Sungani
Maulaliki Amene Mungagwiritse Ntchito mu Utumiki wa Kumunda
Mmene Tingagwiritsire Ntchito Mphatikayi
Ochuluka a maulalikiŵa ali m’makope a m’mbuyomu a Utumiki Wathu wa Ufumu. Tayesani ochuluka amene mukufuna mu ulaliki wanu ndipo mudzaona mapindu ake. Sungani mphatika imeneyi ndipo muziigwiritsa ntchito mukamakonzekera utumiki.
Mungakope chidwi cha munthu pa Mawu a Mulungu ngati mutchula mfundo msanga. Perekani funso lachindunji, kenako ŵerengani yankho lachidule la m’Malemba. Tayesani mfundo izi:
“Mukamaganiza za kutsogolo, kodi mumalimba mtima kapena mumataya mtima? [M’yembekezeni ayankhe.] Baibulo linaneneratu za zinthu zosautsa zimene tikuona zikuchitika masiku ano komanso zotsatira zake.”—2 Tim. 3:1, 2, 5; Miy. 2:21, 22.
“Anthu ambiri masiku ano ali ndi nkhaŵa ya zaumoyo. Kodi mukudziŵa kuti Mulungu akulonjeza kuchotseratu matenda onse?”—Yes. 33:24; Chiv. 21:3, 4.
“Kodi mukudziŵa kuti Baibulo limaneneratu kuti padzakhala boma limodzi lokha lolamulira dziko lonse?”—Dan. 2:44; Mat. 6:9, 10.
“Kodi muganiza kuti zinthu zikanakhala bwanji ngati Yesu Kristu ndiye anali kulamulira dziko lapansi?”—Sal. 72:7, 8.
“Anthu ambiri amawasankha chifukwa chakuti ndi akazi kapena amuna, chifukwa cha chipembedzo chawo kapena fuko lawo. Kodi muganiza Mulungu amaliona bwanji tsankho ngati limeneli?”—Mac. 10:34, 35.
“Tikudziŵa kuti Yesu Kristu anachita zozizwitsa zambiri masiku ake. Ngati zikanakhala zotheka kumupempha kuti achitenso chozizwitsa china, mukanapempha kuti achite chotani?”—Sal. 72:12-14, 16.
“Anthu ambiri atopa kumva za mavuto. Akufuna kumva zimene zingawathandize pa mavuto awo. Nangano thandizo ngati limenelo tingalipeze kuti?”—2 Tim. 3:16, 17.
“Kodi mutha kuutchula Ufumu umene mumapempha m’Pemphero la Ambuye (kapena lakuti, Atate Wathu)?”—Chiv. 11:15.
Mawu Oyambitsa Kukambirana
Mpambo wa mafunso ali mmunsiŵa, wokonzedwa mogwiritsa ntchito mitu ya m’buku la Kukambitsirana, ukusonyeza tsamba la m’bukuli pamene yankho lililonse likupezeka:
N’chifukwa chiyani timakalamba ndi kufa? (151)
Kodi akufa ali mumkhalidwe wotani? (153)
Kodi pali zifukwa zomveka zokhulupirira Mulungu? (307)
Kodi Mulungu amasamaladi zimene zimachitika kwa anthufe? (308)
Kodi Mulungu ndi munthu weniweni? (309)
Kodi anthu onse abwino amapita kumwamba? (203)
Kodi munthu ayenera kupita kumwamba kuti akhaledi ndi m’tsogolo mwachimwemwe? (204)
Kodi n’chifukwa ninji kuli kofunika kudziŵa ndi kugwiritsa ntchito dzina lake la Mulungu? (420)
Kodi Yesu Kristu kwenikweni ali Mulungu? (426)
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachitanji? (376)
Kodi n’chiyani chimene chili chifuno cha moyo wa munthu? (290)
Kodi n’chiyani chimene chingathandize kuwongolera ukwati? (388)
Kodi zipembedzo zonse n’zovomerezeka kwa Mulungu? (83)
Kodi munthu angadziŵe motani chimene chili chipembedzo choona? (89)
Kodi Satana ali munthu wamphamvu motani m’dziko lamakono? (355)
Kodi n’chifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika? (222)
Kodi n’chifukwa ninji pali kuipa kochuluka? (183)
Kodi ndani amene amalamulira dzikoli—Mulungu kapena Satana? (128)
Mfundo Zimene Mungagwiritse Ntchito Pogaŵira Bulosha la Mulungu Amafunanji
“Ndiganiza mukuvomereza kuti ambiri amakhulupirira Mulungu. Onse om’khulupirira amavomereza kuti pali zimene iye amafuna kwa ife. Koma pamene sagwirizana ndi pa yankho la funso lakuti, Kodi Mulungu amafunanji kwa ife?” Kenako m’patseni bulosha la Mulungu Amafunanji, pitani pa phunziro 1 ndi kukambirana phunzirolo.
