Gwiritsani Ntchito Kabuku Kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu
Kabuku Katsopano Kothandiza Pochita Maulendo Obwereza ndi Poyambitsa Maphunziro
1. Kodi tinalandira kabuku kati pa msonkhano wakuti ‘Tetezani Mtima Wanu!’?
1 Pa msonkhano wachigawo wakuti, ‘Tetezani Mtima Wanu!,’ tinasangalala kulandira kabuku katsopano kotithandiza kupanga maulendo obwereza ndi kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Kabuku ka Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu kakulowa m’malo mwa kabuku ka Mulungu Amafunanji ndipo ndi kofananako. Kabuku katsopanoka kalinso ndi mitu ifupiifupi. Choncho munthu angakagwiritse ntchito kuti achititse maphunziro a Baibulo achidule kwambiri. Kabuku ka Mulungu Amafunanji kanali ndi mfundo zimene Mkhristu anayenera kutsatira zomwe zingakhale zovuta kwa anthu amene angoyamba kumene kuphunzira Baibulo. Koma kabuku katsopanoka kamangofotokoza uthenga wabwino wa m’Baibulo.—Mac. 15:35.
2. Kodi cholinga cha kabuku ka Uthenga Wabwino n’chiyani?
2 Kodi cholinga cha kabukuka n’chotani? Abale padziko lonse akhala akupempha kabuku kosavuta kothandiza anthu kuyamba kuphunzira choonadi asanayambe buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, lomwe timagwiritsa ntchito pa maphunziro a Baibulo. Anthu amene amaona kuti sangakwanitse kuphunzira buku lalikulu, nthawi zambiri amavomera kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakang’ono. Komanso mosiyana ndi mabuku akuluakulu, kabuku kamakhala kosavuta kumasulira m’zilankhulo zambiri.
3. Kodi kabukuka kakusiyana bwanji ndi mabuku ena?
3 Kodi Kalembedwa Bwanji? Mabuku athu ambiri alembedwa m’njira yoti munthu angawawerenge n’kumvetsa choonadi popanda kuthandizidwa ndi munthu wina. Koma si mmene kalili kabukuka. Kalembedwa kuti munthu aziphunzira mothandizidwa ndi munthu wina. Choncho mukamapereka kabukuka ndi bwino kukambirana ndi munthuyo ndime imodzi kapena ziwiri. Ndime zake ndi zifupizifupi moti mukhoza kukambirana ndi munthu mutangoimirira kapena ali kuntchito. Ngakhale kuti ndi bwino nthawi zambiri kuyamba kuphunzira ndi munthu pa phunziro 1, mutha kuyamba ndi phunziro lililonse.
4. Kodi kabukuka kadzatithandiza bwanji kuphunzitsa kuchokera m’Baibulo?
4 M’mabuku athu ambiri, mayankho a mafunso amakhala m’ndime. Koma m’kabukuka, mayankho amapezeka nthawi zambiri m’Baibulo. Anthu ambiri amafuna kumva zinthu kuchokera m’Baibulo osati m’mabuku athu. Choncho, ndi malemba ochepa kwambiri amene awagwira mawu. Cholinga n’choti tiziwerenga m’Baibulo lenilenilo. Izi zidzathandiza anthu kudziwa kuti akuphunzitsidwa ndi Mulungu.—Yes. 54:13.
5. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonzekera bwino phunziro lililonse?
5 Kabukuka sikafotokoza malemba onse. Achita dala zimenezi pofuna kuti wophunzira azifunsa mafunso ndipo wophunzitsayo aziyankha mwaluso. Choncho kukonzekera bwino phunziro lililonse n’kofunika. Koma tiyenera kusamala kuti tisamachulukitse gaga m’diwa pofotokoza zinthu. Pajatu ife timakonda kwambiri kufotokoza Malemba. Koma zingakhale zothandiza kwambiri ngati titapempha wophunzirayo kuti afotokoze maganizo ake pa lembalo. Tizigwiritsa ntchito mafunso mwaluso kuti timuthandize kumvetsa malemba.—Mac. 17:2.
6. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji kabukuka: (a) tikapeza anthu amene sakhulupirira kwenikweni Mulungu kapena Baibulo? (b) polalikira kunyumba ndi nyumba? (c) popempha munthu kuti tiziphunzira naye? (d) popanga maulendo obwereza?
6 Mofanana ndi mabuku ena amene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu, tikhoza kugawira kabukuka nthawi iliyonse. Tingachite zimenezi ngakhale kuti pa mweziwo, tikugawira mabuku ena. Ambirife tingakonde kungofunsa anthu pa ulendo woyamba ngati angakonde kuphunzira Baibulo pogwiritsa ntchito kabukuka. Monga tinaphunzirira pa msonkhano wachigawo, kabukuka katithandiza kwambiri kuti tisamavutike kupanga maulendo obwereza.—Onani mabokosi a patsamba 5 mpaka 7.
