Kabuku Katsopano Kamene Tidzagawira
1. Kodi tidzagawira chiyani m’mwezi wa November, nanga cholinga cha kabuku kameneka ndi chiyani?
1 M’chaka cha 2009 pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Khalani Maso,” panatulutsidwa kabuku katsopano ka mutu wakuti, Kodi Baibulo Lili ndi Uthenga Wotani? M’mwezi wa November, mipingo padziko lonse lapansi idzagawira kabuku kameneka kwanthawi yoyamba. Kodi kabuku kameneka kadzathandiza motani anthu m’gawo lathu? Anthu ambiri, makamaka amene ali m’zipembedzo zomwe si zachikhristu, amadziwa zochepa kwambiri zokhudza Baibulo. Choncho, patsamba 3 la kabukuka, amafotokoza kuti kabukuka kakonzedwa n’cholinga chakuti kakuthandizeni “kudziwa mwachidule zimene zili m’Baibulo.”
2. Kodi tingagawire motani kabukuka?
2 Mmene Tingagawire Kabukuka: Pogawira tikhoza kunena kuti: “Tikufuna kumva maganizo anu pa zimene lemba ili limanena. [Werengani 2 Timoteyo 3:16.] Anthu ambiri amavomereza zimene lembali likunena, koma ena amangoona kuti Baibulo langokhala buku labwino chabe. Kodi inuyo Baibulo mumaliona bwanji? [Yembekezani kuti ayankhe.] Tonse, mosaganizira za chikhulupiriro chathu, tili ndi zifukwa zokwanira zofufuzira Baibulo patokha. [Werengani mawu oyambirira amene ali pamwamba patsamba 3.] Pamene mukuwerenga nkhani zosangalatsa ndiponso zachidule za m’Baibulo zomwe zili m’kabuku kano, muona kuti Baibulo lili ndi mfundo yaikulu imodzi.”
3. Kodi tingagawire bwanji kabukuka ngati tikulalikira m’gawo limene anthu ambiri sali m’chipembedzo chachikhristu?
3 Ngati mukulalikira kwa munthu amene si wachipembedzo chachikhristu, mungagwiritse ntchito njira iyi pogawira kabukuka: “Tikufuna timve maganizo anu pa mawu awa ochokera m’buku lopatulika. [Werengani Salimo 37:11.] Kodi mukuganiza kuti ulosi umenewu ukadzakwaniritsidwa, dzikoli lidzakhala bwanji? [Yembekezani kuti ayankhe.] Limeneli ndi limodzi mwa malonjezo olimbikitsa amene Baibulo limapereka kwa anthu amitundu yonse ndiponso azikhulupiriro zosiyanasiyana.” Werengani mawu oyambirira omwe ali pamwamba patsamba 3, kenako apatseni kabukuko.
4. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji kabukuka poyambitsa phunziro la Baibulo?
4 Yambitsani Phunziro la Baibulo: Tikabwerera kwa amene tinakambirana nawo, tingawakumbutse zimene tinakambirana pa ulendo woyamba. Tikatero tikhoza kukambirana nawo ndime imodzi kapena ziwiri zokhudza nkhani imene tinakambirana ulendo woyambawo ndipo tingagwiritse ntchito mafunso amene ali kumapeto kwa gawo limene tinakambirana. Kapena ngati tikufuna kumusonyezeratu buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani, tingawerenge naye limodzi mawu amene ali kuchikuto chakumapeto cha kabukuka. Kenako tingamupatse bukulo, n’kumufunsa kuti asankhe mutu umene wamuchititsa chidwi, ndipo tingakambirane naye ndime imodzi kapena ziwiri pa mutu umene wasankhawo. Tonse tidzayesetse kugwira nawo ntchito yogawira kabukuka m’mwezi wa November.