“Poganiza za mavuto ambiri amene mabanja ali nawo masiku ano, kodi munapezapo chinsinsi chake kuti banja lisangalale?” Akayankha, fotokozani kuti Mulungu m’Baibulo amasonyeza chinsinsi chenicheni kuti banja lisangalale. Ŵerengani Yesaya 48:17. Kenako pitani pa phunziro 8 m’bulosha la Mulungu Amafunanji, ndi kum’sonyeza mavesi ena a m’Baibulo amene akupereka malangizo odalirika kwa munthu aliyense m’banja. Ŵerengani mafunso omwe ali kuchiyambi kwa phunzirolo. M’funseni ngati akufuna kuŵerenga mayankho ake.
“M’bukuli muli maphunziro ozama a ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Patsamba lililonse, mudzapezapo mayankho a mafunso amene anthu avutika nawo zaka zambiri. Mwachitsanzo funso lakuti, Kodi chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi n’chiyani?” Pitani pa phunziro 5, ndi kuŵerenga mafunso omwe ali kuchiyambi kwa phunzirolo. M’pempheni mwininyumba anene funso limene wachita nalo chidwi ndipo ŵerengani ndime yake (zake) komanso malemba oyenerera. Muuzeni kuti angapeze mayankho okhutiritsa a mafunso enawo mosavuta ngati mmene mwachitiramo. M’pempheni kuti mudzabwerenso kudzakambirana funso lina.
“Muganiza n’chiyani chimachititsa chiwawa kusukulu? Kodi ndi kulephera kwa makolo kulangiza ana awo? Kapena pangakhale chifukwa china, ngati mphamvu ya Mdyerekezi?” M’yembekezeni ayankhe. Akanena kuti ndi chifukwa cha mphamvu ya Mdyerekezi, ŵerengani Chivumbulutso 12:9, 12. Tchulani zimene Mdyerekezi akuchita polimbikitsa chipwirikiti m’dziko. Ndiyeno tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji pa phunziro 4, ndipo m’funseni ngati anaganizapo za kumene Mdyerekezi anachokera. Ndiye ŵerengani ndi kukambirana ndime ziŵiri zoyamba. Ngati ayankha kuti chimene chimachititsa chiwawa kusukulu “ndi kulephera kwa makolo kulangiza ana awo,” ŵerengani 2 Timoteo 3:1-3 ndi kusonyeza makhalidwe amene mosakayika amawonjezera vutoli. Mutatero, tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji pa phunziro 8, ndi kuŵerenga ndime 5, ndipo pitirizani kukambirana.
“Kodi mukuona kuti ndi bwino kuganiza kuti Mlengi wathu ayenera kutiuza zimene tifunika kudziŵa kuti tikhale ndi banja labwino?” Akayankha, m’sonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji. Pitani pa phunziro 8 ndi kufotokoza kuti phunzirolo lili ndi mfundo za chikhalidwe zotengedwa m’Baibulo zopita kwa munthu aliyense m’banja. M’pempheni ngati angafune kuti mum’sonyeze mmene angagwiritsire ntchito bukulo ndi Baibulo kuti apindule kwambiri.