7. Kodi mungachititse bwanji phunziro pogwiritsa ntchito kabukuka?
7 Mmene Mungachititsire Phunziro: Mukhoza kuyamba ndi kuwerenga funso lolembedwa m’mawu akuda. Kenako mungawerenge ndime ndiponso malemba amene alembedwa ndi mawu akuda. Mukatero, funsani mafunso mwaluso kuti muthandize munthuyo kumvetsa malembawo. Musanapite pachigawo china, funsaninso funso lija kuti mutsimikizire ngati wamvetsadi. Pa masiku oyambirira, mungachite bwino kumangokambirana funso limodzi lokha. Kenako tikhoza kumawonjezera nthawi pang’onopang’ono mpaka kufika pokambirana phunziro lathunthu.
8. Potchula malemba, kodi tizigwiritsa ntchito mawu monga ati? Perekani chifukwa.
8 Malemba amene alembedwa kuti “werengani” ndi amene amayankha mwachindunji funso la mawu akuda. Tikamatchula malemba, ndi bwino kupewa mawu monga, “Mtumwi Paulo analemba kuti” kapena, “Taonani zimene Yeremiya analosera.” Munthuyo angaganize kuti tikungowerenga mawu a anthu basi. Mungachite bwino kunena kuti, “Mawu a Mulungu akuti” kapena, “Taonani zimene Baibulo linaneneratu.”
9. Kodi tiyenera kuwerenga malemba onse pophunzira ndi munthu?
9 Kodi tiyenera kuwerenga malemba onse kapena okhawo amene alembedwa kuti “werengani”? Mungasankhe nokha malinga ndi mmene zinthu zilili. Palibe lemba limene langoikidwa kuti lisonyeze kumene mungapeze mfundo imene mukukambirana. Lemba lililonse lili ndi mfundo zothandiza zimene mungakambirane. Koma nthawi zina anthu amene timaphunzira nawo sakhala ndi nthawi kapena chidwi chokwanira. Enanso amavutika kuwerenga. Choncho mwina mungafunike kungowerenga nawo malemba olembedwa kuti “werengani.”
10. Kodi tingayambe liti kuphunzira buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani?
10 Kodi Tingayambe Liti Kuphunzira Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani? Titaphunzira ndi munthu kangapo ndipo phunzirolo likuyenda bwinobwino, tingasankhe kuyamba buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena tingapitirize m’kabuku ka Uthenga Wabwino mpaka titamaliza kuphunzira naye kabukuka. Ofalitsa angasankhe okha zoyenera kuchita. Kodi tikamayamba buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, tiyenera kuyamba kumayambiriro? Palibe lamulo pamenepa chifukwa ophunzira amasiyana. Koma buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani limafotokoza nkhani za m’kabukuka mwatsatanetsatane. Choncho ophunzira ambiri angapindule ngati ataphunziranso nkhanizi m’buku limeneli.
11. N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito kabuku katsopanoka?
11 M’dzikoli uthenga wabwino umasowa. Koma ife tili ndi mwayi wolengeza uthenga wabwino kwambiri wakuti, Ufumu wa Mulungu ukulamulira ndipo posachedwapa ubweretsa dziko latsopano lachilungamo. (Mat. 24:14; 2 Pet. 3:13) Sitikukayikira kuti anthu ambiri amene adzamve uthengawu adzagwirizana ndi mawu akuti: “Mapazi a munthu yemwe akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino, ndi okongola kwabasi! Munthu yemwe akulengeza za mtendere, yemwe akubweretsa uthenga wabwino wa zinthu zabwino kuposa kale, yemwe akulengeza za chipulumutso, yemwe akuuza Ziyoni kuti: ‘Mulungu wako wakhala mfumu.’” (Yes. 52:7) Tiyeni tizigwiritsa ntchito kabukuka pouza anthu aludzu m’dera lathu uthenga wabwino wochokera kwa Mulungu.
[Bokosi patsamba 5]
Tikapeza Anthu Amene Sakhulupirira Kwenikweni Mulungu Kapena Baibulo:
● Kumadera ena, anthu ambiri sakonda kukambirana za Mulungu kapena Baibulo. Kumadera otere, mungachite bwino pa ulendo woyamba kulankhula ndi anthu nkhani zimene iwo angachite nazo chidwi. Mwachitsanzo, mungakambirane za kufunika kwa boma labwino, zimene zingathandize mabanja kapena zimene zidzachitike m’tsogolo. Mwina mutalankhula nawo kangapo pa nkhani yakuti Mulungu alipo ndiponso kuti Baibulo n’lodalirika, mutha kuyamba nawo kabuku ka Uthenga Wabwino.
