Lengezani Uthenga Wabwino wa Ufumu ndi Mabrosha
1 Nkosangalatsa chotani nanga kudziŵa choonadi ndi kukhala pakati pa awo amene akulengeza uthenga wabwino mwachangu! Anthu amene ali kunja kwa gulu la Mulungu akufunikiradi kumva uthenga wabwino wa Ufumu. Choonadi chonena za Ufumu chimafotokozedwa mosavuta m’mabrosha akuti Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndi “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”. Amasonyeza bwino lomwe moyo padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu, ndipo amasonyeza woŵerenga zinthu zenizeni za Ufumu zimene zafotokozedwa m’Mawu a Mulungu. Komabe, kugaŵira brosha kwa munthu wofuna kuli chiyambi chabe cha ntchito yathu. (1 Akor. 9:23) Tiyeni tibwerere mwamsanga kumene tinagaŵira zilizonse, ndi chifuno cha kuyambitsa phunziro m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Kodi tingachite motani zimenezi mu August?
2 Mungagaŵire brosha la “Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!” ndi ulaliki wachidule kwambiri. Pamene musonyeza chikuto chake, munganene kuti:
◼ “Ndikufuna kukusonyezani kanthu kena kamene kali ndi uthenga wabwino kwambiri.” Tsegulani brosha la Moyo pa Dziko Lapansi, ndipo ŵerengani ndime yoyamba ya mawu oyamba. Ndiyeno pitirizani kuti: “Limayankhanso funsoli [pitani pa mutu umene uli pamwamba pa chithunzi cha nambala 8]: ‘Kodi nchifukwa ninji munthu amafa?’ Mudzasangalala kuphunzira zithunzi zimenezi ndi kuŵerenga malemba amene ali m’brosha limeneli. Ngati mukufuna kuchita zimenezo, mungatenge kopeli.”
3 Kodi mudzanenanji pamene mupanga ulendo wobwereza kumene munagaŵira brosha la “Moyo pa Dziko Lapansi”? Mungayese mafikidwe awa:
◼ Sonyezani chithunzi cha nambala 49 m’brosha la Moyo pa Dziko Lapansi ndi kufunsa kuti, “Kodi chimenechi si chithunzi chokongola? [Yembekezerani yankho.] Chili m’brosha limene ndinakusiyirani ulendo watha. Ndikufuna kukufunsani funso limene lili patsamba lotsatira.” Pitani pa chithunzi cha nambala 50 ndi kuŵerenga funsolo: “‘Kodi inu mukufuna kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wokongola?’ [Yembekezerani yankho.] Ngati zimenezo nzimene mukufuna, taonani zimene likunena kuti muyenera kuchita: ‘Pamenepotu phunzirani zochuluka ponena za zimene Mulungu amanena.’ [Ŵerengani Yohane 17:3.] Ndingakondwe kuphunzira nanu Baibulo kwaulere. Kodi mungakonde kuchita zimenezo?” Pangani makonzedwe otsimikizirika a kubwererako.
4 Pamene mukugaŵira brosha la “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano,” mungayambe mwa kusonyeza chithunzi chonse chapachikuto ndi kufunsa kuti:
◼ “Kodi muganiza nchiyani chiyenera kuchitika kuti dziko lonse lapansi lioneke chonchi?” Yembekezerani yankho. Fotokozani zina za zimene zili pachithunzicho, zimene zafotokozedwa patsamba 3. Ndiyeno nenani kuti: “Anthu ambiri amaganiza kuti nkosatheka kupanga dziko kukhala chonchi. Koma nzotheka kwa Mulungu. [Tchulani mfundo za m’ndime 43; ndiyeno ŵerengani Yesaya 9:6, 7.] Mulungu walonjeza kubweretsa dziko latsopano mmene anthu ochokera m’mitundu yonse adzakhala m’paradaiso wokongola kwambiri. Ndikufuna kuti broshali muliŵerenge. Lidzasonyeza mmene inuyo ndi banja lanu mungakhalire ndi mtsogolo mwabwino kwambiri mokonzedwa ndi Mulungu.”
5 Paulendo wobwereza, mungagwiritsire ntchito brosha la “Tawonani!” kufotokoza chifukwa chake kuphunzira zambiri ponena za Baibulo kuli kofunika. Mwinamwake mungasonyezenso chikuto chake ndi kunena kuti:
◼ “Pamene ndinakusonyezani chithunzichi poyamba, tinavomerezana kuti tingakondwere kukhala m’dziko labwino koposa limeneli. Kuti zimenezi zitheke, pali china chake chimene aliyense wa ife afunikira kuchita.” Tsegulani brosha la “Tawonani!” pa ndime 52; ŵerengani ndimeyo ndi lembalo la Yohane 17:3. Gwirizanitsani mawu ake ndi fanizo la m’ndime 53 lonena za maphunziro enieni a Baibulo, ndiyeno fotokozani kuti Mboni za Yehova zimapereka maphunziro otero kwaulere panyumba. Pemphani kusonyeza mmene timachitira phunziro, mukumagwiritsira ntchito buku la Chidziŵitso.
6 Pamene mukugaŵira brosha la “Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso,” mungayese kunena izi:
◼ “Ndamva anthu ambiri akunena kuti akufuna kukhala m’boma limene lingathetsedi mavuto aakulu amene tikuyang’anizana nawo lerolino. [Tchulani mavuto akumaloko monga ulova, kuwonjezereka kwa upandu, kapena anamgoneka.] Zinthu zimenezi zimatichititsa kuona kuti ifeyo ndi okondedwa athu tilibe mtsogolo mwabwino. Kodi muganiza kuti padzakhala boma limene lidzathetsa mavuto ameneŵa? [Yembekezerani yankho.] Mwinamwake mwapempherapo Pemphero la Ambuye. Ngati zili choncho, kodi mukudziŵa kuti kwenikweni mukupempherera boma lolungama?” Tsegulani patsamba 3 m’brosha la Boma, ndipo ŵerengani ndime ziŵiri zoyamba. Gaŵirani broshalo.
7 Ngati munagaŵira brosha la “Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso,” paulendo wobwereza mungayambe makambitsiranowo mwa kunena kuti:
◼ “Kumbuyoko tinakambitsirana kufunika kwa boma lolungama limene lingathetse mavuto a anthu. Brosha limene ndinakusiyirani limasonya ku Ufumu wa Mulungu monga chiyembekezo chathu chokha. Anthu ena amadzifunsa zimene bomalo lidzachita kuti liwongolere mkhalidwe wathu. Baibulo limasonyeza kuti Kristu wapereka kale umboni wakuti adzapambana pamene atsogoleri aumunthu alephera.” Tsegulani brosha la Boma patsamba 29, ndipo ŵerengani ndime zinayi zomalizira. Ndiyeno nenani kuti: “Kodi si mtsogolo mwabwino kwambiri mmenemo? Kodi mungafune kudzaonamo?” Yembekezerani yankho. Ŵerengani Yohane 17:3. Limbikitsani kuphunzira zowonjezereka kupyolera mwa phunziro la Baibulo lapanyumba.
8 Ngati mugwiritsira ntchito mabrosha ena, mungakonze maulaliki anu, mukumagwiritsira ntchito awo amene aperekedwa pamwambapo monga zitsanzo. Konzekerani bwino ndi kufunafuna dalitso la Yehova pamene mulengeza uthenga wabwino wa Ufumu.