“Poona mavuto amene tikukumana nawo pa moyo masiku ano, kodi muganiza kuti pemphero lingathandize? [M’yembekezeni ayankhe.] Ambiri amati pemphero limawalimbitsa mtima. [Ŵerengani Afilipi 4:6, 7.] Komabe, munthu angaganize kuti mapemphero ake sayankhidwa. [Tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji pa phunziro 7.] Bukuli likufotokoza mmene pemphero lingatithandizire.”
“Tikukambirana ndi anansi athu chimene pakhalira zipembedzo zambiri m’dziko pamene Baibulo ndi limodzi. Mukaganiza, n’chifukwa chiyani pali zipembedzo zambiri chotere? [M’yembekezeni ayankhe. Tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji pa phunziro 13, ndi kuŵerenga mafunso otsegulira.] Mudzapeza mayankho okhutiritsa a mafunso ameneŵa mwa kuŵerenga phunziro limeneli.”
Mutagaŵira magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, tam’pemphani kuti mumuŵerengere ndime imodzi yachidule. Akalola, tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji pa phunziro 5. Muonetseni mafunso ali kuchiyambi kwa phunzirolo, ndipo muuzeni kuti amvetsere yankho la funso loyamba pamene mukuŵerenga ndime yoyamba. Mutaŵerenga ndimeyo, funsani funso ndipo iye ayankhe. Gaŵirani buloshalo ndipo ngati walandira, konzani zodzabweranso kuti mudzamuyankhe mafunso aŵiri otsatirawo.
Mfundo Zimene Mungagwiritse Ntchito Pogaŵira Buku la Chidziŵitso
Baibulo lanu lili kumanja, yambani mwa kunena kuti: “Pali lemba limene tikuŵerengera wina aliyense mu msewu wanuwu lero. Likuti . . .” Ŵerengani Yohane 17:3, kenako m’funseni kuti: “Kodi mwaona zimene akutilonjeza titadziŵa zolondola? [M’yembekezeni ayankhe.] Ngati munthu akufuna kudziŵa zolondola angazipeze kuti?” Atayankha, m’sonyezeni buku la Chidziŵitso, ndipo nenani kuti: “Buku ili likufotokoza chidziŵitso chotsogolera ku moyo wosatha. Likutero mwa kuyankha mafunso ofala kwambiri amene anthu ali nawo pa Baibulo.” M’sonyezeni zam’katimo, ndipo m’funseni ngati anaganizapo za nkhani iliyonse pa nkhanizo.
“Kodi munaganizapo zakuti kaya Mulungu amaonadi kupanda chilungamo ndi kuvutika zimene timaona ngakhale zimene zimatichitikira? [M’yembekezeni ayankhe.] Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu amatikonda ndi kuti adzatithandiza nthaŵi ya tsoka.” Ŵerengani zigawo za Salmo 72:12-17. Tsegulani buku la Chidziŵitso pamutu 8, ndi kufotokoza kuti mutuwu umapereka yankho pafunso limene ambiri afunsa lakuti, Kodi n’chifukwa ninji Mulungu amalola kuvutika? Ngati kutheka, kambiranani mfundo zina za m’Malemba zofotokozedwa m’ndime 3 mpaka 5, kapena mudzatero paulendo wobwereza.
“Ambiri tinafedwa anthu amene tinkawakonda. Kodi munaganizapo ngati tidzawaonanso? [M’yembekezeni ayankhe.] Yesu anapereka umboni wakuti okondedwa athu atha kuuka kwa akufa. [Ŵerengani Yohane 11:11, 25, 44.] Ngakhale kuti zimenezi zinachitika zaka mazana ambiri kalelo, zimasonyeza zimene Mulungu walonjeza kutichitira.” Tsegulani buku la Chidziŵitso pachithunzi chili patsamba 85 ndi kuŵerenga mawu a chithunzicho. Ndiyeno sonyezani chithunzi chili patsamba 86 ndipo kambanipo pachithunzicho. Yalani maziko a ulendo wotsatira mwa kufunsa kuti: “Kodi mukufuna kudziŵa chifukwa chake anthu amakalamba ndi kufa?” Mudzabwerenso kudzakambirana mutu 6.
