Tsanzirani Yehova mwa Kusamalira Ena Moona Mtima
1 Yehova ndiye chitsanzo chachikulu koposa cha munthu amene amasamalira ena moona mtima. Monga Mfumu Yachilengedwe Chonse, amadziŵa bwino zosoŵa za zolengedwa zake zaumunthu. (1 Pet. 5:7) Yesu analimbikitsa otsatira ake kusonyeza mikhalidwe ya Atate wake, amene amakwezera dzuŵa ndi kuvumbitsa mvula pa olungama ndi osalungama. (Mat. 5:45) Mungathe kutsanzira Yehova mwa kusonyeza nkhaŵa yeniyeni kwa ena—kukhala okonzekera kuuza aliyense amene mungakumane naye za uthenga wa Ufumu. Mwa kukhala odziŵa bwino kwambiri za m’mabrosha amene adzagwiritsiridwa ntchito muutumiki m’July, mudzakhala okhoza kupereka thandizo lauzimu kwa ena. Njira zotsatirazi zikupereka malingaliro onena za mmene mungakonzekerere ulendo woyamba ndiyeno kubwerera kwa okondwerera panthaŵi yake.
2 Pogaŵira brosha lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?” munganene kuti:
◼ “Kodi munayamba mwadabwapo chifukwa chake Mulungu akulolera anthu kuvutika ngati iyeyo amasamaladi za iwo? [Yembekezerani yankho.] Brosha lino silimangopereka mayankho okhutiritsa chabe pa funso limeneli komanso limasonyeza kuti Mulungu walonjeza kuthetsa kuwononga konse kumene anthu abweretsa pa iwo eni ndi mudzi wawo wonse wa padziko lapansi.” Ŵerengani ndime 23 patsamba 27. Sonyezani chithunzithunzi chimene chili pansi pake, ndipo ŵerengani Salmo 145:16 m’ndime 22. Gaŵirani broshalo. Ngati lilandiridwa, funsani funso limene lingayankhidwe paulendo wotsatira, monga lakuti: “Kodi mungakonde kudziŵa mmene Mulungu adzakwaniritsira chifuno chake cha kubweretsa madalitso kwa anthu ndi kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso?”
3 Pamene mubwerera kwa aja amene munawagaŵira brosha lakuti “Kodi Mulungu Amatisamaliradi?” mungayambitse kukambitsirana kwinanso motere:
◼ “Pamene ndinafika tsiku lija, tinakambitsirana kuti Mulungu amasamaladi za ife ndi kuti akufuna kuthetsa kuwononga konse kumene anthu abweretsa pa iwo eni ndi mudzi wawo wa padziko lapansi.” Tsegulani brosha pa chithunzithunzi cha pamasamba 2-3 ndi kunena kuti: “Tinamaliza kukambitsirana kwathu ndi funso lakuti, Kodi Mulungu adzakwaniritsa motani chifuno chake cha kubweretsa madalitso kwa anthu ndi kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso? Kodi mukuganiza motani?” Yembekezerani yankho. Tsegulani patsamba 17, ndipo ŵerengani ndime 2 ndi Danieli 2:44. Pambuyo pake, ŵerengani ndime 12 patsamba 18. Pemphani mwini nyumbayo ngati angakonde kukambitsirana nanu chigawo 9 cha broshalo. Ngati angakonde kutero, phunzirani naye chigawocho.
4 Nawa mafikidwe amene angagwiritsiridwe ntchito pogaŵira brosha lakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.” Sonyezani chikuto chake ndi kunena kuti:
◼ “Lero tikugaŵira brosha ili limene lapereka chitonthozo ndi ndi chiyembekezo kwa mamiliyoni ambiri a anthu amene atayikiridwa okondedwa awo mu imfa. Kodi munayamba mwadabwapo ngati pali chiyembekezo kaamba ka akufa? [Yembekezerani yankho.] Baibulo limafotokoza momveka lonjezo la Mulungu la chiukiriro.” Ŵerengani Yohane 5:28, 29. Tsegulani broshalo ndi kufotokoza mfundo zimene zanenedwa m’ndime yomaliza patsamba 28 ndi ndime yoyamba patsamba 31. Sonyezani zithunzithunzi zimene zilipozo. Gaŵirani broshalo. Mungalinganize ulendo wobwereza mwa kufunsa kuti, “Kodi tingakhale otsimikiza motani kuti imfa idzachotsedweratu potsirizira pake?”
