino kwambiri mwa kugwiritsira ntchito uphungu wothandiza wopezeka m’Baibulo. Nachi chitsanzo china chofotokoza chifukwa chake zilidi choncho.” Ŵerengani ndime yoyamba ya phunziro 1 m’brosha la Mulungu Amafunanji, kuphatikizapo kaya Salmo 1:1-3 kapena Yesaya 48:17, 18. Ngati mpata ulipo, malizani phunziro lonselo. Pemphani kuti mudzabwerereko kuti mukaphunzire limodzi phunziro lotsatira.
6 Tiyeni tiyesetse kuuza ena chinsinsi cha chimwemwe cha banja—potsatira malangizo ochokera m’Mawu a Mulungu.—Sal. 19:7-10.