[Bokosi patsamba 6]
Tikamalalikira Kunyumba ndi Nyumba:
● “Ndabwera kudzakusonyezani kuti mutha kudziwa mosavuta zimene Mulungu watikonzera m’tsogolo. Kodi mukuganiza kuti Mulungu adzathetsa mavuto athu? [Yembekezani ayankhe.] Kabuku aka kakusonyeza malemba amene amayankha funsoli. [M’patseni kabukuko ndipo werengani ndime yoyamba m’phunziro 1 komanso lemba la Yeremiya 29:11.] Kodi mukuona kuti zimene tawerengazi zikusonyeza kuti Mulungu watikonzera zabwino m’tsogolo? [Yembekezani ayankhe.] Ngati mungakonde, mukhoza kutenga kabukuka. Ndidzabweranso kuti tidzakambirane ndime yachiwiriyi. Tidzapeza yankho m’Baibulo la funso lakuti, ‘Kodi Mulungu adzathetsa bwanji mavuto athu?’” Ngati munthuyo ali ndi mpata mungakambirane naye ndime yachiwiri komanso malemba ake atatu. Ndiyeno mugwirizane kuti mudzakambirane funso lachiwiri la phunzirolo.
● “Anthu ambiri amakonda kupemphera makamaka akakhala pa mavuto. Kodi inunso mumapemphera nthawi zina? [Yembekezani ayankhe.] Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamvetsera mapemphero onse kapena pali mapemphero ena amene samusangalatsa? [Yembekezani ayankhe.] Kabuku aka kakuthandizani kupeza mayankho a mafunsowa m’Baibulo. [M’patseni kabukuka ndipo muwerenge ndime yoyamba ya phunziro 12 komanso malemba amene alembedwa kuti “werengani.”] Kodi si zosangalatsa kuti Mulungu amafunitsitsa kumva mapemphero athu? Koma kuti mapemphero athu azitithandiza, tiyenera kudziwa bwino Mulungu. [Tsegulani pa phunziro 2 n’kumusonyeza timitu take.] Ngati mungakonde, ndikhoza kukupatsani kabukuka. Ndiye ndidzabweranso kuti tidzakambirane mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso ochititsa chidwiwa.”
● “Ndikuona kuti anthu ambiri akuda nkhawa akaganizira kumene dzikoli likulowera? Kodi mukuganiza kuti mavuto a m’dzikoli adzatha? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri sadziwa kuti Baibulo lili ndi uthenga wabwino umene ungatipatse chiyembekezo. Baibulo limayankha mafunso ngati awa.” M’patseni kabukuka n’kumusonyeza kuseri kwake. Muuzeni kuti asankhe funso limene lamusangalatsa. Ndiyeno pitani pa phunziro lake n’kuyamba kuphunzira naye. Kambiranani zoti mudzabwerenso kudzapitiriza phunzirolo.
[Bokosi patsamba 7]
Yesani Kungofunsa Ngati Akufuna Kuphunzira:
● “Kodi mungakonde kudziwa njira yatsopano yophunzirira Baibulo? Kabuku aka kali ndi maphunziro 15 okuthandizani kupeza mayankho m’Baibulo a mafunso ofunika kwambiri. [M’sonyezeni zimene zili pachikuto choyamba ndi chomaliza.] Kodi mumaona kuti kuphunzira Baibulo n’kovuta? [Yembekezani ayankhe.] Maphunziro a m’kabukuka ndi osavuta. Tadikirani ndikusonyezeni. [Kambiranani ndime yoyamba ya funso lachitatu m’phunziro 3 ndipo muwerenge Chivumbulutso 21:4, 5. Ngati n’zotheka, kambirananinso ndime yotsatira ndiponso malemba amene alembedwa kuti “werengani”.] Ngati mungakonde, ndikhoza kukupatsani kabukuka. Bwanji tiyese kuphunzira Baibulo limodzi? Ngati zingakusangalatseni tidzapitiriza. Ulendo wotsatira tingadzakambirane phunziro loyamba, lomwe ndi la tsamba limodzi lokha basi.”
[Bokosi patsamba 7]
Pa Ulendo Wobwereza:
● Tikakumananso ndi munthu amene anasonyeza chidwi tinganene kuti: “Ndasangalala kuti takumananso. Lero ndakubweretserani kabuku aka. Kali ndi mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso ambiri ochititsa chidwi. [M’patseni kabukuko n’kumuuza kuti aone pachikuto chomaliza.] Kodi ndi funso liti limene lakusangalatsani? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno pitani pa phunziro limene wasankha.] Dikirani ndikusonyezeni mmene bukuli lingatithandizire kupeza mayankho m’Baibulo.” Ndiyeno phunzirani ndime imodzi kapena ziwiri ndiponso muwerenge malemba amene ali alembedwa kuti “werengani”. Mukatero ndiye kuti phunziro layambika. M’patseni kabukuko n’kupangana naye kuti mudzabwerenso. Mukamaliza phunzirolo, mukhoza kukambirana naye phunziro lina limene angasankhe kapena kungoyamba pa phunziro loyamba.