“Kodi munaganizapo za chimene anthu amafunira moyo wautali?” Atayankha, tsegulani buku la Chidziŵitso pamutu 6, ndi kuŵerenga ndime 3. Kambiranani malemba osonyezedwawo. Potchula mafunso aŵiri ali kumapeto kwa ndimeyo, m’funseni ngati akufuna kupeza yekha mayankho ake. Ngati akufuna zimenezo, kambiranani ndime zoŵerengeka zotsatira.
“Tikufunsa anthu ngati amakhulupirira izi . . .” Ŵerengani Genesis 1:1, ndiyeno funsani kuti: “Kodi mukuvomerezana nawo mawu ameneŵa?” Akavomera, nenani kuti: “Inenso ndikuvomerezana nawo. Komabe, kodi mukuganiza kuti popeza Mulungu analenga zinthu zonse, ndiye kuti ndi amenenso anayambitsa kuipa?” Mutayamikira yankho lake, ŵerengani Mlaliki 7:29. Tsegulani buku la Chidziŵitso pamutu 8, ndipo ŵerengani ndime 2. Ngati sakugwirizana ndi Genesis 1:1, m’limbikitseni kupenda umboni wakuti Mlengi alikodi.—Onani buku la Kukambitsirana, masamba 74-6.
“Kodi mukuvomereza kuti popeza makhalidwe a anthu akusintha mofulumira masiku ano, tikufunika malangizo odalirika pa moyo? [M’yembekezeni ayankhe.] Ngakhale kuti Baibulo ndi buku lakalekale, limapereka uphungu wothandiza pa moyo wamakono komanso wothandiza mabanja kukhala achimwemwe.” Ndiyeno tsegulani pa mutu 2 m’buku la Chidziŵitso, ndi kuŵerenga ndime 10 komanso chiganizo choyamba m’ndime 11, kuphatikizapo 2 Timoteo 3:16, 17.
“Kodi mukufuna kudziŵa zimene anthufe ndi dziko lapansili tikuyembekeza m’tsogolo muno? [M’yembekezeni ayankhe.] Baibulo limafotokoza za m’tsogolo ndi liwu limodzi—Paradaiso! Ndi mmene Mulungu anaika anthu aŵiri oyamba atawalenga. Tamvani mmene mawu aŵa akuyesa kufotokozera mmene paradaisoyo analili.” Tsegulani buku la Chidziŵitso patsamba 8, ndiye ŵerengani ndime 9, pakamutu kakuti “Moyo M’Paradaiso.” Kenaka kambiranani mfundo zili m’ndime 10, ndiyeno muŵerenge lemba lili pamenepolo la Yesaya 55:10, 11. M’pempheni kuti mukambirane za mmene moyo udzakhalira m’Paradaiso wobwezeretsedwa pa ndime 11-16.
Paulendo Wobwereza kwa Aja Amene Munagaŵira Magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Munganene Izi:
“Ulendo watha uja, ndinasangalala n’takusiyirani magazini ya Nsanja ya Olonda. Mwina munaona kuti magazini imeneyi dzina lake lonse ndi Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Lero ndati ndifotokoze Ufumu umenewu ndi mmene ukukukhudzirani inuyo ndi banja lanu.” Kenako tsegulani bulosha la Mulungu Amafunanji paphunziro 6, ndipo ŵerengani ndi kukambirana ndime zochuluka malinga ndi nthaŵi imene munthuyo ali nayo.
“Nditabwera kudzakuchezerani posachedwa pomwepa, ndinakusiyirani magazini ya Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Magazini ameneŵa amalimbikitsa anthu kulemekeza Baibulo ndi malangizo ake a makhalidwe abwino. Popeza ndikuona kuti munthu aliyense afunika kuwamvetsa Mawu a Mulungu, ndabweranso kuti ndikusonyezeni zimene zingakuthandizeni kuwamvetsa.” M’sonyezeni bulosha la Mulungu Amafunanji kapena buku la Chidziŵitso, ndipo m’pempheni kuphunzira naye Baibulo.