5 Kumene munagaŵira brosha lakuti “Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira,” mungafune kugwiritsira ntchito ulaliki uwu paulendo wanu wobwereza:
◼ “Pa kukambitsirana kwathu koyamba, tinalankhula za chiyembekezo chabwino kwambiri kaamba ka akufa. Brosha limene ndinakusiyirani likulongosola chifukwa chake tingakhalire otsimikizira kuti imfa idzachotsedweratu potsirizira pake. Kodi simunapeze malonjezo a Mulungu kukhala otonthoza ndi opereka chitsimikiziro?” Yembekezerani yankho. Ndiyeno tsegulani patsamba 31 m’broshalo, ndi kuŵerenga ndime yachiŵiri ndi yachitatu, pamodzi ndi Chivumbulutso 21:1-4. Sonyezani chiyembekezo chimene tili nacho cha kudzasangalala ndi moyo wopanda imfa. Mungapemphe kuchita naye phunziro la Baibulo m’buku la Chidziŵitso kapena kufunsa funso lina kuti mutsegule njira ya ulendo wina wobwereza, zikumadalira pa chidwi cha munthu ndi mikhalidwe ya panthaŵiyo.
6 Munganene zotsatirazi pogaŵira brosha lakuti “Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?”:
◼ “Anthu ambiri adabwa za chimene chili chifuno cha moyo. Adzifunsa kuti: ‘Kodi nchifukwa ninji ndili pano? Kodi ndikumka kuti? Kodi mtsogolomu mulinji kwa ine?’ Kodi mukuganiza kuti nkuti kumene tingapeze mayankho ake? [Yembekezerani yankho.] Taonani zimene Baibulo limanena. [Ŵerengani Salmo 36:9.] Kodi sikwanzeru kunena kuti Mlengi wa munthu ndiye amene angathe kufotokoza bwino koposa chifukwa chake tili pano? [Yembekezerani yankho.] Brosha ili likusonyeza za chifuno chachikulu chimene Mulungu watisungira.” Tsegulani pamasamba 20-1, ŵerengani mawu ofotokoza chithunzithunzi, ndipo fotokozani za chithunzithunzicho; ndiyeno gaŵirani broshalo. Ngati alilandira, funsani kuti: “Kodi tingatsimikizire motani kuti kukhala ndi moyo kosatha kwa anthu m’Paradaiso pa dziko kukali chifuno cha Mulungu?” Konzani nthaŵi ya kudzabweranso.
7 Ngati brosha lakuti “Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani—Kodi Mungachipeze Motani?” linagaŵiridwa, munganene zonga izi pamene mubwererako:
◼ “Paulendo wanga wathawo, ndinasangalaladi kukambitsirana nanu kuti lingaliro la Baibulo lakuti, moyo wa munthu ulidi ndi chifuno.” Sonyezani chithunzithunzi patsamba 31 ndi kufunsa kuti: “Kodi tingatsimikizire motani kuti kukhala ndi moyo kosatha kwa anthu m’Paradaiso padziko lapansi kukali chifuniro cha Mulungu?” Ŵerengani ndime 3 patsamba 20. Kambitsiranani mfundo za m’mutu waung’ono wakuti, “Chidakali Chifuno cha Mulungu,” patsamba 21. Tembenukirani pa chikuto cha kumbuyo cha broshalo, ndi kuŵerenga za phunziro la Baibulo lapanyumba laulere. Sonyezani buku la Chidziŵitso, ndipo pemphani kusonyeza mmene timaligwiritsirira ntchito monga lothandizira kuphunzira Baibulo.
8 Utumiki wathu uyenera kusonyeza chidwi chenicheni chimene tili nacho pofuna kuthandiza anthu oona mtima ‘kufika pa chidziŵitso cholongosoka cha choonadi.’ (1 Tim. 2:4, NW) Motero, patulani nthaŵi mu mndandanda wanu wa utumiki ya kupitanso kwa munthu aliyense amene munamgaŵira brosha. Kusonyeza kwanu nkhaŵa yeniyeni kwa iwo kungathandize awo amene akuusa moyo ndi kulira ndi zinthu zonyansa zochitidwa m’chipembedzo chonyenga kukhala oikidwa chizindikiro cha kupulumuka. (Ezek. 9:4, 6) Mudzakhalanso ndi chimwemwe ndi chikhutiro chimene chimadza chifukwa cha kudziŵa kuti mukutsanzira Yehova mwa kusamalira ena moona mtima.—Yerekezerani ndi Afilipi 2:20.