Pogaŵira mabuku a masamba 192 alionse akale, mungayese ulaliki uwu:
“Ambiri amalimbikitsa maphunziro abwino. Inuyo mukaganiza, kodi ndi maphunziro a mtundu wanji amene munthu akufunikira kuti azisangalala kwambiri pa moyo ndi kuti zinthu zizimuyendera bwino? [M’yembekezeni ayankhe. Kenako ŵerengani Miyambo 9:10, 11.] Buku ili [tchulani mutu wa buku limene mukugaŵira] lazikidwa pa Baibulo. Likutchula gwero lokha la nzeru yopatsa moyo wosatha.” M’sonyezeni mfundo ina m’bukulo, ndi kum’limbikitsa kuliŵerenga.
Zofalitsa Zina
Aja amene amamva Chingelezi atha kupeza maulaliki amene angagwiritse ntchito pogaŵira mabuku ena ndi mabulosha mu Watch Tower Publications Index pamutu wakuti:
Presentations
List by Publication
Njira Yolunjika
Ngati mukufuna kuyambitsa phunziro la Baibulo, yesani imodzi mwa njira zolunjika izi:
“Kodi mukudziŵa kuti pamphindi zochepa chabe mutha kupeza yankho la funso lofunika kwambiri la m’Baibulo? Mwachitsanzo, . . .” Mukatero, perekani funso limene lili kuchiyambi kwa limodzi la maphunziro a m’bulosha la Mulungu Amafunanji, limene mukuganiza kuti lidzam’kopa chidwi munthuyo.
“Ndafika kuti ndikuonetseni mmene timachitira phunziro lathu la Baibulo kwaulere. Zimatenga mphindi ngati faifi zokha kukuonetsani. Kodi muli ndi nthaŵi?” Akavomera, gwiritsani ntchito phunziro 1 m’bulosha la Mulungu Amafunanji pomuonetsa mmene timachitira phunziro, ndipo ŵerengani lemba limodzi kapena aŵiri amene mwasankha basi. Mukamaliza, m’funseni kuti: “Ndi liti pamene mudzakhala ndi mphindi 15 kuti tikakambirane phunziro lotsatira?”
“Anthu ambiri Baibulo ali nalo koma sadziŵa kuti lili ndi mayankho a mafunso ofunika kwambiri okhudza za m’tsogolo omwe tonsefe timakhala nawo. Mwa kugwiritsa ntchito buku ili [la Mulungu Amafunanji kapena la Chidziŵitso] kuphunzira pafupifupi ola limodzi pamlungu, mungayambe kulidziŵa Baibulo pamiyezi yochepa chabe. Ndakonzeka kukuonetsani mmene timachitira.”
“Ndabwera kuti ndikupempheni kuti tiziphunzira nanu Baibulo kwaulere. Kwa mphindi zingapo chabe, ndati ndikuonetseni mmene anthu m’mayiko pafupifupi 200 amachitira pokambirana za Baibulo panyumba monga mabanja. Pokambirana, titha kugwiritsa ntchito mutu umodzi mwa mitu iyi. [M’sonyezeni zam’kati mwa buku la Chidziŵitso.] Kodi ndi mutu uti umene wakusangalatsani?” M’yembekezeni asankhe. Pitani pa mutu umene wasankha ndipo yambani phunziro m’ndime yoyamba.
“Ndimaphunzitsa Baibulo kwaulere ndipo ndili ndi mpata woti ndiwonjezere ophunzira ena. Timagwiritsa ntchito buku ili kuphunzirira Baibulo. [M’sonyezeni buku la Chidziŵitso.] Kosi imeneyi imangotenga miyezi yochepa chabe ndipo imapereka mayankho pa mafunso onga akuti: N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuvutika? N’chifukwa chiyani timakalamba ndi kufa? Chimachitika n’chiyani kwa anthu amene timawakonda akamwalira? Ndipo ngati tikufuna kuyandikira kwa Mulungu tingachite chiyani? Kodi ndikuonetseni mmene timaphunzirira?”
Ngati mwapeza ulaliki wogwira mtima, pitirizani kuugwiritsa ntchito! Muzingousintha pang’ono kuti uzigwirizana ndi buku logaŵira mweziwo.